Kodi Mungayesetsebe Kutetezera Mphatso ya Moyo?
1 Yehova wadalitsa kwambiri zoyesayesa za anthu ake zofuna kukulitsa mgwirizano wawo ndi achipatala ndiponso azamalamulo. Chotsatirapo chake, tsopano nkwapafupi kupeza chithandizo chamankhwala cholemekezeka ndiponso chokwanira. Zimenezi zachepetseratu nkhaŵa zimene tinali kukhala nazo pazoyesayesa zathu za kusunga chikhulupiriro chathu chachikristu ndi ‘kusala mwazi.’ Zimenezi nthaŵi zambiri zatheka chifukwa cha khama la akulu athu a mumpingo ndi akulu a m’Makomiti Olankhulana ndi Chipatala (HLCs). Iwo alidi kwa ife “monga pobisalira mphepo, ndi . . . monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.”—Mac. 15:28, 29; Yes. 32:1, 2.
2 Tsopano tili ndi Makomiti Olankhulana ndi Chipatala okwana aŵiri muno m’Malaŵi, ndipo akulu oposa 10 akutumikira m’makomiti ameneŵa. Makomiti Olankhulana ndi Chipatala oposa 1,300 akugwira ntchito padziko lonse lapansi, ndipo programuyi tsopano ikuchitika m’maofesi ambiri anthambi a Sosaite. Zimenezi zikutanthauza kuti abale athu m’maiko onse 232 akupindula ndi makonzedwe ameneŵa. Pakali pano tikulemba ndandanda ya madokotala omwe akugwirizana ndi makonzedwewa. Chiŵerengero chochokera kunthambi zonse chikusonyeza kuti pali madokotala oposa 74,000 omwe akugwira nafe ntchitoyi kuzungulira dziko lonse lapansi. Kupita patsogolo kumeneku kwachitika kwenikweni chifukwa cha kulankhulana kwabwino kwa pakati pa Makomiti athu Olankhulana ndi Chipatala ndi magulu a madokotala a m’zipatala zotchuka kuzungulira dziko lonse lapansi. M’madera ena a dziko lapansi kuli zipatala zoposa 100 zomwe zikupereka chithandizo cha mankhwala ndi kuchita opaleshoni popanda kugwiritsira ntchito magazi.
3 Zikuonetsa kuti nkoyenerera, pomwe tikukuuzani nkhani yabwinoyi, kuti tikukumbutseni za (1) zinthu zofunika zomwe muyenera kuchita pamene mukukonzekera zopita kuchipatala kukalandira chithandizo cha mankhwala, ndiponso (2) mmene mungagwirizanire ndi Makomiti Olankhulana ndi Chipatala ndiponso akulu a kwanuko pamene mupempha chithandizo chawo. Ndithudi, pali zinthu zina zomwe kungakhale kwanzeru kuzichitiratu vuto lililonse ngati limeneli lisanabuke.
Kutetezera Thanzi Lanu Ndiko Kulemekeza Mphatso ya Moyo
4 M’masiku ano otsiriza matenda akufalikira kwambiri. (Luka 21:11) Chotsatirapo chake, zimenezi nthaŵi zambiri zimavutitsa moyo wa abale ndi alongo athu ambiri, makamaka ana. Popeza kuti kuno ku Malaŵi nthaŵi zina kwakhala kukubuka matenda ena, monga mliri wa matenda a cholera wa posachedwapa, nkwanzeru kugwiritsira ntchito uphungu woperekedwa m’nkhani za m’magazini aposachedwapa a Galamukani! monga nkhani yakuti “Kuteteza Thanzi la Ana” ndi “Njira Zisanu ndi Imodzi Zotetezera Thanzi Lanu,” m’magazini ya Galamukani! ya October 8, ndi December 8, 1997. Kungakhale kwanzeru kuti banja lililonse likambitsirane mmene lingagwiritsirire ntchito uphungu umenewu panyumbapo ndi kuona ngati pali mbali zina zofunika kuwongolera. Ngati tichita zimenezi tidzathandizira kutetezera thanzi lathu, makamakanso la ana athu. Lipoti laposachedwapa la bungwe la United Nations Children’s Fund (UNICEF), la mutu wakuti The Progress of Nations (Chitukuko cha Maiko), likusonyeza kuti chaka chilichonse, ana mamiliyoni ambiri angathe kupulumutsidwa kuimfa pogwiritsira ntchito njira zosavuta ndiponso zotsika mtengo. Ngakhale kuti si matenda onse omwe angapeŵedwe, ena angathe kupeŵedwa, ndipo kungakhale koyenerera kwa Akristu kulemekeza mphatso yamtengo wapatali ya moyo mwa kuchita chilichonse chothekera pofuna kutetezera thanzi lawo ndiponso la ana awo.
5 Ukhondo si chizoloŵezi chabwino chabe koma madokotala amauyamikiranso kwambiri. Ngati pali matenda ofunikira chithandizo chamankhwala, madokotala ndi manesi amagwira ntchito mofunitsitsa pothandiza anthu amene akusonyeza kuti akuyesetsa kukhala aukhondo ndi athanzi. Zimenezi zimakhala zothandizadi kwambiri ngati pabuka nkhani yokhudza kuika magazi. Ndiponso, pamene tikhala aukhondo timakhala tikupereka umboni wabwino. Mwachitsanzo, m’dera lina la kumpoto kwa Mozambique wazachipatala wina anafotokoza mmene Mboni za Yehova za kumeneko zilili zaukhondo mosiyana ndi anthu ena onse m’deralo. Zimenezi zinatsimikizika makamaka pamene kunabuka mliri wa cholera m’deralo ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe wa Mbonizo amene anadwala matendawo. Wazachipatalayo ananena kuti zinali choncho chifukwa chakuti “Mboni ndizo anthu aukhondo kwambiri kuposa ena onse.” Ndemanga zonga zimenezi zimapereka chitamando kwa Yehova.—Deut. 23:14; 1 Pet. 1:16; 2 Akor. 3:18.
6 Mfundo ina yofunika njakuti m’dziko muno, imodzi mwa nthenda zoopsa kwambiri ndiyo kusoŵa magazi. Ngati pali vuto limeneli kungakhale bwino kutsatira malangizo a m’nkhani yakuti “Kuteteza Thanzi la Ana” ya mu Galamukani! yomwe inafotokoza za kufunika kwa kudya zakudya zopatsa thanzi monga “mapapaya, mango, karoti, zamasamba, ndi mazira.” Zakudya zimenezi zili ndi iron wambiri ndipo zingathandizire kuthetsa vuto la kusoŵa magazi. Madokotala amanenanso kuti zakudya monga “mtedza, chiŵindi, malalanje ndi beetroot” zili ndi iron wambiri. Maproteni, amene amathandiza kwambiri kumanga thupi ndi magazi, amapezeka m’zakudya monga zakudya zamkaka, nsomba, nyama, nyemba, mapeyala, chigwada ndiponso mazira. Inde, dzira limodzi patsiku lingapatse mwana maproteni okwanira. Dzira limodzi patapita masiku aŵiri kapena atatu alionse lingapatse munthu wamkulu maproteni okwanira, popeza kuti munthu wamkulu amakhala woti anasiya kukula. Dokotala wina ananenanso kuti kwenikweni nyemba zili ndi maproteni ambiri ndi mavitameni ndipo kuli bwino kuzidya kwambiri. Ngakhale kuti nzodziŵika kuti si zakudya zonse zomwe zimapezeka mosavuta, nzodabwitsa kuti anthufe timakonda kudya chinangwa, nsima kapena mkate pamene zipatso ndi zakudya zina zaziŵisi zilipo zoti zingatipatse mavitameni olimbitsa magazi. Tisamaganize kuti zipatso ndi zakudya zina zaziŵisi nzakudya za ana okha ayi. Zakudya zimenezi zingathandizire kwambiri pathanzi la tonsefe kaya ndife ana kapena akuluakulu. Ngati tiyesetsa kudya chakudya chopatsa thanzi, mosakayika konse tidzamanga magazi athu ndiponso thanzi lathu lonse ndipo tikatero tidzatha kuchira mosavuta pamene tidwala kapena kuyang’anizana ndi vuto lina lotaya magazi.
7 Zimenezi zikutifikitsa pamfundo ina imene madokotala ena akudandaula nayo. Zikuonetsa kuti ena amatenga nthaŵi yaitali asanapite kuchipatala pamene munthu wina wadwala kwambiri. Zimenezi zimapangitsa kuti wodwalayo afooke kwambiri kotero kuti nthaŵi zina kumapezeka kuti achedwa kupulumutsa wodwalayo chifukwa chofika naye kuchipatala mochedwa. Mwinanso angakhale kuti ngwodwala kwambiri kotero kuti amatenga nthaŵi yaitali kuti achire ndipo amafunikanso chisamaliro chamankhwala chapafupipafupi. Monga Mboni za Yehova tiyenera kupeŵa chithandizo chamankhwala monga opaleshoni yaikulu, chimene chingaloŵetsepo nkhani yoika magazi yomwe tingathe kuipeŵa mwa kupita kuchipatala mwamsanga. Zimenezi zikugogomezera kuti nkofunika kusachedwa kupita kuchipatala ndi munthu amene wadwala kwambiri. Ndipo zimenezi zimakhala zofunikanso kwambiri ngati akudwalawo ndi ana kapena amayi apakati, popeza kuti iwo angadwale mosavuta matenda a kusoŵa magazi. Tiyeneranso kusamala kwambiri pamene mwana wadwala malungo popeza kuti matendawa amawononga maselo ofiira a magazi a m’thupi mwake ndipo chotsatirapo chake mwanayo amatha magazi. Vuto limeneli lingakule mwamsanga popeza kuti mwana amakhala ali ndi magazi ochepa kale m’thupi mwake. Madokotala a kuchipatala cha Lilongwe Central Hospital anauza Komiti Yolankhulana ndi Chipatala ya m’derali kuti pafupifupi tsiku lililonse pachipatalapo pamafika mwana wodwala malungo amene amamwalira chifukwa chochedwa kufika naye kuchipatala. Tiyenera kuyesetsa kuti vuto limeneli lisachitike m’banja mwathu. Ndithudi, kungakhalenso bwino kwambiri ngati tingapeŵeretu malungo. Tingachite zimenezi mwa kugona m’masikito. Ngati sitingathe kugulira banja lonse masikito, mwina tingagulire ana okha. Njira zosavuta zimenezi zingathandizire kupulumutsa moyo.—Kuti mudziŵe zambiri onani g93 5/8 tsamba 15.
8 Ndithudi, tiyenera kukumbukira kuti pomwe tikhalabe m’dongosolo loipa lino lazinthu, timadziŵa kuti sitingathe kuthetsa matenda kapena vuto la kusoŵa magazi pazochitika zina. Koma mwa kuyesetsa kudya zakudya zopatsa thanzi, nthaŵi zonse kumwa madzi osamalidwa bwino, kusunga ukhondo ndiponso kupeŵa kuchedwetsa kupita kuchipatala tingathe kudzitetezera kwambiri. Ndipo tikatero tidzasonyeza kuti timayamikira mphatso ya moyo yomwe Yehova watipatsa.—Sal. 36:9.
[Bokosi patsamba 3]
Ofalitsa onse asunge mphatika ino monga chitsogozo cha mabanja awo!
[Bokosi patsamba 4]
“Njira Zisanu ndi Imodzi Zotetezera Thanzi Lanu”
1. Sambani m’manja ndi sopo mutakhudza tubzi ndiponso musanagwire chakudya.
2. Gwiritsirani ntchito chimbudzi.
3. Gwiritsirani ntchito madzi abwino.
4. Ŵiritsani madzi akumwa kusiyapo ngati achoka mumpopi wabwino.
5. Sungani chakudya chanu mwaukhondo.
6. Tenthani kapena kwirirani zinyalala zonse zapanyumba.
—Zotengedwa mu Galamukani! ya December 8, 1997
[Bokosi patsamba 5]
Gwiritsirani Ntchito Bwino Mtengo wa Papaya
Nkhani ina ya mu Galamukani! yachingelezi ya August 8, 1978, inafotokoza mmene mtengo wa papaya ulili ndi mavitameni ambiri. Inafotokoza kuti kutafuna ndi kumeza tsamba lake kapena njere zake zodzala sipuni imodzi yaikulu panthaŵi iliyonse ya chakudya kungatetezere mphamvu ya thupi lanu yolimbana ndi tizilombo kapena nyongolotsi zoyambitsa matenda. Ndipo zimenezi zimachepetsa matenda a kutsegula m’mimba.