Bokosi la Mafunso
◼ Kodi tizivala ndi kudzikongoletsa motani pokacheza ku nyumba za Beteli ndiponso ku maofesi anthambi?
Popita ku Beteli, kaya kukaona malo kapena kukaona a m’banja la Beteli, “mavalidwe athu, mmene tadzikongoletsera komanso khalidwe lathu, ziyenera kufanana ndi mmene tiyenera kuchitira pamene tili pamisonkhano yolambira pa Nyumba ya Ufumu.” (om-CN 131) Koma, kwapezeka kuti abale ndi alongo ena popita ku maofesi a nthambi amavala motayirira kwambiri. Zimenezi si zoyenera popita ku maloŵa. Zovala zathu zizikhala zopereka chitsanzo chabwino, zovalidwa bwino ndiponso zopatsa ulemu, zosonyeza khalidwe labwino ndiponso ulemu woyenera atumiki a Yehova Mulungu.—1 Tim. 2:9, 10.
Izi n’zofunika kwambiri popita ku nyumba za Beteli ndi ku maofesi a nthambi chifukwa chakuti alendoŵa amaonedwa ndi anthu ambiri amene si Mboni. Zimene anthu ameneŵa amanena zokhudza anthu a Mulungu ndi gulu lake zimadalira pa zimene aona. Ndi bwinonso kuuza ophunzira Baibulo ndiponso anthu ena amene akukacheza ku maloŵa kuti n’kofunika kuvala ndi kudzikongoletsa bwino. Banja la Beteli lidzayamikira kwambiri mukachita zimenezi.
Monga atumiki achikristu, tiyenera kusamala kuti zovala zathu sizikupereka chokhumudwitsa chilichonse. (2 Akor. 6:3, 4) Koma, ‘tikometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu, Mulungu, m’zinthu zonse’ mwa kuvala bwino nthaŵi zonse.—Tito 2:10.