Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/00 tsamba 5-6
  • Kubwereramo Kolemba M’sukulu Ya Utumiki Wateokalase

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereramo Kolemba M’sukulu Ya Utumiki Wateokalase
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 4/00 tsamba 5-6

Kubwereramo Kolemba M’sukulu Ya Utumiki Wateokalase

Kubwereramo kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa January 3 kufikira April 17, 2000. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.

[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso n’ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]

Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:

1. Nthaŵi zina tiyenera kuyembekezera kuti tilandire madalitso a Yehova, popeza Yehova amadziŵa mmene zinthu zilili kwa ife ndipo amatipatsa chosoŵa chilichonse panthaŵi imene chidzatithandiza kwambiri. (Sal. 145:16; Yak. 1:17) [w98-CN 1/1 tsa. 23 ndime 6]

2. Kukhalapo kokha kwa likasa la chipangano sikunatanthauze kuti Aisrayeli apeza chipambano. Madalitso a Yehova anadalira mkhalidwe wawo wauzimu komanso kumvera mokhulupirika kwa aja okhala ndi likasalo. (Yos., chap. 7) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani it-1, tsa. 167 ndime 2.]

3. Lerolino timachirikizika mwauzimu mwa kungoŵerenga mawu a Yehova. (Deut. 8:3) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w85 6/15 tsa. 17 ndime 15, 17.]

4. Mfundo yachikhalidwe yogogomezedwa m’Chilamulo cha Mose pa Deuteronomo 23:20 imasonyeza kuti ngati Mkristu afuna chiwongola dzanja pokongoza wina ndalama ndiye kuti alibe chikondi. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani it-1, tsa. 1212 ndime 5-6; it-2, tsa. 259 ndime 12; w86-CN 10/15 tsa. 21 ndime 9.]

5. Lipoti labwino la Yoswa ndi Kalebi linazikidwa pa chikhulupiriro cholimba ndi kutsimikiza mtima kwa Aisrayeli kogonjetsa zopinga zilizonse zowalepheretsa kulanda Dziko Lolonjezedwa. (Num. 13:30) [w98-CN 2/1 tsa. 5 ndime 4.]

6. Potchula “mphatsoyo” pa 1 Timoteo, Paulo anali kukumbutsa Timoteo za kudzozedwa kwake ndi mzimu woyera ndi mphotho ya kumwamba imene ankayembekeza. (1 Tim. 4:14) [w98-CN 2/15 tsa. 25 ndime 1]

7. “Zovumbuluka” zotchulidwa pa Deuteronomo 29:29 zinaphatikizapo chidziŵitso chonse cholembedwa m’Baibulo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 5/15 tsa. 31.]

8. Yehova anakonza kuti fuko la Yuda ‘liphunzitse Yakobo maweruzo a Mulungu ndi Israyeli chilamulo cha Mulungu.’ (Deut. 33:10) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 8/15 tsa. 11 ndime 7.]

9. Pempho la Gideoni, lofotokozedwa pa Oweruza 6:37-39, limasonyeza kuti anasamala mopambanitsa komanso amakayika. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 4/1 tsa. 30 ndime 6.]

10. Mwa kulangiza ophunzira ake ‘kusakupatira aliyense panjira kum’patsa moni,’ Yesu anali kugogomeza kufulumira kwa ntchito yolalikira komanso kufunika koika mtima wonse pa ntchito yofunika koposa imeneyi. (Luka 10:4, NW) [w98 3/1 tsa. 30 ndime 5]

Yankhani mafunso otsatiraŵa:

11. N’chifukwa chiyani mawu a Yehova afunika kukhala pamtima wa makolo? (Deut. 6:5, 6) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w98-CN 6/1 tsa. 20 ndime 4.]

12. Kodi mutu wa banja ungagwiritse ntchito motani mfundo yachikhalidwe yopezeka pa Deuteronomo 11:18, 19? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani fy-CN tsa. 70 ndime 14.]

13. Kodi ndi umboni wotani wa m’Malemba umene ulipo wakuti kapolo wothaŵayo Onesimo anali ndi mtumwi Paulo kwa kanthaŵi Paulo asanalembere Filemoni kalata? [w98-CN 1/15 tsa. 30 ndime 2]

14. Pamene tiona kupanda chilungamo kapena tachitidwa mosalungama, kodi tiyenera kuchitanji kuti tipeŵe kutaya mtima ndi chiyembekezo? [w98-CN 2/1 tsa. 6 ndime 2-3]

15. Kodi ndi motani mmene Chilamulo cha Mulungu ‘chikakhalira ngati chapamphumi pakati pa maso’ a Aisrayeli? (Deut. 6:8) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w73 tsa. 192.]

16. Kodi zochitika zofotokozedwa pa Yoswa 10:10-14 zikufanana motani ndi zomwe tingayembekeze pa Armagedo? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 12/15 tsa. 26 ndime 12-14.]

17. Tchulani mapindu atatu a kutamandidwa moona chifukwa cha khalidwe labwino. (Yerekezani ndi Miyambo 15:23.) [w98-CN 2/1 tsa. 31 ndime 5-6]

18. Mogwirizana ndi Yoswa 20:4, kodi munthu amathaŵira motani ku mudzi wopulumukirako wophiphiritsa? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 12/15 tsa. 27 ndime 16.]

19. Kodi Oweruza 5:31 amasonyeza motani kuti kugonjetsa magulu ankhondo amphamvu a Sisera kumene Woweruza Baraki anachita kumtsinje wa Kisoni kuli ndi tanthauzo lalikulu m’tsiku lathu? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 8/1 tsa. 21 ndime 4.]

20. Kodi tingasonyeze motani kuti timalemekeza mfundo yachikhalidwe yosonyezedwa m’mawu akuti “anaima yense m’mbuto mwake,” olembedwa pa Oweruza. 7:21? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w82 6/1 tsa. 25 ndime 17.]

Pezani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:

21. Kuti Yehova atidalitse mokwanira, tiyenera kupitiriza ․․․․․․․ ndi kupempha Yehova kutithandiza ․․․․․․․ ziphunzitso za Mawu ake ouziridwa. (1 Tim. 4:8, 9) [w98-CN 1/1 tsa. 24 ndime 6]

22. Kusyasyalika Yehova sakondwera nako ayi chifukwa ․․․․․․․ n’limene limam’sonkhezera munthu kutero, ․․․․․․․ komanso ․․․․․․․ , makamaka ․․․․․․․ . [w98-CN 2/1 tsa. 30 ndime 2-3]

23. Mutamaliza kuŵerenga Baibulo, ndi bwino kukhala ndi nthaŵi ․․․․․․․ ngati simukumvetsa mfundozo. [sg-CN tsa. 35 ndime 7]

24. Mogwirizana ndi fanizo la Yesu pa Mateyu 7:24-27, makolo anzeru angathandize ana awo kupirira mavuto onga chimphepo mwa kuwapatsa ․․․․․․․ zimene zidzawathandiza kukhalabe ․․․․․․․ . [w98-CN 2/15 tsa. 9 ndime 1]

25. ‘Kulandira chikole moyo wa munthu’ ndiko kulanda munthu ․․․․․․․ . (Deut. 24:6) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w84 7/15 tsa. 25.]

Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:

26. Kukonzekera kusiyira wina chuma chako ngati ungamwalire ili (nkhani ya mpingo; nkhani ya munthu mwini; Akristu oona afunikira kutero). (Agal. 6:5) [w98-CN 1/15 tsa. 19 ndime 6]

27. Paulo analimbikitsa Filemoni kulandira (Onamu; Onesiforo; Onesimo) ndi manja aŵiri koma sanagwiritse ntchito udindo wake monga mtumwi kum’lamula kuti atero kapena kuti am’masule. (Filem. 21) [w98-CN 1/15 tsa. 31 ndime 1]

28. Cholakwa chachikulu chimene chikusonyezedwa ndi nkhani ya akhate amene Yesu anachiritsa ndicho (kusoŵa chikhulupiriro; kusamvera; kusayamikira). (Luka 17:11-19) [w98-CN 2/15 tsa. 5 ndime 1]

29. Popeza kuti Mulungu anayanja zimene Rahabi anachita, mawu ake kwa amuna a m’Yeriko amene ankalondola azondi achiisrayeli amasonyeza kuti (kunama ndi nkhani ya munthu mwini; munthu alibe udindo wouza zinthu zoona kwa anthu amene sizikuwakhudza; anali asanasinthe njira zake zonse za dziko). (Yos. 2:3-5; yerekezani ndi Aroma 14:4.) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 12/15 tsa. 25 ndime 1.]

30. Malinga ndi zolembedwa pa Yohane 13:5, phunziro lachitsanzo limene Yesu anapereka limagogomeza mkhalidwe wa (chifundo; kulingalira ena; kudzichepetsa), kumene kumachititsa munthu kukonda kuchita ntchito zapansi pofuna kuthandiza ena. [w98-CN 3/15 tsa. 7 ndime 6]

Gwirizanitsani malemba otsatiraŵa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:

Deut. 7:3, 4; 17:7; 25:11, 12; 28:3; Yer. 15:20

31. Kulemekeza kwa Mlengi ziwalo zoberekera kuyenera kuthandiza Mkristu posankha njira yoyenera ya kulera. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w99-CN 6/15 tsa. 28 ndime 1-4.]

32. Tiyenera kukhala ndi chidaliro chakuti Yehova atichirikiza pochita ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. [w98-CN 3/1 tsa. 28 ndime 1]

33. Kulabadira chenjezo la Baibulo kumatithandiza kupeŵa zotsatira zoipa pamene Mkristu aloŵa m’goli ndi wosakhulupirira. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 11/1 tsa. 20 ndime 11.]

34. Kulandira madalitso a Mulungu sikudalira kumene tikukhala kapena kutumikira kapena ntchito imene tili nayo mu utumiki wa Mulungu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 6/15 tsa. 15 ndime 15.]

35. Monga umboni wa malangizo ake mu 1 Akorinto chaputala 5 onena za kuchotsa, Paulo akubwereza mawu a Chilamulo cha Yehova. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani si tsa. 213 ndime 24.]

S-97-CN #300 4/00

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena