Samalirani Mapesedwe ndi Mavalidwe Anu
1 Maonekedwe aumwini abwino ndi ofunika pazifukwa zambiri. Ngati sizipatsidwa chisamaliro chokwanira, mtumiki angapeze kuti maonekedwe ake akudodometsa anthu akunja mwakuti samvetsera kwenikweni ulaliki wake. M’malo mwake, amachititsa anthu kuchita chidwi ndi iye, zimene mwachionekere, sichili cholinga chake. Ngati munthu sasamalira maonekedwe ake aumwini, angapangitse ena ngakhale kunyoza gulu limene iye alimo ndi kukana uthenga umene akupereka. Izi siziyenera kukhala chonchi. Chotero, ndi bwino kuti nkhani imeneyi ikambidwe.
2 Osati Sitayelo, Koma Kusiyana ndi Machitachita a Dziko: Tingaone nkhani ya sitayelo, kapena ya kavalidwe, mwa njira ina. Yerekezerani kuti inu, monga mwamuna, munakhalako m’nthaŵi ya Israyeli, pamene kunali Chilamulo, ndipo simunali kukonda ndevu. Mwinamwake munali kukonda mmene Aigupto amaonekera, ometa bwino. Kodi munakachita chiyani? Kodi mukanachita zofuna zanu ndi kumeta? Ayi, popeza simukanakhala ndi ufulu umenewo. Mukanayenera kusunga ndevu, chifukwa Chilamulo chinalamula amuna onse kuti: “Musamameta mduliro, kapena kusenga m’mphepete mwa ndevu zanu.”—Lev. 19:27; 21:5.
3 Kodi Lamulo limeneli linaperekedwa monga sitayelo? Ayi. Kunali kutetezera Aisrayeli kuti asatsatire zochita za mitundu ina yachikunja yowazungulira. Aisrayeli anafunika kusunga ndevu zawo zoduliridwa bwino, zaudongo, komanso zopesedwa bwino. Ndevu zosasamalidwa kapena zometedwa zinali kusonyeza chisoni ndi kulira chifukwa cha masoka ena. (2 Sam. 19:24-28; Yes. 7:20) Komanso kaŵirikaŵiri amadulako tsitsi, kokha ngati anali Mnaziri sanali kulidula. Mu ulosi wa Ezekieli ansembe analamulidwa kumanga pamodzi tsitsi lawo osati kungolisiya losamanga.—Ezek. 44:15, 20, NW.
4 ‘Chibadwidwe Chomwe,’ Chimatiphunzitsa: M’Baibulo mulibe malamulo enieni onena, mwachitsanzo, za mmene tsitsi liyenera kutalikira, kapena autali wa siketi. Koma mtumwi wouziridwayo anapereka zitsogozo zabwino zimene zimapangitsa Akristu oona, odzipatulira, komanso mpingo, kudziŵa pamene sitayelo kapena chikhalidwe chili choyenera, ndi chabwino. Anati: “Kodi ubadwidwe womwe sutiphunzitsa kuti ngati mwamuna aweta tsitsi chimnyozetsa iye? Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lake lapatsidwa kwa iye ngati chophimba.”—1 Akor. 11:14, 15.
5 Ponenapo za mawu a mtumwi amenewa, wophunzira za Baibulo Albert Barnes ananena kuti: “Liwulo chibadwidwe . . . mwachionekere limatanthauza mmene aliyense amamvera kuti ayenera kuchita zinthu zoyenera, malingana ndi mmene zinthu zimakhalira kaŵirikaŵiri kapenanso malinga ndi chikhalidwe chonse. . . . Zili monga mmene amuna onse mwachibadwa amafunira kukhala amphamvu . . . Choncho, liwulo pankhaniyi silitanthauza khalidwe la mkazi kapena la mwamuna, . . . kapena chizoloŵezi wamba ndi chikhalidwe, . . . koma limatanthauza chikhumbo chachikulu chochita zabwino ndi zoyenera.” Ndipo wophunzira za Chigiriki Dr. A. T. Robertson ananena kuti: “Pamenepa limatanthauza chikhumbo chachibadwa chofuna kuchita zoyenera (yerekezerani ndi Aroma 2:14) kuphatikiza pa chikhalidwe wamba, koma chimene chimasiyanitsa zinthu.”
6 Choncho si nkhani yochita kuuzidwa choyenera kuchita ndi chosayenera kuchita, monga mwa malamulo. Ngati ndife Akristu ndipo mitima yathu imakonda chimene chili chabwino, timadziŵa mwachibadwa, makamaka chifukwa cha chikumbumtima chathu chophunzitsidwa, ngati chinthu chikuwonjezera kapena kuchotsa ulemerero wa uthenga wabwino umene timalalika. Timadziŵa ngati tikumangirira kapena tikupasula mbiri kapena chithunzi cha mpingo m’maso mwa ena. Koma, ngati wina sadziŵa, ayenera kulamuliridwa ndi chikumbumtima chabwino cha mpingo wachikristu. Ayenera kumvera uphungu wabwino ndi kudalira nzeru ya abale achikulire.—Miy. 12:15.
7 Akristu oona amakondana, ndipo amene ali ndi maudindo ayenera kuchitira abale awo zinthu zabwino zokhazokha, kaya mwa chitsanzo chimene amasonyeza, kapena uphungu umene amapereka. Nthaŵi zonse zochita zathu tonsefe ziyenera kutsogozedwa ndi pulinsipulo lakuti: Kodi ‘ndikukometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse’? Ngati timasamalira maudindo athu, ndi kuwachita ndi moyo wonse monga kwa Yehova, osati kwa anthu, Yehova adzatipatsa madalitso ochuluka kuposa “ufulu” uliwonse umene tingadzipatse tokha, ndi zaka za moyo ndi mtendere.—Tito 2:10; Akol 3:23, 24; Miy. 3:1, 2.
8 Musalole Kutcheredwa Msampha ndi Mafashoni: Masitayelo opambanitsa atsitsi angatcherenso wina msampha wa Mdyerekezi, ndi kukhumudwitsa ena. Mwachitsanzo, mnyamata wina ku United States anali kupita patsogolo ndi phunziro lake la Baibulo, ndipo analimbikitsidwa kupita kukalalikira ndi Mboni yozoloŵera za zinthu zabwino zimene anali kuphunzira m’Baibulo. Kuyambira kumayambiriro kwa unyamata wake anali kusunga ndevu, komanso popeza anthu ena ogwira ntchito anali kusunga ndevu, anaganiza kuti kupita choncho ndi ndevu zake kolalikira kukakhala kopanda vuto. Koma polankhula kwa mkazi wina sananene zambiri koposa kungonena mawu oyamba okha, pamene mkaziyo ananena kuti: “Pepa, mnyamata, sindikufuna kukhala m’gulu la anyamata oukira.” Palibe mawu ena amene anakatha kunena kuti achotse malingaliro olakwawa. Makambitsiranowo atatha mwa kutseka chitseko, mnyamatayo anafunsa Mboni yozoloŵerayo zimene zachitika. Anamupempha kupenda maonekedwe ake mogwirizana ndi zimene anali kudzinenera kukhala, mtumiki wa Mulungu. Posafuna kukhala ndi mlandu wa amene angakhumudwe komanso kuphonya moyo wosatha, wofalitsa za Ufumu woyamba kumeneyu anameta ndevu zake. Kodi mudzakhala wofunitsitsa kuchita zofananazo kapena kupanga masinthidwe ofananawo ngati maonekedwe anu amapereka chithunzi cholakwika m’dera lina?
9 Tiyenera kuzindikira kuti dziko limayang’ana anthu a Yehova. Uthenga wa Ufumu umene amapititsa kwa anthu nthaŵi zina umaweruzidwa ndi maonekedwe a anthu amene akuupereka. Zingatheke kuti mbale kapena mlongo wachikristu amene wavala sitayelo ina yake angakope chidwi cha munthu yemwe wamupeza panyumba moti munthuyo sakumvetsera zimene Mkristuyo akunena, koma kuganiza kuti sitili osiyana ndi anthu adziko m’makhalidwe. Ngati zili chonchi, wolalikirayo waphonya cholinga chake chonse cha utumiki wakumunda. Nthaŵi zina timapemphedwa kulepa zinthu zimene timafuna, kumlingo wokulira kapena wochepera, malinga ndi kufunika kwake, kuti tipeŵe kukhumudwitsa ena. Umenewu unali mkhalidwe wa mtumwi Paulo. Iye anati: “Osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe; koma m’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu.”—2 Akor. 6:3, 4.
