Zinthu Zomwe Mufunikira Kusamala Kwambiri Pamene Mukukonzekera Zopita Kuchipatala
● Popeza kuti palibe munthu amene angadziŵe nthaŵi imene angamtengere kuchipatala kuti apulumutse moyo wake, kapena pamene angakhale m’chipatala chifukwa cha matenda ooneka ngati “aang’ono” komano amene pambuyo pake akuloŵetsapo nkhani yoika magazi, kungakhale kwanzeru kuchita zotsatirazi:
● Nthaŵi zonse muziyenda ndi khadi la Advance Medical Directive (Chidziŵitso kwa Dokotala) losainidwa, lolembapo wokuchitirani umboni, ndiponso la chaka chimenecho. Kuli bwino kwambiri KUSALITCHA kuti “KHADI LA MWAZI”; chifukwa chakuti ena angalimve molakwa dzina limenelo.
● Dziŵitsani akulu akwanuko nthaŵi iliyonse yomwe mupita kuchipatala kukalandira chithandizo.
● Uzani dokotala, wochita opaleshoni, ndiponso wopereka mankhwala ochititsa dzanzi kuti akutsimikizireni kuti akufunitsitsa kukuthandizani popanda kugwiritsira ntchito magazi. (Musalingalire kuti mungapeŵe makambitsirano ameneŵa ngati simukufuna magazi).
● Pamene akugonekani m’chipatala, nthaŵi yomweyo ndipo mosazengereza dzidziŵikitseni monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Ngati nkotheka, pemphani mkulu kuti atsagane nanu kuti akakuthandizeni kulemba zikalata zofunika zofotokoza cholinga chanu chakuti akuthandizeni popanda kugwiritsira ntchito magazi. (Nthaŵi zambiri zipatala zimakhala ndi mafomu a ‘release from liability’ (kusaimbidwa mlandu chifukwa cha zobukapo za chosankha cha wodwala), ndi zina zotero. Ngati chipatalacho chilibe mafomu ameneŵa ndipo inuyo mwadwala kwambiri koma akuchedwa kukupatsani chithandizo kapena akukana kukuthandizani, mkulu yemwe anatsagana nanu uja, ngati mutamuuza, angaimbire telefoni a m’Komiti Yolankhulana ndi Chipatala ndi kuwauza kuti abweretse fomuyo kapena kuitumiza pa fax kuchipatalako.)
● Musanasaine mafomu alionse a kuchipatala, CHOYAMBA muyenera kuwaŵerenga mosamala kuopera kuti mwina mosazindikira konse mungalole achipatala kugwiritsira ntchito magazi pa vuto limene muli nalo kapena lomwe akuganiza kuti muli nalo. Mafomu awo angakhale ndi mawu onena kuti zonse zomwe mwanena pankhani yokana magazi nzopanda ntchito. Muli ololedwa mwalamulo kupha mawu onse oterowo ndi kulembamo zimene mukufuna kuti fomuyo inene, ndipo kenaka muyenera kulemba zilembo zoyamba za maina anu pa zosintha zonse. Khalani ndi kope la fomu yosinthidwayo kuti idzakhale monga lifalensi yanu pamene vutolo lidzabukanso mtsogolo. Ngati wina akuyesa kukuletsani kuti musasinthe fomuyo, pemphani kuti mulankhule ndi mkulu wa pachipatalapo kapena womthandizira wake. Musachedwe kulemba mafomu ameneŵa mosamala. (Ngati mufuna kudziŵa zambiri ponena za mmene mungasamalire ana, onani nkhani yokonzedwanso ya m’mphatika ya mu Utumiki Wathu Waufumu wa January 1995.)
● Monga momwe tafotokozera pamwambapo, kulankhula ndi akulu akwanu ponena za chithandizo chilichonse cha mankhwala chomwe mungafune nkothandiza kwambiri. Ngati pambuyo pa kupenda bwino iwo aona kuti nkoyenera kutero, ndipo ngati muwalola, iwo adzaimbira telefoni Komiti Yolankhulana ndi Chipatala kuti ithandizepo, mwinamwake mwa kukuuzani za dokotala amene angakuthandizeni. Akulu a kwanuko amadziŵa kuti ndi ntchito yawo kukuthandizani m’njira zimenezi, kotero kuti sangakusiyeni nokhanokha kuti muchite zonsezi. Iwo amachita zimenezi pamene muwapempha kuti akuthandizeni mwachikondi ndi kukulimbikitsani kuti muchirimike.—Mlal. 4:9, 10, 12.