Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 11/1 tsamba 24
  • Guinea Alandira Osonkhana pa “Mtendere wa Umulungu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Guinea Alandira Osonkhana pa “Mtendere wa Umulungu”
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Ntchito Yopanga Ophunzira Yakhudza Kwambiri Zochita Pamoyo Wanga
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Wa Nsanja ya Olonda
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova 2014
  • Ndimakhala Wosatekeseka Chifukwa Chodalira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 11/1 tsamba 24

Ripoti la Olengeza Ufumu

Guinea Alandira Osonkhana pa “Mtendere wa Umulungu”

MASIKU anayi oyambirira a 1987 anawona msonkhano wa chigawo woyamba wa Mboni za Yehova wochitidwa mu Republic la Guinea, West Africa. Ngakhale kuti Guinea mokulira liri dziko la Chisilamu kumene ntchito ya Mboni za Yehova sinazindikiridwebe mwalamulo, Mboni kumeneko zapeza ulemu monga anthu abwino, achifundo amtendere. Chinali chifukwa cha ulemu umenewu kuti boma linatsegula zitseko ku kulandira osonkhana pa “Mtendere wa Umulungu.”

Pakati pa nthumwizo panali amishonale asanu ndi anayi omwe anayenda kuchokera ku Freetown, Sierra Leone, mu galimoto ndi pa njinga zamoto ziŵiri. Pa malire, iwo anayenera kuoloka mtsinje pa chikepe chimene chinali ndi mabwato atatu okhala ndi matabwa ondandalikitsidwa mopingasa iwo. Pamene iwo anawoloka mwachisungiko ndi magalimoto, amishonalewo anafunsa: “Ndi ndalama zingati zimene tiyenera kupereka?” “Anthu inu ndinu Mboni za Yehova,” linali yankho. “Palibe malipiro.”

Bwanji ponena za akasitomu ndi za kutuluka m’dziko? “Musadere nkhaŵa za icho,” iwo anauzidwa. “Chirichonse chasamaliridwa kale. Tangovalani mabaji anu.” Mazana a nthumwi zina zinali kukumana ndi zokumana nazo zofananazo. Sikuti kokha boma la Guinea linavomereza kuwoloka kwaufulu pa mtsinje wolekanitsa Guinea ndi Sierra Leone ndi Liberia iwo anali ataletsa mchitidwe wa kasitomu ndi zotuluka kapena kulowa m’dziko kwa aliyense wokhala ndi baji la “Mtendere wa Umulungu”! Woyang’anira wadera mmodzi, yemwe anabwera kuchokera ku Liberia, ananena kuti: “Bajiyo inali yabwino koposa chiphaso chotulukira m’dziko.”

Boma la Guinea linali lothandiza m’njira zina. Iwo anapereka galimoto kuyendetsa Mboni kuchokera ku mzinda waukulu, wa Conakry, kupita ku mzinda wa msonkhano wa Guéckédou, pa mtunda woposa 640 km. Iwo anavomereza kugula kwa petulo kaamba ka magalimoto omwe anabwera kuchokera ku Freetown. Iwo anatsogoza hotela yapafupi ndi malo a msonkhano kusunga zipinda zawo zonse kaamba ka Mboni. Iwonso anachotsa kugwiritsira ntchito kwa holo ya m’mzindawo kaamba ka msonkhano, kupereka iyo kwaulere.

Mkulu wa boma, yemwe ali nduna ya pamwamba koposa m’mbali imeneyo ya dziko, anasunga nthumwi 11 panyumba yake. Iye analinso pakati pa 1,132 amene anamvetsera ku nkhani ya poyera pa Sande.

Yehova Mulungu sadzaiwala kukoma mtima kotero kosonyezedwa kwa atumiki ake.​—Mateyu 10:42; 25:40.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena