Mbiri Yateokrase
◼ Muno m’Malaŵi, ntchito yomanga pamalo a Sosaite ku Lilongwe inayamba Loŵeruka, pa March 21, pamene mpanda unayamba kumangidwa. Ntchito yomanga Beteliyo akuyembekezera kudzaitsiriza m’chaka cha 2000.
◼ Nthambi zingapo za m’zisumbu padziko lonse zinapereka lipoti la ziŵerengero zatsopano zapamwamba za ofalitsa mu January. Nthambi zinazo zinali Dominican Republic, Haiti, Martinique, Mauritius, Philippines, Taiwan, ndi Trinidad.
◼ Chiwonjezeko cha ku Seychelles chinali 18 peresenti kuposa avareji ya chaka chatha, ndipo cha ku St. Maarten chinali 16 peresenti.
◼ Ku Hong Kong ofalitsa anachita avareji ya maola 12.7.
◼ Nyumba ya Ufumu yoyamba yomangidwa masiku oŵerengeka ku Taiwan inamalizidwa mu February.