Mwayi Umene Sunapezekeponso
1 Kodi mwaona mmene kuipa kwa mikhalidwe padziko kwapangitsira kulankhula choonadi ndi anthu masiku ano kukhala kosavuta? N’zoona kuti ambiri samvetsera uthenga wathu, koma zimenezo zimangotsimikizira kuti tikukhala m’masiku otsiriza. (2 Tim. 3:1-5) Ndipo tikamaona zimenezi timasangalala, si choncho kodi? Nanga chimachitika n’chiyani tikakumana ndi okonda chilungamo? Kodi saonetsa kuti akufunitsitsa kulankhula nafe ndi kutinso akufuna mayankho a mafunso awo? Inde, ano ndiwo masiku a mwayi umene sunapezekeponso wochitira umboni za Ufumu wa Yehova. Tikusangalala kwambiri pokhala ndi moyo m’nthaŵi imeneyi!
2 Mwanzeru, Atate wathu wakumwamba Yehova wapereka utumiki wa kunyumba ndi nyumba monga njira yabwino kwambiri pofuna oyenerera. Ntchito imeneyi imayenerana ndi maluso a aliyense wa ife, chifukwa imaphatikizapo kulankhula ndi munthu mmodzi kapena aŵiri nthaŵi imodzi, ndiponso, ndiyo njira yabwino kwambiri yotsimikizira kuti palibe amene akutsala pa anthu amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo.—Mat. 5:6.
3 Komabe, malipoti a mipingo ina m’dziko lino akusonyeza kuti ambiri sakuchirikiza ntchito ya kunyumba ndi nyumba, makamaka mkati mwa mlungu. Kodi abale, n’chiyani chikuchititsa zimenezi? Kodi ena mwa ife chiyamikiro chathu chikuchepa pa mbali imeneyi ya utumiki wathu? Kodi taiŵala mawu a Paulo pa Machitidwe 20:20 onena za kuphunzitsa kunyumba ndi nyumba? Kodi tikuiŵala kuti njira yabwino kwambiri yoonana ndi anthu ndiyo kuwafikira pamakomo pawo?—Mat. 10:11-13.
4 N’zoona kuti ntchito yolalikira ikutsogozedwa ndi angelo, ndipo angelowo lerolino ali otanganidwa kwambiri kutsogoza ntchitoyo! (Mat. 24:31; Chiv. 14:6, 7) Koma funso ndi lakuti, Kodi ife aliyense payekha tikutengamo mbali mokwanira m’ntchito imeneyi? Taganizani za madalitso amene tingaphonye ngati sitichita mokwanira utumiki wa kunyumba ndi nyumba, makamaka pamene tikudziŵa kuti Yehova ndi angelo ake akuichirikiza kwambiri ntchito imeneyi. (1 Akor. 3:9) Ndithudi kudziŵa kwathu zimenezi kuyenera kutilimbitsa mtima ndi kutipatsa changu ndi kuti chopinga chilichonse, sichingakhoze kutifooketsa kapena kutiletsa kupitiriza ntchitoyi.
5 Ambiri a ife timafuna kuchita ntchito ya kunyumba ndi nyumba. Tili ndi maganizo abwino kwa Yehova ndi anthu onga nkhosa. Koma ena angazengereze kuchita ntchito imeneyi, chifukwa sadziŵa zoti akanene. Ngati ndi mmene mumaganizira, bwanji osapangana ndi wochititsa phunziro la buku la mpingo kapena mkulu wina kuti musangalale ndi mwayi umenewu? Ngati akulu apereka chitsanzo komanso kutsogolera ntchito ya kunyumba ndi nyumba, mpingo udzadalitsidwa kwambiri. (Mat. 11:1) Ngati apanganiranatu ndi ena, mwinamwake zogwira ntchito pamodzi mapeto a mlunguwo, m’kupita kwa nthaŵi angachite zambiri pakuphunzitsa ena ntchito ya kunyumba ndi nyumba. Ngati simungathe kukhala nthaŵi yaitali, khalani kwa nthaŵi imene mungathe, pakutitu Yehova amalandira zimenezo.—Luka 21:2-4.
6 Abale athu ena amakhala ndi misonkhano mmaŵa ndipo apeza kuti Lamlungu masana ndi nthaŵi yabwino yopita mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Panthaŵi ngati imeneyi anthu sakhala otanganidwa ndipo nthaŵi zambiri amakhala ndi maganizo abwino komanso osavuta kuwalankhula. Nthaŵi imeneyi, mwayi wapezeka woyambitsa maphunziro a Baibulo ambiri, ntchito imene imatithandiza kupanga ophunzira.
7 Ofalitsa ena anena kuti amakhala otanganidwa kwambiri mkati mwa mlungu moti satha kuchita nawo utumiki wa kunyumba ndi nyumba. N’zoona, dziko limene tikukhala n’lotanganitsa. Tonsefe nthaŵi zina timafunika kupeza zofunika pa moyo wa tsiku ndi tsiku, si choncho kodi? Koma tikudziŵa kuchuluka kwa zimene tingachite, choncho timachita zomwe tingathe. Mfundo n’njakuti ngati tipeza mpata m’miyoyo yathu wochitira utumiki umenewu, ngati tizindikira kuti ntchito imeneyi sidzabwerezedwanso, tidzakhaladi ndi maganizo abwino ku utumiki umenewu. Komanso utumiki wakumunda ulinso mankhwala othetsa kutopa. Umachiritsa. Umatithandiza kukhala ndi maganizo abwino moti pochoka mu utumiki wakumunda timamva bwino m’maganizo ndi m’thupi.
8 M’nthaŵi za m’Baibulo, atumiki anzathu, Yeremiya, Ezekieli ndi Yesaya anapereka mauthenga ku mtundu wa Israyeli. M’nthaŵi yawo anali aneneri a Yehova. Ena mwa aneneri amenewa, monga Yeremiya, anauzidwiratu kuti palibe amene adzamvetsera uthenga wawo. Yehova anati: “Uzinena kwa iwo mawu awa onse, koma sadzakumvera iwe; ndipo udzawaitananso; koma sadzakuyankha iwe.” (Yer. 7:27) Kodi lero anthu ena amene tingawalalikire kunyumba ndi nyumba angakhale osalabadira kuposa pamenepa? Komabe, mosasamala kanthu za maganizo a Aisrayeli amenewo, Yeremiya anapirira. Alidi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife kuti tipirire pantchito yokhutiritsayi imene imatipatsa mwayi waukulu wochitira umboni za Ufumu masiku ano!
9 Lero tikukhala ‘m’nthaŵi ya chimaliziro.’ Tiyenera kufunafuna oyenerera kuti asadzawonongeke pa “chisautso chachikulu.” (Mat. 10:11) Ano ndiwo masiku otsiriza a dongosolo la zinthu lakale lino komanso a ntchito ya kunyumba ndi nyumba imene sidzabwerezedwanso.
10 Chokumana nacho chotsatirachi chikutithandiza kuona mmene ntchito yathu ya kunyumba ndi nyumba imakhudzira anthu. Mwamuna wina wachikulire anauza mbale wathu wina amene anali kupita kunyumba ndi nyumba kuti: “Anthu inu ndimakusirirani kwambiri, ana ndi akulu omwe. Ndinu nokha amene mumalimba mtima kupita kunyumba ndi nyumba ndi uthenga wanu wachipembedzo.” Inde, utumiki wa kunyumba ndi nyumba umatidziŵikitsa kuti ndife atumiki enieni a Yehova ndipo umapatsa anthu oona mtima mwayi woona ntchito za Chikristu. Kodi inuyo panokha mukutengamo mbali mokwanira mu utumiki umenewu?