Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu April ndi May: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Khalani ndi bulosha la Mulungu Amafunanji kaamba ka anthu osonyeza chidwi, ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. June: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. July ndi August: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabulosha amasamba 32 ali m’munsiŵa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha komanso What Happens to Us When We Die? Mabulosha a Buku la Anthu Onse, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? angagaŵiridwe pamene kuli koyenera kutero.
◼ Kuyambira mwezi uno wa April, mabaji a msonkhano wachigawo wa 2000 a m’Chingelezi adzatumizidwa pamodzi ndi mabuku. Simudzafunikira kuchita kufunsira zimenezi. Mabaji adzaikidwa m’mipukutu ya mabaji 25, malinga ndi kukula kwa mpingo uliwonse. Ngati mipingo ikufuna mabaji owonjezereka, iyenera kufunsira pogwiritsa ntchito Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). N’kofunika kufunsira mapulasitiki oikamo mabaji kaamba ka aliyense amene akuwafuna mumpingo. Popeza mabaji amapangidwa kaamba ka msonkhano winawake pachaka, tikupempha abale ndi alongo athu kuti asamavale mabaji ameneŵa nthaŵi yamsonkhano itatha.
◼ Sosaite ili ndi mabaundi voliyumu a Watchtower a chaka cha 1951 mpaka 1955, 1987, 1995, ndi 1996, ndi Awake! a chaka cha 1987 ndi 1989. Wofalitsa aliyense kapena mipingo yatsopano imene ikuwafuna mabuku ameneŵa ingafunsire pakalipano kudzera mwa mtumiki wamabuku pampingo.
◼ The Watchtower Library—1999 Edition on CD-ROM tsopano ikupezeka mu zinenero 9. Chonde kumbukirani kuti zimenezi sizofunika kugaŵira aliyense, kuika mu laibulale ya sukulu, kapena kugaŵira awo amene akuonetsa chidwi chabe mwa Mboni za Yehova. Watchtower Library—1999 ndi yofunika anthu a mumpingo ndipo ingatumizidwe kokha kudzera mumpingo. Mpaka pamene makaseti amadisiki adzakhalapo ndi kutumizidwa, pakali pano adzaonekera ngati “Zoyembekezeredwa” pampambo wolongedzera mabuku a mipingo.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo—Chicheŵa
Insight on the Scriptures—Chingelezi
Munthu Wamkulu Woposa Wonse Amene Anakhalako—Chingelezi
Pay Attention to Daniel’s Prophecy—Chingelezi
Revelation—It’s Grand Climax at Hand!—Chingelezi
◼ Makaseti Atsopano Amene Alipo:
Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira (kaseti imodzi) —Chingelezi
◼ Kaseti Yatsopano ya Vidiyo imene ilipo:
Young People Ask—“How Can I Make Real Friends?”—Chingelezi (Kaseti ya vidiyo imeneyi yapangidwa kaamba ka Mboni zachinyamata pankhani yosankha mabwenzi abwino.)