Bokosi la Mafunso
◼ Kodi sitikupereka kaŵiri za mabuku ngati tiponya m’bokosi la ntchito ya Sosaite ya padziko lonse pamene tikutenga mabuku, kenako n’kudzaponyamonso zopereka zimene talandira m’munda?
Ayi. Zopereka zimene timaponya m’mabokosi a zopereka za ntchito ya Sosaite ya padziko lonse sikuti ndi za mabuku okha. Ofalitsa ndiponso anthu osonyeza chidwi chenicheni m’munda azilandira mabuku popanda kuwauza mtengo woikika. Zopereka zimene ofalitsa azipereka n’zoti zichirikize maofesi anthambi, nyumba za Beteli, sukulu za amishonale ndi zophunzitsa utumiki, amishonale, oyang’anira oyendayenda, malo otumizira mabuku, ndi ntchito zina zofunika pokwaniritsa ntchito yonse imene Yesu anapatsa ophunzira ake. Kufalitsa mabuku ndi mbali yochepa chabe ya ntchito imeneyi.
Choncho, pamene anthu osonyeza chidwi chenicheni m’munda apereka chopereka, tisawauze kuti zopereka zawo ndi “za mabuku.” Monga m’mene tikuwauzira, amene asonyeza chidwi chofuna kuŵerenga mabuku athu amalandira popanda mtengo woikika. Chopereka chilichonse chomwe angapereke chidzagwiritsidwa ntchito kulipirira zofunika pantchito yapadziko lonse. Chimodzimodzinso ndi zopereka za ofalitsa.