Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/99 tsamba 2-7
  • Misonkhano ya Utumiki ya August

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano ya Utumiki ya August
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira August 2
  • Mlungu Woyambira August 9
  • Mlungu Woyambira August 16
  • Mlungu Woyambira August 23
  • Mlungu Woyambira August 30
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 8/99 tsamba 2-7

Misonkhano ya Utumiki ya August

Mlungu Woyambira August 2

Nyimbo Na. 39

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Tchulani za lipoti la utumiki wakumunda la April, la dzikolo ndi la mpingo wanu. Limbikitsani ofalitsa onse kutenga mbali mu utumiki wakumunda mu August.

Mph. 17: “Lilemekezeni Kwambiri Dzina Lokoma la Yehova.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosakwana imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gogomezerani malemba operekedwawo.—Onani buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha, masamba 184-5.

Mph. 18: “Maphunziro Akusukulu ndi Zolinga Zanu Zauzimu.” Bambo akambirane nkhaniyi ndi mwana wake wamwamuna kapena wamkazi. Apendenso nkhani zofanana ndi nkhaniyi mu Galamukani! wa January 8, 1996, patsamba 23-27.

Nyimbo Na. 148 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 9

Nyimbo Na. 138

Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 12: Apainiya Athandiza Ena—N’kupita Patsogolo Kotani Kumene Kwachitika? Nkhani ndi kufunsa kochitidwa ndi woyang’anira utumiki. Pendani malangizo operekedwa mu Utumiki Wathu Waufumu wa September 1998, patsamba 4. Simbani mmene zimenezi zinalinganizidwira pampingopo, ndipo nenani kupita patsogolo komwe kulipo kwa awo amene anathandizidwa. Funsani mpainiya mmodzi kapena aŵiri ndi ofalitsa ena amene apindula ndi thandizo lawo. Limbikitsani enanso amene athandizidwe kupezerapo mwayi pa makonzedwe amenewa.

Mph. 25: “Kodi Tsopano Khomo Lochita Upainiya Lakutsegukirani?” Nkhani ya mkulu ya mafunso ndi mayankho. Molimbikitsa, sonyezani mipata imene ilipo yoti ofalitsa ambiri angachite upainiya. Funsani apainiya asimbe zokumana nazo zawo za mmene anagonjetsera zopinga zofala. Pendani “Zitsanzo za Ndandanda ya Apainiya Okhazikika,” ndipo gogomezerani mmene kukonzekera bwino kungapangitsire maola ofunikawo kukhala osavuta kukwaniritsa. Lengezani kuti aliyense amene akufuna fomu yofunsira upainiya atha kutenga mutamaliza msonkhano.

Nyimbo Na. 202 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 16

Nyimbo Na. 131

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kwatsala milungu iŵiri yokha kuti August athe, choncho limbikitsani onse kutenga mbali mu utumiki mwezi usanathe. Pendani “Pologalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera.”

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: Kodi Mukuchita Nawo Ntchito Yopanga Ophunzira? Kukambirana ndi omvetsera. Poona kuchuluka kwa mabuku amene amagaŵiridwa, cholinga chathu chiyenera kukhala kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba kuti tithandize anthu kupindula ndi mabuku amene amalandira. Khalani ndi ofalitsa kuti anene mavuto amene amawalepheretsa kuchititsa maphunziro ochuluka: (1) Ndi kovuta kupeza anthu ofuna kuphunzira. (2) Anthu ena amene amasonyeza chidwi amanena kuti sangapeze nthaŵi yophunzira. (3) Phunziro likayambitsidwa, n’kovuta kupeza munthuyo panyumba kuti phunzirolo likhale lokhazikika. Komanso nenani malingaliro amene ofalitsa ena amakhala nawo ponena za ntchito yochititsa maphunziro a Baibulo: (1) ‘Ndilibe luso lophunzitsa.’ (2) ‘Ndilibe nthaŵi yochititsira phunziro mlungu uliwonse.’ (3) ‘Sindifuna kukhala ndi udindo kwa munthu wina aliyense.’ (4) ‘Kuchita nawo mbali zina za utumiki kumandikwanira.’ Perekani malingaliro othandiza a mmene angagonjetsere zopinga zimenezi kuti paokha atenge mbali m’ntchito yopanga ophunzira. Khalani ndi ofalitsa opita patsogolo anene chimwemwe chimene apeza m’ntchito yochititsa maphunziro a Baibulo.—Onani m’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa May 1998, ndime 3-8, 15.

