Kulondola Chuma Chakuthupi
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU TAIWAN
‘NDALAMA sizingagule chimwemwe!’ Ngakhale kuti anthu ochuluka mwinamwake amavomereza mawu amenewo, ambiri a iwo adakalondolabe mosalekeza chuma chakuthupi monga njira yopezera moyo wachimwemwe chokulirapo. Ndipo nkulekeranji kutero? Ndi iko komwe, kukuonekera kuti mankhwala othetsera mavuto ambiri a mtundu wa anthu ali m’kupeza chuma ndi kulemera.
Tangoganizani kuti likanakhala dziko lotani ngati mwamuna aliyense, mkazi, ndi mwana akanakhala wachuma! Sipakanakhalanso umphaŵi ndi kuvutika kwa mamiliyoni amene amakhala m’zithando za m’dzikoli. Sipakanakhalanso vuto la anthu osoŵa malo okhala limene likukantha dziko lililonse tsopano, lolemera ndi losauka.
Nangano bwanji ponena za thanzi labwino, lofunika kwambiri kaamba ka chimwemwe? Ngakhale kuti sayansi ya zamankhwala ikupita patsogolo mofulumira kwambiri, anthu owonjezereka akupeza kuti sangathe kulipirira mtengo wake. Komanso, njala ndi manyutilishoni zili zochitika zatsiku ndi tsiku kwa mamiliyoni. Ngati kulemera kukanakhala padziko lonse, aliyense akanakhala ndi mwaŵi wa kukhala ndi moyo wathanzipo, ndipo motero akumakhala ndi moyo wachimwemwepo—kodi sichoncho?
Ngakhale dziko lapansi lenilenilo likanakhala mu mkhalidwe wabwino. Motani? Malo a dziko lapansi tsopano akuwonongedwa ndi zinthu zoipitsa zakupha, mwapang’ono zochititsidwa ndi kutentha malasha ndi mafuta. Komabe, chifukwa china chotchulidwa cha kusagwiritsira ntchito njira za maluso ofunikira a mitundu yosaipitsa kwambiri ya mphamvu za magetsi, nchakuti njira za malusozo zimalira ndalama zambiri. Kufuna chuma kwanenedwa kukhala chochititsa china chachikulu cha kuwononga nkhalango za mvula, chiwopsezo china chachikulu cha kulinganizika kwa chilengedwe.
Popeza kuti chuma chakuthupi mwachionekere chikanathetsa ambiri a mavuto athu ndi kuthetsa kuvutika kochuluka, mposadabwitsa kuti kwanthaŵi yaitali anthu aona chuma kukhala chopatsa chimwemwe. Mwachitsanzo, pamene kuli kwakuti anthu a maiko a Kumadzulo mwachizoloŵezi amalonjerana mwa kunena kuti “Happy New Year!” pa tsiku la New Year, Atchaina, mkati mwa nyengo ya New Year, mwamwambo amanena kuti “Kung hsi fa tsai” kwa wina ndi mnzake, akumayembekezera kuti ‘adzapeza chuma!’ Inde, sitingakane kuti tikukhala m’dziko limene anthu amalondola chuma chakuthupi monga chinthu chofunika koposa. Kaŵirikaŵiri chipambano kapena kulephera zimapimidwa ndi chuma.
Pamene kuli kwakuti kupeza zinthu zakuthupi ndi kusangalala nazo sikuli kolakwa mwa iko kokha, kodi izo zingatsimikiziritse chimwemwe? Kodi ziyenera kuonedwa kukhala zofunika motani? Kodi chuma chakuthupi chilidi njira yopezera dziko labwinopo?