Kodi Chuma Chakuthupi Chingatsimikiziritse Kupeza Chimwemwe?
“MWA ophunzira pafupifupi 50 pasukulu pathu, ndi 1 kapena 2 okha amene ankavala nsapato,” akukumbukira motero Poching wazaka 45, amene anakulira kummwera kwa Taiwan mkati mwa ma 1950. “Sitikanatha kuzigula. Komabe, sitinadzione kukhala osauka. Tinali ndi zonse zimene tinafunikira.”
Zimenezi zinali zaka pafupifupi 40 zapitazo. Chiyambire pamenepo, moyo wasintha kwambiri kwa Poching ndi nzika zina zonse 20 miliyoni za chisumbu chimenecho. Monga momwe buku lakuti Facts and Figures—The Republic of China on Taiwan limafotokozera kuti, “Taiwan anasinth[idw]a kuchoka pa kukhala wa chitaganya chaulimi kukhala wa chitaganya chopita patsogolo cha maindasitale.” Podzafika kumapeto kwa ma 1970, Taiwan anaonedwa monga “chitaganya chokhazikika, ndi cholemera.”
Ndithudi, umboni wa kulemera umaoneka paliponse mu Taiwan. Kuyambira pa maofesi anyumba zazitali zamakono zimene zamangidwa mofulumira pachisumbu ponsepo kufikira pamisewu yaikulu yodzala ndi galimoto zokwera mtengo zogulidwa kumaiko akunja, kulemera kwa Taiwan kumasiriridwa ndi maiko ena osatukuka. China Post, nyuzipepala yotchuka ya Chingelezi ya ku Taiwan, ikunena monyadira kuti lerolino “anthu a Taiwan ali ndi muyezo wapamwamba koposa wa moyo m’mbiri ya China.”
‘Mavuto Aakulu Ochuluka’
Kodi chuma chakuthupi chonsechi chabweretsera anthu chimwemwe ndi chikhutiro choona? Ngakhale kuti kuli kosakayikitsa kuti pali zambiri zimene anthu a ku Taiwan amazinyadira, palinso mbali ina ya nkhani imeneyi ya chipambano. China Post ikupitiriza kusonyeza kuti: “Limodzi ndi kulemera kwakukulu kumeneku, pakhalanso mavuto ocholoŵana aakulu ochuluka.” Chuma cha Taiwan sichinangokhalapo popanda kulipirira mtengo wake.
Ponena za “mavuto ocholoŵana aakulu” amene akuvutitsa chisumbu chimenechi chimene kale chinalibe upandu, China Post ikunena kuti: “M’zaka zaposachedwapa upandu ndi kusalamulirika kwa zinthu zawonjezeka mochititsa mantha m’chitaganya chathu cha olemera, zikumawopseza mowonjezereka miyoyo ndi katundu wa nzika zonse zomvera lamulo.” M’nkhani yakuti “Chuma Chipangitsa Taiwan Kukhala Dziko la Chilakolako Chonyansa,” Post ikutsutsa mwamphamvu za kuwonjezera “malesitilanti a atsikana ovala mosakwanira ndi nyumba za moŵa” ndi nyumba zamahule zonamizira kukhala mashopo ometera tsitsi. Kulanda ndi kufwamba ndi cholinga cha kulandira dipo moumiriza kwakhala vuto linanso. Lipoti lina likunena za kufwambidwa kwa ana kukhala “bizinesi yatsopano ya Taiwan yomakula mofulumira.” Ambiri amatembenukira pa kuchita maupandu otero monga njira yolipirira ngongole za juga kapena ndalama zina zimene anataya.
Ana sali chabe anthu ochitiridwa upandu osalakwa. Iwo akudziloŵetsa kwambiri m’kuchita maupandu amenewo. Malipoti akusonyeza kuti mu 1989 mokha, maupandu ochitidwa ndi ana anawonjezereka mofulumira ndi 30 peresenti. Ena anapeza kuti kuwonjezereka kumeneku kumachititsidwa ndi kusamvana kwa m’banja, ndipo maumboni akuonekera kukhala ochirikiza zimenezi. Mwachitsanzo, kuyambira 1977 kufikira 1987, chiŵerengero cha Ataiwani amene anakwatirana chinatsika, komano chiŵerengero cha zisudzulo chinaŵirikiza kaŵiri ndi kuposerapo. Popeza kuti mwamwambo Atchaina amagogomezera kufunika kwa banja m’chitaganya chokhazikika, mposadabwitsa kuti ambiri akudera nkhaŵa kwambiri ndi mikhalidwe yomaipiraipira.
Muzu wa Vutolo
Malongosoledwe osiyanasiyana aperekedwa poyesa kudziŵa chifukwa chochititsa kunyonyotsoka kwa dongosolo labwino la anthu a m’chitaganya cholemera. Anthu ena, polingalira kuti ndi odziŵa zinthu, amanena kuti zimenezi zangokhala mtengo wake wachipambano. Koma kupatsa mlandu chipambano kapena chuma kuli ngati kuimba chakudya mlandu wa kususuka. Sikuti anthu onse amene amadya ali osusuka, ndiponso si wachuma aliyense amene ali wokondetsa chuma kapena amene ali waupandu. Ndithudi, chuma chakuthupi mwa icho chokha sichimachititsa upandu ndi chisokonezo m’chitaganya.
Nkhani ina ya mkonzi mu China Post inasonyeza chochititsa chachikulu. Iyo inati: “Kwa zaka makumi ambiri, tagogomezera kwambiri pa chitukuko cha chuma. Zimenezi ndizo zochititsa kunyonyotsoka kwa chikhalidwe chabwino ndi makhalidwe auzimu m’chitaganya chathu lerolino.” (Kanyenye ngwathu.) Inde, kugogomezera mopambanitsa kulondola zinthu zakuthupi kumatsogolera ku mzimu wa kukondetsa chuma ndi umbombo. Kumachirikiza mzimu wa kudzigangira. Uli mzimu umenewowo umene umachititsa kusamvana m’mabanja ndi kufalikira kwa mavuto a m’chitaganya. Zimene Baibulo linanena zaka 2,000 zapitazo zidakali zoona: “Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama [osati ndalama mwa izo zokha].”—1 Timoteo 6:10.
Vuto la Padziko Lonse
Pofunafuna mtendere ndi bata—ndi chitetezo—anthu zikwi zambiri a ku Taiwan asamukira kumaiko ena. Koma mavuto amene Taiwan akukumana nawo sali a Taiwan yekha. Iwo ngofala padziko lonse.
Zaka zingapo zapitazo kufufuza kwina kunasonyeza kuti dera lina la chuma koposa mu California, U.S.A., linali ndi mlingo wapamwamba koposa wa zisudzulo m’dzikolo. Pafupifupi 90 peresenti ya kugulitsidwa kwa chuma chonse m’mbali zina za deralo kunachitika chifukwa cha kusweka kwa maukwati. Kudzipha kowirikiza kaŵiri pa avareji ya mtunduwo kunachitiridwa lipoti. Mlingo wa uchidakwa unali umodzi wa milingo yapamwamba koposa m’dziko, ndipo m’deralo munanenedwa kuti muli madokotala anthenda zamaganizo ndi ochiritsa nthenda zamaganizo ambiri, pa munthu aliyense, kuposa kulikonse mu United States.
Yesu Kristu anasonyeza choonadi chofunika kwambiri pamene anati: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Chuma chakuthupi, mosasamala kanthu kuti nchochuluka motani, sichingakhutiritse chosoŵa cha munthu chilichonse, ndiponso sichingatsimikiziritse chimwemwe. Mosiyana ndi zimenezo, monga momwe mwambi wina Wachitchaina umanenera kuti: “Pamene munthu adya ndi kufunda bwino, malingaliro ake amatembenukira pa kumwerekera ndi zikhumbo za thupi.” Zimenezi zimasonyezedwa ndi zimene zikuchitika ku Taiwan ndi kwina kulikonse—chuma chakuthupi chokha kaŵirikaŵiri chimadzakhala chinthu chotsogolera kukunyonyotsoka kwa makhalidwe ndi chitaganya ndi mavuto ake.
Nangano, nchiyani chimene chikufunika kuti chuma chakuthupi chikhaledi mbali ya chimwemwe chenicheni ndi chosatha? Kuti mupeze yankho, chonde ŵerengani nkhani yotsatira.
[Mawu Otsindika patsamba 6]
“Pamene munthu adya ndi kufunda bwino, malingaliro ake amatembenukira pa kumwerekera ndi zikhumbo za thupi.”—Mwambi Wachitchaina
[Chithunzi patsamba 5]
Kulemera kwakuthupi kunasintha matauni aang’onoang’ono kukhala mizinda yapiringupiringu ndi yamagetsi