Nyimbo Na. 100 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 23

Nyimbo Na. 94

Mph. 10: Zilengezo za pampingo.

Mph. 15: Thandizani Achatsopano Kuzindikira Kupatulika kwa Ukwati. Kukambirana ndi omvetsera kotsogozedwa ndi mkulu kuchokera mu buku la Kukambitsirana, masamba 383-85. Timakumana ndi mabanja amene amamvetsera uthenga wa Ufumu koma amene amachedwa kupita patsogolo chifukwa chakuti akukhalira pamodzi popanda kulembetsa ukwati wawo mwalamulo. Kambiranani mmene tingawathandizire kumvetsetsa chifukwa chake Akristu ayenera kukhala ndi ukwati wolemekezeka. (Onani Galamukani! wa January 8, 1992, masamba 30-31.) Perekani malingaliro a zimene tinganene mochenjera pothandiza mabanja oterowa kuzindikira chifukwa chake sangakhale mbali ya mpingo mpaka atalembetsa ukwati wawo mwalamulo.

Mph. 20: “Kodi Mukanena Chiyani kwa Mbuda?” Mafunso ndi mayankho. Nthaŵi zambiri timasoŵa chonena pamene m’gawo tapezamo anthu amene sali achipembedzo chachikristu okhala ndi malingaliro, zochita, komanso miyambo yachilendo kwa ife. Nkhani imeneyi ndi yoyamba pankhani zisanu zimene zidzatsatire. Onetsani chitsanzo cha ulaliki wokonzedwa bwino kwambiri. Zina zowonjezera za Abuda mungazipeze m’buku la Kukambitsirana, patsamba 21.

Nyimbo Na. 133 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 30

Nyimbo Na. 99

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti a utumiki wakumunda a August. Ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo ayenera kuona kuti aliyense wa m’kagulu kawo wapereka malipoti kuti onse akhale atasonkhanitsidwa pofika pa September 6.

Mph. 17: Timakonda Abale Athu. Nkhani yokambidwa ndi mkulu, kuphatikizapo kukambirana ndi omvetsera kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1995, masamba 15-17, ndime 7-11. Gogomezerani mapindu amene tonse timapeza pamene tidziŵana bwino ndi abale athu, kulimbikitsana, ndi kuthandizana kupirira ziyeso. Nenani mmene zimenezi zingachitikire mokulirapo. Pemphani omvetsera kusimba zochitika zosonyeza mmene anatsitsimulidwira komanso kulimbikitsidwa ndi chilimbikitso chachikondi cha ena.

Mph. 18: Nenani Chifukwa cha Chiyembekezo Chanu. Mkulu afunse wachinyamata mmodzi kapena aŵiri achitsanzo chabwino amene ali pasukulu. Amakumana ndi mikhalidwe imene anzawo achikunja amafuna kudziŵa chifukwa chake iwo sachita nawo zinthu zimene anzawo amachita. Pogwiritsa ntchito mipata imeneyo kufotokoza zikhulupiriro zawo za m’Baibulo, achinyamata athu afunika kukhala osasintha pakukana kwawo. Anthuwa akambirane mmene angachitire ngati apatsidwa fodya kapena mankhwala osokoneza bongo. Pendani zifukwa zoperekedwa m’buku la Achichepere Akufunsa, masamba 277-81. Fotokozani mmene kutchinjiriza chosankha chawo chochita chimene chili chabwino kumakhalira chitetezo komanso mmene kumaperekera umboni wabwino.

Nyimbo Na. 129 ndi pemphero lomaliza.

Yapitirizidwa patsamba 7

Misonkhano (kuchokera patsamba 2)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena