Mmene Mungagwiritsire Ntchito Kabuku Kakuti, Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
Kabuku Katsopano Kothandiza Ophunzira Baibulo Kuti Abwere M’gulu
1. Kodi cholinga cha kabuku kakuti Chifuniro cha Yehova n’chiyani?
1 Kodi mwayamba kale kugwiritsa ntchito kabuku katsopano kakuti, Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano? Cholinga cha kabukuka ndi (1) kuthandiza ophunzira Baibulo kuti atidziwe bwino, (2) kuwathandiza kuti adziwe ntchito yathu, ndipo (3) kuwathandiza kuti adziwe zimene gulu lathu likuchita. Kabuku katsopanoka kali ndi timitu ta tsamba limodzi lokha ndipo mukhoza kukambirana mphindi 5 kapena 10 mukamaliza phunziro tsiku lililonse.
2. Kodi m’kabukuka muli zinthu ziti?
2 Zimene Zili M’kabukuka: Kabukuka kali ndi zigawo zitatu. Chigawo chilichonse chikufotokoza zinthu zosiyanasiyana zokhudza gulu la Yehova. Kali ndi mitu 28 ndipo mutu uliwonse ndi funso. Timitu ting’onoting’ono takuda timene tili m’munsi mwake tikuyankha funsolo. M’kabukuka mulinso zithunzi zochokera m’mayiko oposa 50 pofuna kusonyeza kuti ntchito yathu ikuchitika padziko lonse. Mitu yambiri ili ndi kabokosi kakuti “Dziwani Zambiri.” M’kabokosi kameneka muli zinthu zimene mungauze wophunzira wanu kuti achite.
3. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji kabuku kakuti Chifuniro cha Yehova?
3 Kodi Mungakagwiritse Ntchito Bwanji?: Choyamba muzifunsa funso lomwenso ndi mutu wa nkhani. Kenako mungawerenge nkhaniyo koma muzitsindika kwambiri timitu ting’onoting’ono timene talembedwa ndi inki yakuda kwambiri. Pomaliza muzikambirana mafunso amene ali pansi pa tsambalo. Mukhoza kuwerenga nkhani yonse kenako n’kukambirana. Apo ayi mukhoza kumakambirana pambuyo powerenga ndime iliyonse. Mungasankhe nokha malemba amene mukuona kuti ndi oyenera kuwawerenga. Musaiwalenso kukambirana zithunzi komanso kabokosi kakuti, “Dziwani Zambiri.” Mungachite bwino kuphunzira kabukuka motsatira ndondomeko ya mitu yake. Koma ngati mukuona kuti mutu wina wakutsogolo uli ndi mfundo imene ikufunika pa nthawiyo, mukhoza kuphunzira mutu umenewo. Mwachitsanzo, ngati msonkhano waukulu wayandikira mungapite pa mutu 11.
4. N’chifukwa chiyani mukusangalala kwambiri ndi kabuku katsopanoka?
4 Tikamaphunzira Baibulo ndi munthu, timamuthandiza kuti adziwe bwino Atate wathu wakumwamba. Koma tiyenera kumuthandizanso kudziwa bwino gulu la Yehova. (Miy. 6:20) Ndife osangalala kwambiri kuti kabukuka kadzatithandiza kuchita zimenezi m’njira yosavuta.