10 Maonekedwe ndi Ofunika: Posachedwapa Khoti Lapamwamba ku United States linachirikiza chigamulo cha District Court chakuti kampani ya masitolo akuluakulu ili ndi ufulu wokhalabe ndi lamulo lakuti antchito ena “asamasunge ndevu.” Munthu amene anatchotsedwa ntchito chifukwa chokana kumeta ndevu anakapanga apilo. Anati ali ndi vuto la matenda a pakhungu amene ali ofala pakati pa anthu akuda amene amayamba kuyabwa kapena kupanga zilonda pamene ndevu ziyamba kumera. A District Court anagamula kuti “lamulo limenelo la kampani ya masitolo akuluakulu linali ndi cholinga chothandizira bizinesi chimene chinali chofunika kwambiri kuposa mmene linawakhudzira pang’ono anthu olembedwa ntchito,” inatero American Medical News.
11 Nyumba ya Aphungu ku California inati, pamsonkhano wa aphungu, amuna ayenera kuvala “zovala zoyenera,” monga majekete ndi mataye. Phungu amene anadzutsa mfundo imeneyi ananena kuti “maonekedwe ndi ofunika,” ndi kuti anthu onse amakupatsanso ulemu. Ndithudi izi ndi zoonanso kwa onse amene amanena kuti akuimira Wopanga Malamulo wamkulu m’chilengedwe chonse, Yehova Mulungu.
12 Masitayelo ena akametedwe ka tsitsi ndi kusunga ndevu sangakhale oipa pa iwo okha koma kungakhale kulakwa Mkristu kuchita zimenezi ngati ena m’deralo angakhumudwe nazo, ndipo ngati angam’fanizire ndi anthu ena adziko kapena ngati angaganize kuti akutsata miyambo ina yake. Mwachitsanzo, akatswiri ena omenya nkhonya, amameta tsitsi lonse m’mutu, ndi kukhala ndi mpala. Anthu ambiri masiku ano amachita zofananazo powatsatira. Ngati Mkristu wachinyamata ameta mwanjira imeneyi—popanda zifukwa zenizeni—kodi anthu angamuone kuti ndi wosiyana ndi dziko? Bwanji Akristu ena mumpingo, kodi sangakhumudwe?
13 M’madera ena m’Malawi muno mwambo wometa achinyamata amene akula amaumaliza mwa kuwameta mipala. Tsopano ngati timeta mofanana ndi mmene amachitira, kodi anthu ena angatiganizire zotani? Ngakhale kuti palibe lamulo la mmene tiyenera kumetera, nthaŵi zonse ndi bwino kutsatira chitsanzo chabwino cha mtumwi Paulo amene anati: “Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chilichonse chakukhumudwitsa mbale wako.”—Aroma 14:21.
14 Mofanana ndi Akristu oyambirira, lerolino atumiki achikristu amasamala za udongo ndi ukhondo, koma amayesetsa kuti asavale mopambanitsa, kuti maonekedwe awo m’njira iliyonse asachotsere ulemu uthenga umene ali nawo kapena kuuchititsa kuti usakhale wogwira mtima. (2 Akor. 6:3, 4) M’zaka zinozi m’mayiko ambiri ndevu kapena tsitsi lalikulu la mwamuna limadabwitsa anthu ndipo zingapangitse ambiri kuganiza kuti munthu ameneyo akugwirizana ndi magulu ogalukira kapena zigaŵenga. Atumiki a Mulungu amafuna kupeŵa kupereka chithunzi chimene chingachotse chidwi pa utumiki wawo kapena kulepheretsa aliyense kumvetsera choonadi. Amadziŵa kuti anthu amayang’anira Akristu oona kwambiri ndi kuti iwo makamaka amaweruza mpingo wonse ndi uthenga wabwino mwa maonekedwe a mtumikiyo monga woimira mpingo.
15 Chikatikati ndi Maonekedwe Aumwini: Za mavalidwe oyenera kwa abale pamene akupereka nkhani mu sukulu kapena pamsonkhano wa utumiki, kunganenedwe kuti ayenera kuvala mofanana ndi mbale amene amapereka nkhani yapoyera. Ngati nthaŵi zonse m’dera lanulo amene amapereka nkhani zapoyera amavala taye ndi jekete, ndiye kuti zimenezo ndizo zovala zoyenera popereka nkhani mu Sukulu ya Utumiki Wateokalase, popeza kuti mukuphunzitsidwa kukamba nkhani poyera.
16 M’pofunikanso kupereka chisamaliro pa mapesedwe oyenera. Tsitsi losapesa lingapereke chithunzi cholakwika. Tiyenera kusamala ndithu kuti tikhale ndi maonekedwe audongo. Mofananamo, pamene amuna mu mpingo ali ndi nkhani pamisonkhano, ayenera kuona kuti ameta bwino ndevu zawo.