Misonkhano Yautumiki ya December
Mlungu Woyambira December 7
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Ndiponso, “Kodi Mwayambitsa Phunziro la Baibulo?”
Mph. 15: “Tiyenera Kuwafikira Mobwerezabwereza.” Mafunso ndi mayankho. Kambanipo mwachidule pa Ezekieli 3:17-19 kuti mugogomezere udindo wathu wopereka uthenga wachenjezo.
Mph. 20: “Kugaŵira buku la Chidziŵitso.” Mbale akambirane nkhaniyi ndi ofalitsa okhoza bwino aŵiri kapena atatu. Chitani chitsanzo cha kugaŵira buku logaŵira mu December ndiponso mmene tingatchulire chopereka chanthaŵi zonse.
Nyimbo Na. 176 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 14
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Perekani malingaliro a mmene tingayankhire mochenjera moni wapanthaŵi ya maholide adziko. Ngati mpingo wanu uli ndi mabuku a Munthu Wamkulu kapena Mphunzitsi Wamkuru’yo sonyezani mmene angagwiritsidwire ntchito mogwira mtima mu utumiki pa maholide a Khirisimasi. Longosolani makonzedwe apadera a utumiki wakumunda a pa December 25 ndi pa January 1.
Mph. 15: “Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda.” Nkhani yokambidwa ndi wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Alongosole ntchito yake ndi mmene anthu onse ofika pa phunzirolo angathandizire kuti likhale phunziro losangalatsa, lopatsa chidziŵitso, ndi lomangirira mwauzimu.—Onani buku la Uminisitala Wathu, tsamba 67.
Mph. 20: “Atha Kuona Kuti Ndife Osiyana.” Mafunso ndi mayankho. Pendani mwachidule mkhalidwe uliwonse umene umatipanga kukhala apadera. Sonyezani mmene chidziŵitso chimenechi chingagwiritsidwire ntchito potsogoza anthu okondwerera kugulu ndi powasonyeza mmene choonadi chimabweretsera mikhalidwe yachikristu mwa amene amakhala ndi moyo wotero.
Nyimbo Na. 146 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 21
Mph. 5: Zilengezo za pampingo. Limbikitsani ofalitsa onse kuti azisunga makope awo a Utumiki Wathu Waufumu, makamaka mphatika. M’tsogolomu tingamapemphedwe kuzionanso.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 25: “Mangani Moyo Wanu pa Utumiki wa Yehova.” Mafunso ndi mayankho. Funsani munthu amene ndi mbeta ndi munthu amene ndi mutu wabanja amene akhala okhoza kupita mu utumiki wakumunda mosajomba ndi mokhazikika mlungu uliwonse. Alongosole zimene munthu amafunika kulinganiza kuti aziika zinthu zauzimu patsogolo.
Nyimbo Na. 119 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 28
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti a utumiki wakumunda a December. Sonyezani buku lililonse la masamba 192 limene mpingo uli nalo loti ligaŵiridwe mu January. Limbikitsani ofalitsa kuombolako ena akuti agaŵire pamapeto a mlungu uno.
Mph. 10: “Pindulani ndi Pologalamu ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 1999.” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Ofalitsa ena asimbe mapindu amene apeza mwa kutsatira “Ndandanda ya kuŵerenga Baibulo Yowonjezera” mlungu uliwonse. Limbikitsani onse kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse.
Mph. 25: “Kodi Mumalemekeza Malo Anu Olambirira?” Nkhani yokambidwa ndi mkulu kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1993, masamba 28-31. Limbikitsani onse kuti azilemekeza kwambiri malo athu olambirira.
Nyimbo Na. 195 ndi pemphero lomaliza.