Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/98 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya June

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya June
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira June 1
  • Mlungu Woyambira June 8
  • Mlungu Woyambira June 15
  • Mlungu Woyambira June 22
  • Mlungu Woyambira June 29
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 6/98 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya June

Mlungu Woyambira June 1

Nyimbo Na. 223

Mph. 8: Zilengezo zapampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Mbiri Yateokrase.

Mph. 15: “Wokonzeka Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino.” Mafunso ndi mayankho.

Mph. 22: “Kuchitira Umboni kwa Anthu Onse.” Mkulu akufotokoza kuti ngakhale kuti mabuku ochita kusankhidwa a masamba 192 ndiwo chogaŵira cha June, ngati kuli koyenera kugaŵira anthu ena buku la Munthu Wamkulu tingatero. Mkuluyo ndi kagulu ka ofalitsa aluso akukambitsirana mmene angakaperekere maulaliki. Pendani mwachidule zipembedzo zimene mumakumana nazo kwanuko, ndi kufotokoza chifukwa chake tiyenera kukhala ndi chonena kuti tizitha kuyamba kukambitsirana panthaŵi iliyonse. Mungachite chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri zachidule.

Nyimbo Na. 112 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 8

Nyimbo Na. 209

Mph. 10: Zilengezo zapampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 15: 

Mph. 20: “Tonsefe Timafunikira Kugwirizana Kuti Ntchito Igwirike.” Nkhani ndi kukambitsirana ndi omvetsera. Fotokozani chifukwa chake akulu amadalira antchito ambiri odzifunira pakuchita zinthu. Pendani zosoŵa za kwanuko, zonga kuyeretsa Nyumba ya Ufumu ndi kuisamala, kuthandiza odwala ndi achikulire, ndi kufola gawo. Pemphani akulu akambepo mmene amayamikirira zimene ambiri amachita kuti athandize. Gogomezerani kuti kuyesayesa kwa aliyense nkofunika.

Nyimbo Na. 153 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 15

Nyimbo Na. 7

Mph. 9: Zilengezo zapampingo.

Mph. 18: “Apainiya Amapereka ndi Kulandira Madalitso.” Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1994, masamba 21-3. Kambitsiranani kuti upainiya wokhazikika ngwofunika, mukumalimbikitsa ena kuti alembetse pa September 1.

Mph. 18: “Kuchitira Umboni mwa Khalidwe Labwino.” Mafunso ndi mayankho. Funsani achinyamata ena osonyeza chitsanzo chabwino. Nanene mmene ena achitira chidwi ndi khalidwe lawo lachikristu. Simbaninso chokumana nacho chimodzi kapena ziŵiri za mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 1995, masamba 24-5.

Nyimbo Na. 170 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 22

Nyimbo Na. 61

Mph. 10: Zilengezo zapampingo. Tchulani kuti anatha liti kuŵerengera maakaunti a mpingo.

Mph. 15: Mmene Tingayambire Njira ya Magazini. Fotokozani zofunika zake: Lembani zonse zimene mwagaŵira, bwererakoni patapita milungu iŵiri, auzeni malingaliro atsopano a m’magazini atsopano kuti chidwi chawo chikhalepobe. Tchulaninso kuti mwina tingaphatikizepo achinansi, ogwira nawo ntchito, ogwira ntchito m’sitolo, ogwira ntchito pomwetsera petulo, ndi ena oterowo. Gaŵirani masabusikripishoni a miyezi isanu ndi umodzi kwa amene akusonyezabe chidwi. Pemphani ofalitsa aŵiri asimbe chokumana nacho chabwino chonena za njira zamagazini.

Mph. 20: Apainiya Athandiza Ena. Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki, kupenda njira zimene apainiya angathandizire ena payekhapayekha. Fotokozani mmene maprogramu a kuthandiza anayambira kale. (jv 100; km 9/79 1, 3) Anthu oposa miliyoni imodzi omwe anabatizidwa zaka zitatu zapitazo afunikira kuphunzitsidwa. Programu ya “Apainiya Athandiza Ena” imagwiritsira ntchito luso ndi maphunziro amene apainiya okhazikika ndi apadera anapeza ku Sukulu Yautumiki Waupainiya. Cholinga chake nchakuti mpainiya aliyense athandize ofalitsa aŵiri pachaka kuti apeze luso ndithu mu utumiki ndi kutinso akalamire kuchita zambiri. Anthu amene akuthandizidwawo sayenera kudera nkhaŵa; chofunika kwambiri panopa ndicho kulimbikitsa mwachikondi, ndi mokoma mtima. Programu yatsopano imeneyi ikhoza kuthandiza anthu zikwi mazana ambiri kukhala atumiki okhoza bwino kwambiri.

Nyimbo Na. 207 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 29

Nyimbo Na. 114

Mph. 7: Zilengezo. Kumbutsani onse kupereka malipoti a utumiki a June. Kambitsiranani mabuku ogaŵira mu July.

Mph. 23: “Kodi Mungayesetsebe Kutetezera Mphatso ya Moyo?” Ikambidwe ndi mkulu waluso ndi kukambitsirana ndi omvetsera. Pendani mwachidule ndime 1-3. Pandime 4-8 zamafunso ndi mayankho, ŵerengani ndime 4-7. Mveketsani kwa omvetsera chifukwa chake mfundo iliyonse m’bokosi la patsamba 6 ili yofunika.

Mph. 15: Tonsefe Tingachitire Umboni wa Mwamwayi. Nkhani yokambitsirana ndi omvetsera, yochokera m’buku la Uminisitala Wathu, masamba 93-94. Sonyezani mmene awo amene nthaŵi yawo imathera kuntchito yolembedwa, pabanja, kapena pantchito zina zaumwini, angapezere mipata youzira ena uthenga wabwino. Tchulanipo zokumana nazo za kwanu konko.

Nyimbo Na. 76 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena