Kodi Mumayamikira Kuleza Mtima kwa Yehova?
1 Chikhala kuti Yehova sanaleze mtima zaka 10, 20, kapena zaka zambiri zapitazo n’cholinga chakuti ntchito yochitira umboni ipitirire, kodi inu mukanaphunzira choonadi? Si mmene timasangalalira kuona kuti walola anthu ambiri ‘kufika kukulapa.’ Komabe, tsiku lalikulu la Yehova la Chiweruzo “lidzadza ngati mbala.” (2 Pet. 3:9, 10) Chotero, sitiyenera kuona kuleza mtima kwa Mulungu monga kuchedwa kubweretsa mapeto a dongosolo la zinthu lino.—Hab. 2:3.
2 Amvereni Anthu Chisoni: Kuleza mtima kwa Yehova n’kwakukulu koti sitingakumvetsetse. Sitiyenera kuiŵala cholinga chake. (Yona 4:1-4, 11) Yehova amaona khalidwe lomvetsa chisoni la anthu ndipo amawamvera chifundo. Yesu amamvanso chimodzimodzi. Popeza ankawamvera chisoni makamu a anthu omwe ankawalalikira, anafuna kuti ntchito yolalikira ipitirire kotero kuti anthu ambiri akhale ndi mwayi wopeza moyo wosatha.—Mat. 9:35-38.
3 Kukagwa mavuto ndi masoka, kodi sitiwamvera chisoni anthu amene sadziŵa choonadi? Lerolino anthu ali ngati “nkhosa zopanda mbusa” chifukwa amayesetsa kupirira ndi kufunafuna tanthauzo la chipwirikiti chimene chili m’dziko. (Marko 6:34) Mwa kulalikira uthenga wabwino timatonthoza anthu a mitima yabwino ndipo timasonyeza kuyamikira kwathu kuleza mtima kwa Yehova.—Mac. 13:48.
4 Ntchito Yathu ndi Yamwamsanga: Chaka chatha anthu 323,439 anabatizidwa ndipo anthu oposa 14,000,000 anafika pa Chikumbutso. N’chizindikirotu chakuti anthu ambiri akhoza kupulumuka chiwonongeko cha dongosolo loipa lilipoli! Sitikudziŵa kuti “khamu lalikulu” lidzakhala lalikulu motani. (Chiv. 7:9) Sitikudziŵa kuti ntchito yathu yolalikira idzatha liti. Koma Yehova akudziŵa. Uthenga wabwino udzalalikidwa mpaka iye atakhutira, “ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mat. 24:14.
5 Nthaŵi yomwe yatsala yafupikitsidwa, ndipo tsiku la Mulungu lili pafupi kudza. (1 Akor. 7:29a; Aheb. 10:37) Mosakayikira konse, “chipulumutso chathu chili pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupira.” (Aroma 13:11) Tiyeni tisaiŵale cholinga cha kuleza mtima kwa Mulungu. M’malomwake, tiyeni tilalikire mwachangu kuti anthu ambiri amene amafuna chilungamo aone chifundo chachikulu cha Yehova.