MBIRI YA MOYO WANGA
Ndimakhala Wosatekeseka Chifukwa Chodalira Yehova
ANTHU akandifunsa za moyo wanga ndimakonda kuwauza kuti, “Ndili ngati chikwama m’manja mwa Yehova.” Ndimatanthauza kuti mofanana ndi chikwama chimene ndimachitenga kulikonse kumene ndikufuna, ndimafunanso kuti Yehova ndi gulu lake azindigwiritsa ntchito mmene akufunira pa nthawi iliyonse. Ndavomerapo utumiki wovuta ndipo nthawi zinanso woopsa. Koma ndaphunzira kuti kukhulupirira Yehova ndi kumene kumathandiza kuti munthu azikhala mosatekeseka.
MMENE NDINAYAMBIRA KUDALIRA YEHOVA
Ndinabadwa mu 1948 m’mudzi wina waung’ono kum’mwera chakumadzulo m’dziko la Nigeria. Pa nthawiyo, bambo anga aang’ono dzina lawo a Moustapha anabatizidwa ndipo kenako nayenso mkulu wanga dzina lake Wahabi anabatizidwa. Ndili ndi zaka 9, bambo anga anamwalira ndipo ndinakhumudwa kwambiri. Wahabi anandiuza kuti ndidzawaonanso bambo anga akadzaukitsidwa. Mawu olimbikitsawa anachititsa kuti ndiyambe kuphunzira Baibulo. Ndinabatizidwa mu 1963. Azing’ono anga atatu nawonso anabatizidwa.
Mu 1965, ndinapita kumakakhala ndi mkulu wanga dzina lake Wilson mumzinda wa Lagos. Tinkasonkhana mumpingo wa Igbobi ndipo tinkasangalala kucheza ndi apainiya a mumpingowu. Nditaona mmene ankasangalalira komanso khama lawo, zinandilimbikitsa kuti inenso ndiyambe upainiya. Ndipo ndinauyamba mu January 1968.
M’bale Albert Olugbebi, yemwe ankatumikira ku Beteli, anakonza msonkhano wapadera kuti atilimbikitse achinyamatafe, ndipo anatiuza kuti kumpoto kwa Nigeria kunkafunika apainiya apadera. Ndimakumbukirabe mawu olimbikitsa omwe M’bale Olugbebi anatiuza kuti: “Mudakali achinyamata ndipo mukhoza kugwiritsa ntchito nthawi yanu komanso mphamvu zanu potumikira Yehova. Pali ntchito yambiri yomwe mungagwire.” Pofuna kutsanzira kudzipereka kwa mneneri Yesaya, ndinalemba fomu yofunsira utumikiwu.—Yes. 6:8.
Mu May 1968, ndinatumizidwa monga mpainiya wapadera mumzinda wa Kano kumpoto kwa dziko la Nigeria. Pa nthawiyi n’kuti kuderali kukuchitika nkhondo yapachiweniweni yomwe inayamba mu 1967 mpaka mu 1970 ndipo inachititsa kuti anthu ambiri aphedwe. Pasanapite nthawi, nkhondoyi inayamba kuchitikira kum’mawa kwa dzikoli. Chifukwa chondiganizira, m’bale wina anandiuza kuti ndisapite. Koma ine ndinamuuza kuti: “Zikomo chifukwa chondiganizira koma ngati Yehova akufuna kuti ndipite kumeneko sindikukayikira kuti akandithandiza.”
NDINKADALIRA YEHOVA KUDERA LIMENE KUNACHITIKA NKHONDO
Zinthu sizinali bwino ku Kano. Mzinda waukuluwu unali utawonongedwa kwambiri chifukwa cha nkhondo. Tikamalalikira, nthawi zina tinkapeza mitembo ya anthu amene anaphedwa. Ngakhale kuti ku Kano kunali mipingo yambiri, abale ambiri anali atathawa. Kunali kutangotsala ofalitsa osakwana 15 ndipo anali amantha komanso okhumudwa. Abale ndi alongo anasangalala kwambiri apainiya apadera 6 titafikako. Abale ndi alongowo anayamba kumva bwino titawalimbikitsa. Tinawalimbikitsa kuti ayambirenso kuchita zinthu zokhudza kulambira, kutumiza malipoti awo ku ofesi ya nthambi komanso kuitanitsa mabuku.
Kenako apainiya tonse tinayamba kuphunzira Chihausa. Anthu ambiri anayamba kumvetsera titayamba kuwalalikira m’chilankhulo chawo. Anthu a m’chipembedzo chomwe chinali chachikulu m’deralo sankasangalala ndi ntchito yathu yolalikira. Choncho tinkafunika kukhala osamala. Tsiku lina, ine ndi mnzanga yemwe ndinali naye tinathamangitsidwa ndi munthu wina atatenga mpeni. Mwamwayi tinathamanga kwambiri moti sanatipeze. Ngakhale kuti kunali koopsa, Yehova anatithandiza “kukhala otetezeka” ndipo chiwerengero cha ofalitsa chinayamba kuwonjezereka. (Sal. 4:8) Panopa ku Kano kuli ofalitsa oposa 500 m’mipingo 11.
TINKATSUTSIDWA KU NIGER
Ndikutumikira monga mpainiya wapadera ku Niamey ku Niger
Nditakhala ku Kano kwa miyezi yochepa, mu August 1968 ndinatumizidwa ku Niamey, lomwe ndi likulu la dziko la Niger limodzi ndi apainiya apadera ena awiri. Pasanapite nthawi yaitali tinazindikira kuti ku Niger, ku West Africa, ndi limodzi mwa mayiko otentha kwambiri padziko lonse. Tinkafunika kupirira kutentha, komanso kuphunzira Chifulenchi chomwe ndi chilankhulo chachikulu m’dzikolo. Ngakhale kuti panali mavuto onsewa, tinkakhulupirira Yehova. Ndipo tinayamba kulalikira mumzindawo limodzi ndi ofalitsa ochepa omwe ankakhala kumeneko. Pasanapite nthawi yaitali, pafupifupi munthu aliyense amene ankadziwa kuwerenga mumzinda wa Niamey anali atalandira buku lomwe tinkagwiritsa ntchito pophunzitsa anthu Baibulo lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Anthu ankachita kutifunafuna kuti apeze bukuli.
Pasanapite nthawi, tinazindikira kuti akuluakulu a boma sankasangalala ndi a Mboni za Yehova. Mu July 1969, tinachita msonkhano wadera woyamba m’dzikolo ndipo panali anthu pafupifupi 20. Panali ofalitsa awiri oti abatizidwe pamsonkhanowu. Koma pa tsiku loyamba panabwera apolisi ndipo anaimitsa msonkhanowo. Anatenga apainiya apadera komanso woyang’anira dera n’kupita nawo kupolisi. Titafika, iwo anatifunsa mafunso ndipo anatiuza kuti tidzapitenso tsiku lotsatira. Titaona kuti zinthu zikhoza kufika poipa, tinakonza zoti nkhani ya ubatizo ikambidwe m’nyumba ya m’bale kenako tinapita kumtsinje mwachinsinsi kukabatiza anthu awiri aja.
Patapita milungu yochepa, akuluakulu a mu unduna woona za anthu olowa ndi kutuluka m’dzikolo anauza ine ndi apainiya apadera ena 5 aja kuti tituluke m’dzikolo. Anatiuza kuti tichoke m’dzikolo pasanapite maola 48, komanso tinkafunika kukonza tokha mayendedwe. Tinamvera ndipo tinapita ku ofesi ya nthambi ya ku Nigeria komwe tinakapatsidwa mautumiki ena.
Ine ananditumiza kumudzi wina ku Nigeria wotchedwa Orisunbare. Ndinkasangalala kugwira ntchito yolalikira ndi ofalitsa ochepa omwe anali kumeneko. Patangopita miyezi 6, ofesi ya nthambi inandiuza ine ndekha kuti ndipitenso ku Niger. Poyamba ndinadabwa ndipo ndinkachita mantha koma kenako ndinkafunitsitsa kuti ndikakumanenso ndi abale ku Niger.
Ndinabwereranso ku Niamey. Tsiku lotsatira, munthu wina wa bizinesi wa ku Nigeria anazindikira kuti ndine wa Mboni ndipo anayamba kufunsa mafunso okhudza Baibulo. Ndinayamba kuphunzira naye Baibulo ndipo atasiya kusuta komanso kumwa mowa kwambiri anabatizidwa. Kenako ndinasangalala kuthandiza nawo pa ntchito yolalikira m’madera osiyanasiyana a ku Niger, komwe chiwerengero cha ofalitsa chinkakwera pang’onopang’ono. Pamene ndinkafika kunali a Mboni 31 ndipo pamene ndinkachoka analiko 69.
“SITIKUDZIWA MMENE NTCHITO YOLALIKIRA IKUYENDERA KU GUINEA”
Cha kumapeto kwa 1977, ndinabwerera ku Nigeria kuti ndikalandire maphunziro. Titamaliza maphunzirowo, omwe anali a milungu itatu, M’bale Malcolm Vigo yemwe anali wogwirizanitsa Komiti ya Nthambi, anandipempha kuti ndiwerenge kalata yochokera ku ofesi ya nthambi ya Sierra Leone. Abale kumeneko ankafuna m’bale wathanzi, wosakwatira komanso yemwe amatha kulankhula Chingelezi ndi Chifulenchi kuti akakhale woyang’anira dera ku Guinea. M’bale Vigo anandiuza kuti ndikuphunzitsidwa kuti ndikachite utumiki umenewu. Iye anatsindika kuti utumikiwu si wophweka. Ndiye anandilangiza kuti, “Uiganizire kaye nkhaniyi usanavomere.” Mwamsanga ndinayankha kuti, “Popeza ndi Yehova amene akunditumiza, ndipita.”
Ndinakwera ndege kupita ku Sierra Leone ndipo ndinakakumana ndi abale a ku ofesi ya nthambi. M’bale wina wa m’Komiti ya Nthambi anandiuza kuti, “Sitikudziwa mmene ntchito yolalikira ikuyendera ku Guinea.” Ngakhale kuti ofesi ya nthambiyi ndi imene imayang’anira ntchito yolalikira ku Guinea, sankatha kulumikizana ndi ofalitsa kumeneko chifukwa cha mavuto a zandale omwe anali kumeneko. Iwo anali atayesa maulendo angapo koma zinali zovuta kutumizako anthu. Choncho anandipempha kuti ndipite kulikulu la dzikolo ku Conakry kuti ndikapemphe chilolezo chokhala m’dzikolo.
“Popeza ndi Yehova amene akunditumiza, ndipita”
Nditafika ku Conakry ndinapita ku ofesi ya kazembe wa dziko la Nigeria. Ndinauza kazembeyo kuti ndikufuna kudzalalikira ku Guinea. Iye anandiuza kuti ndisakhale kumeneko chifukwa mwina ndikhoza kumangidwa kapena zinthu zina zoipa zikhoza kundichitikira. Anandiuza kuti, “Ubwerere ku Nigeria uzikalalikira kumeneko,” koma ine ndinayankha kuti, “Ndikufunitsitsa kukhala kuno.” Choncho Kazembeyo analembera kalata nduna yoona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko la Guinea ndipo ndunayo inandilandira bwino.
Kenako ndinabwerera ku nthambi ya ku Sierra Leone kukafotokozera abale zimene nduna ija inanena. Abalewo anasangalala kwambiri atamva mmene Yehova anandidalitsira pa ulendowu. Ndinali nditapatsidwa ufulu wokhala m’dziko la Guinea.
Ndili woyang’anira dera ku Sierra Leone
Mu 1978 mpaka mu 1989, ndinatumikira monga woyang’anira dera ku Guinea ndi Sierra Leone komanso monga woyang’anira dera wogwirizira ku Liberia. Poyamba ndinkadwaladwala, ndipo nthawi zina zimenezi zinkachitika ndili kumadera akutali. Koma abale ankayesetsa kunditengera kuchipatala.
