Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/00 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira April 10
  • Mlungu Woyambira April 17
  • Mlungu Woyambira April 24
  • Mlungu Woyambira May 1
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 4/00 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira April 10

Nyimbo Na. 122

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Musaiwale nkhani yapoyera yapadera pa April 16, yamutu wakuti “Chifukwa Chake Mtundu wa Anthu Ukufunikira Dipo.” Limbikitsani onse kutsatira ndandanda ya kuŵerenga Baibulo ya Chikumbutso ya April 14-19, monga alembera m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2000. Pendani “Zofunika Kukumbukira Panthaŵi ya Chikumbutso,” patsamba 4 m’mphatika.

Mph. 15: “Kodi Mukuyamikira Chikondi cha Kristu?” Kambani mawu oyamba mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 1998, masamba 16-17, ndime 12-13. Limbikitsani aliyense kuyesetsa kwambiri kuitanira anthu ku Chikumbutso.

Mph. 20: “April—Nthaŵi Yokhala Achangu pa Ntchito Zokoma!” Mafunso ndi mayankho. Kukambirana ndi mtima wonse zimene tikufuna kuchita mu April. Gwiritsani ntchito mphindi zitatu kapena zinayi za kumapeto amsonkhano uno kupenda kabokosi kakuti “Changu Chimene Chimautsa Ochuluka.”

Nyimbo Na. 199 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 17

Nyimbo Na. 25

Mph. 13: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kwangotsala mapeto a milungu aŵiri okha kuti mwezi wa April uthe, choncho limbikitsani onse kuloŵa nawo muutumiki wakumunda mweziwu usanathe. Sonyezani ulaliki wachidule pogwiritsa ntchito magazini atsopano. Popeza tingakakamizike kuwayankha anthu omwe akufuna kuti tichite nawo miyambo ya Isitala, pendani zimene zili m’buku la Kukambitsirana, masamba 242-43.

Mph. 16: “Kodi Muli Ndi Mzimu Wodzimana?” Mafunso ndi mayankho. Tiyenera kuika zinthu zofunika patsogolo. Pamafunika khama ndi kudziletsa kuti tipitirize kuchita zimene zingatipindulitse mwauzimu. Fotokozani zimene tingaphunzire mu chitsanzo cha Yesu.—Onani buku la Munthu Wamkulu, kamutu kakang’ono kachitatu ndi kachinayi m’mawu oyamba.

Mph. 16: Gaŵirani Magazini kwa Amene Angapindule Nawo Kwambiri. Nkhani, ndi kukambirana ndi omvetsera. Pendani mfundo zimene zaperekedwa mu Galamukani! wachigelezi wa January 8, 1995, masamba 22-4. Fotokozani chifukwa chake kuli kwabwino kufunafuna anthu amene angasangalale ndi nkhani zinazake za m’magaziniwo. Perekani zitsanzo kuchokera m’makope a m’mbuyomo ndiponso mtundu wa anthu, amalonda, kapena mabungwe amene anasangalala ndi nkhani zake m’gawo lanulo. Pemphani omvetsera kusimba zokumana nazo zosonyeza mmene anapindulira mwakutsatira njira imeneyi.

Nyimbo Na. 71 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 24

Nyimbo Na. 137

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lengezani chiŵerengero champingo cha opezeka pa Chikumbutso. Pemphani omvetsera kusimba zimene anthu omwe n’koyamba kukhala nawo pamwambowu ananena.

Mph. 17: Thandizani Atsopano Kufika pa Misonkhano. Nkhani yochokera m’buku la Chidziŵitso, masamba 161-3, ndime 5-8. Mutaphunzira nawo kwakanthaŵi ndithu, n’kofunika kuti atsopano ayambe kupezeka pa misonkhano. Kungakhale kovuta kuti muwalimbikitse kuyamba kupezekapo. Kodi mungatani kuti muwalimbikitse? Amene akuchititsa maphunziro ayenera kukhala ndi nthaŵi yopenda nkhaniyi ndi ophunzira awo kuchokera m’buku la Chidziŵitso ndiyeno n’kupanga makonzedwe owathandiza kuti akhale nawo m’kulambira koona.

Mph. 18: “Kodi Ndinu Wofalitsa Ufumu Wokhazikika?” Nkhani yokambidwa ndi mlembi yokambirana ndi omvetsera. Fotokozani chifukwa chake timapereka lipoti la ntchito yathu yautumiki wakumunda. (Onani Olinganizidwa, masamba 106-8.) Tchulani mavuto ena amene angakhalepo pamene tilephera kupereka malipoti athu panthaŵi yake. Pemphani omvetsera kunena zimene amachita kuti azikumbuka kupereka maola awo panthaŵi yake. Nenani mmene ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo angathandizire. Kwatsala mapeto a mlungu amodzi okha mu April, choncho gogomezani kufunika kwakuti aliyense apite muutumiki ndiponso kupereka lipoti la ntchitoyo pamapeto a mwezi.

Nyimbo Na. 200 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 1

Nyimbo Na. 213

Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti awo a muutumiki wakumunda a April. Ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo ayenera kuonetsetsa kuti aliyense m’gulu lawo wapereka malipoti kuti onse adzakhale atatumizidwa pofika pa May 6. Pendani Bokosi la Mafunso, tchulani kugwirizana komwe kulipo ndi mpingowo.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 18: “Kumbukirani Kubwererako!” Kukambirana ndi omvetsera. Pendani zifukwa zimene zingatilepheretse kupanga maulendo obwereza. Fotokozani chifukwa chake notsi zolondola ndi kufunitsitsa kubwererako zili zofunika. Perekani malingaliro opatula nthaŵi mlungu uliwonse yopanga maulendo obwereza. Pendani zimene zili m’buku la Olinganizidwa, masamba 88-9. Simbani chokumana nacho cha mu 1995 Yearbook, patsamba 45.—1 Akor. 3:6, 7.

Nyimbo Na. 68 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena