Atha Kuona Kuti Ndife Osiyana
1 Chaka chatha, anthu owonjezereka oposa 300,000 anagwirizana nafe mwa kubatizidwa. Kodi anthu amenewa aonanji mwa Mboni za Yehova chimene chawapangitsa kufuna kukhala m’gulu la Mulungu? Nchifukwa chiyani timakhala osiyana ndi zipembedzo zina zonse? Nawa mayankho ena odziŵika bwino:
—Timamamatira pa Baibulo osati pa malingaliro a munthu: Timalambira Yehova Mulungu “mumzimu ndi m’choonadi,” monga momwe Yesu Kristu ananenera. Izi zatanthauza kukana mabodza achipembedzo ndi kuchita mogwirizana ndi Mawu olembedwa a Mulungu.—Yoh. 4:23, 24; 2 Tim. 3:15-17.
—Timafikira anthu m’malo moyembekezera kuti iwo atipeze: Tavomera ntchito ya Kristu yolalikira ndi kuphunzitsa, ndipo timatsanzira chitsanzo chake chofunafuna anthu oona mtima. Timawafunafuna kunyumba zawo, mumsewu, kapena kulikonse kumene angapezeke.—Mat. 9:35; 10:11; 28:19, 20; Mac. 10:42.
—Timapereka malangizo a m’Baibulo kwa aliyense kwaulere: Timagwiritsa ntchito zinthu zathu ndi mphamvu zathu mosaumira, tikumathera maola oposa biliyoni imodzi chaka chilichonse mu utumiki wa Mulungu. Timaphunzira Baibulo ndi anthu a mitundu yonse mosasankha.—Mat. 10:8; Mac. 10:34, 35; Chiv. 22:17.
—Ndife ophunzitsidwa bwino kuti tithandize anthu mwauzimu: Mwa phunziro lathu laumwini la Baibulo ndi malangizo operekedwa pamisonkhano yampingo, yadera ndi yachigawo, timalandira maphunziro apamwamba kwambiri ndi osalekeza a teokalase amene amatithandiza kuchenutsa ena mwauzimu.—Yes. 54:13; 2 Tim. 2:15; 1 Pet. 3:15.
—Sititenga choonadi mopepuka, timachigwiritsadi ntchito m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku: Chifukwa cha kukonda kwathu Mulungu, timasintha nkugwirizanitsa moyo wathu ndi chifuno chake. Umunthu wathu watsopano wonga wa Kristu umakopera ena m’choonadi.—Akol. 3:9, 10; Yak. 1:22, 25; 1 Yoh. 5:3.
—Timayesetsa kukhala ndi ena ndi kugwira nawo ntchito mwamtendere: Kukulitsa mikhalidwe yaumulungu kumatithandiza kusamalira kalankhulidwe ndi kachitidwe kathu ka zinthu. ‘Timafunafuna mtendere ndi kuulondola’ ndi anthu onse.—1 Pet. 3:10, 11; Aef. 4:1-3.
2 Zitsanzo za moyo wachikristu zimene anthu amaona m’gulu la Yehova zimasonkhezera ambiri kuti alandire choonadi. Chitsanzo cha ife eni chikhaletu ndi zotsatirapo zofananazo kwa aja amene amatidziŵa ndi kutiona.