Kodi Mwayambitsa Phunziro la Baibulo?
◼ Kodi mumaphunzira mokhazikika ndi banja lanu, ngati inu ndinu mutu wabanja?
◼ Kodi mwayesa kuyambitsa phunziro la Baibulo ndi wachibale wanu, mnzanu wa kuntchito kapena wa kusukulu?
◼ Kodi mumapanga maulendo obwereza mwakhama kwa amene anasonyeza chidwi ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo?
◼ Bwanji osapanga kuyambitsa phunziro la Baibulo kukhala cholinga chanu mwezi uno?