Misonkhano Yautumiki ya November
Mlungu Woyambira November 2
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Kambanipo za lipoti lautumiki wakumunda la July la dziko lino ndi la mpingo wanu.
Mph. 15: “Onse Ayenera ‘Kulandira Mawu Mofunitsitsa’!” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo malingaliro ena kuchokera mu mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996, ndime 21.
Mph. 20: “Ndikufuna Phunziro la Baibulo!” Woyang’anira utumiki akambitsirane ndi omvetsera. Fotokozani mmene kuyesayesa kwa pamodzi kumeneku kopanga maulendo obwereza kudzalinganizidwira pampingo wanu. Ku mlingo wothekera, ofalitsa ozoloŵera angagwire ntchito ndi achatsopano. Magulu ayenera kukhala ang’onoang’ono kotero kuti anthu ambiri angafikiridwe. Pendani malingaliro amene ali mu mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa May 1998, ndime 12-15. Wofalitsa wodziŵa achite chitsanzo cha kupempha munthu kuyamba naye phunziro pa ulendo wobwereza. Limbikitsani aliyense kuti ayesetse kuyambitsa phunziro latsopano.
Nyimbo Na. 35 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 9
Mph. 13: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Bokosi la Mafunso.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 17: “Limbikitsanani mwa Kuyankha Pamisonkhano.” Mafunso ndi mayankho. Fotokozani mmene kuyankha kumatithandizira kupita patsogolo mwauzimu. (Onani Bukhu Lolangiza la Sukulu, phunziro 38, ndime 4.) Pemphani ena kuti asimbe mmene anathetsera kuzengereza pofuna kuyankha ndi mmene adalitsidwira mwa kuyankha nawo pamisonkhano.
Nyimbo Na. 51 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 16
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Longosolani makonzedwe apadera a utumiki wakumunda a mapeto a mlungu uno.
Mph. 20: “Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Woyang’anira Sukulu Yautumiki Wateokratiki.” Nkhani ya woyang’anira sukulu. Bwerezani ndime 6-12 pamasamba 10-11, mu Bukhu Lolangiza la Sukulu.
Mph. 17: “Khalani Wogwira Mtima mu Utumiki Wanu.” Kukambirana ndime 1-7 za mphatika mwa mafunso ndi mayankho. Kambiranani makamaka mfundo zimene kwenikweni zingagwire ntchito m’gawo la mpingo wanu.
Nyimbo Na. 167 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 23
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Simbani zokumana nazo zosindikizidwa patsamba lothera la Galamukani! wa August 8, 1998, zonena za mmene buku la Munthu Wamkulu lakhudzira anthu. Ofalitsa onse ayenera kukhala atcheru kugaŵira bukuli panthaŵi zoyenera.
Mph. 17: “Khalani Wogwira Mtima mu Utumiki Wanu.” Kukambirana ndime 8-14 za mphatika mwa mafunso ndi mayankho. Kambiranani makamaka mfundo zimene kwenikweni zingagwire ntchito m’gawo la mpingo wanu.
Mph. 20: Malingaliro a Kuwongolera Kuŵerenga Baibulo Kwanu. Nkhani yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya May 1, 1995, masamba 16-17. Tchulani mapindu auzimu amene amapezeka pa kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Bwerezani malingaliro operekedwawo, ndipo fotokozani mmene tingawagwiritsire ntchito. Ofalitsa aŵiri kapena atatu asimbe mmene akupindulira mwa kuŵerenga Mawu a Mulungu mokhazikika.
Nyimbo Na. 46 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 30
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti autumiki wakumunda. Limbikitsani aliyense amene sanayambitse phunziro mu November kuti apitirize zoyesayesa zawo mu December, pamene tikugaŵira buku la Chidziŵitso. Wofalitsa wokhoza achite chitsanzo cha ulendo wobwereza pogwiritsa ntchito bokosi lomwe lili patsamba 19 mu buku la Chidziŵitso; wofalitsayo alongosole mmene munthu angaliphunzirire bukulo kuti amvetsetse ziphunzitso za Baibulo, ndiyeno wofalitsayo ayambitse phunziro.
Mph. 15: Gwiritsani Ntchito Mwanzeru Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1999. Nkhani. Pendani mbali za kalendayo: (1) zithunzithunzi zochititsa chidwi zimene zimaimira zochitika ndi ziphunzitso zotchuka za m’Baibulo, (2) ndandanda ya kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki, (3) ndandanda ya pachaka ya kuŵerenga Baibulo ya mlungu wotsagana ndi Chikumbutso, (4) chidziŵitso cha kubwereza kolemba, ndi (5) zikumbutso pa kuchita nawo utumiki wa magazini mokhazikika. Fotokozani njira zogwiritsira ntchito malo amene alipo kulembapo ndandanda ya utumiki wakumunda, malipoti a utumiki ndi malonjezano ogwira ntchito ndi ena, kundandalikapo nkhani za misonkhano zimene mwapatsidwa, zikumbutso za kuchezetsa kwa woyang’anira dera ndi misonkhano ikuluikulu imene tidzakhala nayo. Kupachika kalenda pamalo oonekera m’nyumba kapena kuntchito, kungapereke mwayi woyambitsa makambitsirano a Malemba.
Mph. 15: “Mitu ya Mabanja—Kodi Mukusamalira Udindo Wanu Wachikristu?” Kukambitsirana kwa mafunso ndi mayankho kotsogozedwa ndi mkulu. Pakufunika kuphunzitsa ana mu utumuki kuyambira ali ang’ono. Athandizeni kuzindikira kufunika kofika pamisonkhano ya mpingo.
Nyimbo Na. 121 ndi pemphero lomaliza.