Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/99 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 6/99 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu June: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. July ndi August: Lililonse la mabolosha a masamba 32 ali m’munsiŵa angagwiritsidwe ntchito: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha. Bolosha la Mizimu ya Akufa—Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? lingagaŵiridwe pamene kuli koyenera. September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.

◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina amene iye wamusankha ayenera kuŵerengera maakaunti a mpingo pa June 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detili. Akatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo mutapereka lipoti lotsatira la maakaunti.

◼ Tikufuna kumveketsa zinthu bwino ku mabungwe a akulu amene sakudziŵa mmene Sukulu ya Utumiki Wateokalase ndi Msonkhano wa Utumiki ziyenera kukhalira m’mlungu umene ali ndi woyang’anira dera. Ikatha nyimbo yotsegulira ndi pemphero pazikhala Sukulu ya Utumiki yamphindi 30 yokhala ndi nkhani ya chilangizo yamphindi 10 yopanda mafunso openda, mfundo zazikulu za Baibulo, nkhani yachiŵiri (kuŵerenga Baibulo), ndi nkhani inanso ya wophunzira. Pasakhale nyimbo yotsegulira Msonkhano wa Utumiki umene umatsatirapo, umene ungasinthidwe kuti ukhale wa mbali zitatu zamphindi 10 kapena mbali ziŵiri zamphindi 15, popanda zilengezo. Kenako pazikhala nyimbo, kenako nkhani ya woyang’anira dera yamphindi 30. Pologalamu yonse izikhala ya ola limodzi ndi theka, osaphatikizapo nyimbo ndi pemphero.

◼ N’kolimbikitsa kuona kuti Sosaite inalemba m’makope apapitapo a Utumiki Wathu wa Ufumu kuti atsegula zipinda za mabuku kunyumba ya amishonale ya ku Blantyre, ku Zomba, pa Beteli ku Lilongwe, ndi kunyumba ya amishonale ya ku Mzuzu. Abale—apainiya ndi ofalitsa omwe—tsopano akhoza kugula mabuku ogwiritsa ntchito mu utumiki wakumunda ndi kumisonkhano ya mpingo. Koma kwapezeka kuti apainiya ena amabwera ku zipinda za mabuku zimenezi ndi kugulira ofalitsa a kumpingo mabuku pamtengo wa mpainiya. Izi si zoyenera. Abale sayenera kupita ku zipinda za mabuku zimenezi ndi kugula mabuku pamtengo wa mpainiya ndi kumawagulitsa kwa ofalitsa pamtengo wa ofalitsa. Mabuku ogulira wofalitsa ayenera kugulidwa pamtengo wa wofalitsa, ngakhale ngati mpainiyayo watumidwa ndi wofalitsa.

◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:

Buku la Anthu Onse—Chicheŵa, Chingelezi

Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha—Chicheŵa, Chitumbuka

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena