Nkwabwinotu Kwambiri Kupezekapo Nthaŵi Zonse!
1 Kwa zaka makumi ambiri ku Eastern Europe, ambiri mwa abale athu okondedwa analetsedwa kusonkhana poyera. Tangoganizani mmene anakondwera pamene analoledwa kumasonkhana mwaufulu!
2 Woyang’anira dera wina, pofotokoza zimene zinachitika mumpingo umene anali kuchezetsa, analemba kuti: “Lachiŵiri madzulo, ndikungoyamba kumene kuchezetsa, ziŵiya zotenthetsera m’nyumba zinawonongeka. Panja, kuzizira kwake kunali koumika magazi, mkati, ndiye ngati munali ‘kutentha 5 digirii Celsius basi.’ Abale anangokhala atavala majasi awo, ma scarf, magolovesi, zipeŵa, ndi mabuti. Palibe aliyense amene anakwanitsa kumaŵerenga malemba, poti kunali kosatheka kutsegula Baibulo. Ndili chilili paplatifomu nditavala suti yanga, ndinangouma gwaa, ndipo paliponse ndikamapuma, nthunzi inali kutuluka. Koma chimene chinandisangalatsa chinali chakuti sindinamve ngakhale liwu limodzi lodandaula. Abale onse ananena kuti kunali kwabwino ndi kosangalatsa kwambiri kupezekapo!” Abalewo sanaganizire ngakhale pang’ono kuti aphonye msonkhano umenewo!
3 Kodi ndi Mmene Ifenso Timaonera? Kodi timayamikira mpata wakusonkhana mwaufulu pamisonkhano yathu ya mlungu ndi mlungu? Kapena kodi timanyalanyaza misonkhano pamene mikhalidwe ili bwino? Kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse sikungakhale kosavuta, ndipo nthaŵi zina tingakhale ndi chifukwa chomveka chosapezekerapo. Komabe, musamaiŵale kuti pali ena mwa ife, omwe akukalamba, omwe ali ndi mavuto aakulu athanzi, ngopunduka, ogwira ntchito yodya nthaŵi, ndi ntchito zina zovuta, komabe mosasamala zonsezo, amaona kuti misonkhano njofunika ndipo amapezekapo nthaŵi zonse. Amenewotu ndiwo zitsanzo zabwino kwambiri zoti tizitsanzira!—Yerekezerani ndi Luka 2:37.
4 Tiyeni tizoloŵere kuchirikiza kulambira koona mwa kupezeka pamisonkhano yonse yachikristu, kuyambira pakagulu ka phunziro la buku mpaka pamsonkhano waukulu. Kodi nchifukwa chiyani tiyenera kuiona misonkhano imeneyi monga yofunika chonchi? Chifukwa Mulungu analamula kuti tizisonkhana pamodzi. Koma palinso zifukwa zina zomveka. Tonsefe timafunikira mapindu a kulangizidwa ndi Mulungu ndiponso kuthandizidwa ndi mzimu woyera, zimenezo timazipeza pamisonkhano. (Mat. 18:20) Tikamasonkhana ndi abale athu timamangiriridwa mwa kulimbikitsana.—Aheb. 10:24, 25.
5 Pa masomphenya a kusandulika paja, Petro anati: “Ambuye, nkwabwino kuti tili pano.” (Luka 9:33) Nafenso tiyenera kumaiona choncho misonkhano yathu yachikristu yonse. Komadi, nkwabwinotu kwambiri kupezekapo nthaŵi zonse!