Pa nthawi ina ndinadwala malungo aakulu komanso njoka zam’mimba. Nditachira ndinamva kuti abale ankakambirana za kumene angakandiike ndikamwalira. Ngakhale kuti ndinkakumana ndi zoopsa zotere, sindinaganizepo zosiya utumiki wanga. Ndimakhulupirirabe kuti chitetezo chenicheni chimachokera kwa Mulungu yemwe angatiukitse ngati titamwalira.
KUDALIRA YEHOVA LIMODZI NDI MKAZI WANGA
Pa tsiku la ukwati wathu mu 1988
Mu 1988, ndinakumana ndi Dorcas yemwe ankachita upainiya, ndipo anali wodzichepetsa komanso ankakonda Yehova. Tinakwatirana ndipo tinkachita limodzi utumiki woyang’anira dera. Dorcas ndi mkazi wachikondi komanso wodzipereka. Nthawi zina tinkayenda wapansi maulendo aatali mwina makilomita 25 kuchoka mpingo wina kupita mpingo wina titanyamula katundu. Tikamapita kumipingo yakutali kwambiri, tinkakwera magalimoto n’kumayenda m’misewu yamatope komanso maenje.
Dorcas ndi wolimba mtima kwambiri. Mwachitsanzo, nthawi zina tinkawoloka mitsinje yokhala ndi ng’ona. Pa nthawi ina tinali pa ulendo womwe tinayenda masiku 5 ndipo pamlatho wina matabwa anali atawonongeka. Choncho tinawoloka mtsinjewo pogwiritsa ntchito bwato. Dorcas ataimirira kuti atsike m’bwatomo, anagwera m’madzi omwe anali akuya. Tonse sitinkadziwa kusambira ndipo mumtsinjemo munali ng’ona. Mwamwayi anyamata ena analowa m’madzimo ndi kumupulumutsa. Kwa masiku angapo tonse tinkalephera kugona tikaganizira zomwe zinachitikazo komabe tinapitiriza utumiki wathu.
Ana athu, Jahgift ndi Eric, ndi mphatsodi zochokera kwa Yehova
Cha kumayambiriro kwa 1992, tinadabwa kwambiri titazindikira kuti Dorcas ndi woyembekezera. Tinkaganiza kuti utumiki wathu wathera pamenepo. Tinadziuza kuti, “Yehova watipatsa mphatso.” Kenako tinapatsa mwana wathu wamkaziyo dzina lakuti Jahgift. Patapita zaka 4 kuchokera pamene anabadwa, tinakhalanso ndi mwana wina dzina lake Eric. Timaona kuti ana athu onsewa ndi mphatsodi zochokera kwa Yehova. Jahgift anatumikira kwa kanthawi ku ofesi yomasulira mabuku ku Conakry, ndipo Eric ndi mtumiki wothandiza.
Ngakhale kuti pa nthawiyo Dorcas anasiya kuchita upainiya wapadera, ankapitirizabe kuchita upainiya wokhazikika uku akulera ana athu. Yehova anandithandiza kuti ndipitirizebe kuchita utumiki wanthawi zonse. Ana athu atakula, Dorcas anayambiranso kuchita upainiya wapadera. Panopa tikutumikira monga amishonale ku Conakry.
YEHOVA NDI AMENE AMATITETEZA
Nthawi zonse ndakhala ndikupita kulikonse komwe Yehova ankanditumiza. Nthawi zambiri takhala tikuona iye akuteteza komanso kutidalitsa. Kukhulupirira Yehova kwatiteteza ku mavuto ambiri omwe amasautsa anthu omwe amadalira chuma. Ine ndi Dorcas tadzionera tokha kuti chitetezo chenicheni chimachokera kwa Yehova, yemwe ndi “Mulungu wachipulumutso chathu.” (1 Mbiri 16:35) Sindimakayikira kuti anthu omwe amamudalira, iye ‘amakulunga moyo wawo m’phukusi la moyo kuti utetezeke.’—1 Sam. 25:29.