Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. October: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kumene tapeza anthu ochita chidwi, tingagaŵire masabusikripishoni paulendo wobwereza. November: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. December: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina amene iye wamsankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa September 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Lengezani kumpingo mutatha kuchita zimenezo.
◼ Akulu akukumbutsidwa kutsatira malangizo operekedwa pamasamba 21-3 a Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, onena za wochotsedwa aliyense kapena munthu wodzilekanitsa amene angakonde kubwezeretsedwa.
◼ Amene akugwirizana ndi mpingo ayenera kutumiza masabusikripishoni onse atsopano ndi olembetsanso a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, kuphatikizapo masabusikripishoni awo, kupyolera mumpingo.
◼ Sosaite siimadzazira munthu aliyense zofunsira mabuku za wofalitsa. Woyang’anira wotsogoza ayenera kuona kuti mwezi uliwonse pazikhala chilengezo asanatumize ku Sosaite chofunsira mabuku a mpingo cha mwezi ndi mwezi, kuti onse ofuna kupeza mabuku awoawo auziretu mbale wosunga mabuku. Chonde kumbukirani kuti ndi mabuku ati amene afunikira oda yapadera.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha—Chicheŵa, Chingelezi, Chitumbuka