Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/98 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 6/98 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu June: Lililonse la mabuku otsatirawa a masamba 192 limene mpingo ungakhale nalo m’sitoko: Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere,” Happiness—How to Find It, Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo, Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Latsopano, “Let Your Kingdom Come,” Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?, Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona, ndi Your Youth—Getting the Best Out Of It. July ndi August: Mungagwiritsire ntchito lililonse la mabrosha otsatirawa a masamba 32: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Mabrosha akuti Buku la Anthu Onse, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Our Prolems—Who Will Help Us Solve Them?, ndi Will There Ever Be a World Without War? mungawagaŵire pamene kuli koyenera. September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Linanso limene tingagaŵire lingakhale buku la Creation kapena la Kukhala ndi Moyo Kosatha.

◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina amene iye wamsankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa June 1 kapena padeti lina koma lapafupi. Mutatha zimenezo lengezani kumpingo.

◼ Kuyambira mlungu wa September 21, 1998, mabrosha adzakhala akuphunziridwa pa Phunziro la Buku la Mpingo, kuyamba ndi lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?

◼ Tili okondwa kulengeza kuti ku Mzuzu tsopano kuli nyumba ya amishonale ndiponso malo ofikira mabuku. Zimenezo zikutanthauza kuti abale okhala m’mzinda wa Mzuzu ndi chapafupi azitha kupeza zofalitsa kumeneko. Chipinda cha mabuku kunyumba ya amishonale kumeneko chidzayamba kugwira ntchito pa June 1, 1998, ndipo chizitsegudwa Lolemba ndi Lachisanu lililonse. Nthaŵi yotsegulira idzakhala kuyambira 8:00 a.m. mpaka 12:00 masana. Chili mumsewu wa Kaning’ina Drive, Plot MZ 750.

◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:

Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?—Chicheŵa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena