Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndani ayenera kulandira baji lamsonkhano wachigawo?
Mabaji amsonkhano amathandiza zedi kudziŵikitsa abale athu ndiponso kulengeza msonkhano. Komabe, sayenera kugaŵidwa mwachisawawa. Amadziŵikitsa wovalayo kukhala waunansi wabwino ndi mpingo wa Mboni za Yehova umene iye ali.
Khadili lili ndi malo olembapo dzina la munthu komanso dzina la mpingo. Choncho, munthuyo ayenera kukhala akusonkhana mokwanira ndi mpingo wotchulidwawo. Sosaite imatumiza chiŵerengero cha makadi ku mpingo uliwonse. Kukakhala koyenera kupereka khadi kwa ofalitsa aliyense wobatizidwa ndi wosabatizidwa. Komanso, ana ndiponso ena amene amapezeka pamisonkhano yampingo nthaŵi zonse ndiponso amene akupita patsogolo kuti aziloŵa muutumiki wakumunda, angalandire. Sikukakhala koyenera kupereka baji lamsonkhano kwa munthu wochotsedwa.
Makadi akabwera, akulu ayenera kuona kuti akugaŵa makadiwo mogwirizana ndi malangizoŵa.