Kuleza Mtima N’kofunika Kwambiri pa Utumiki Wathu
1. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti ndi woleza mtima?
1 Mulungu amatilezera mtima kwambiri anthufe. (Eks. 34:6; Sal. 106:41-45; 2 Pet. 3:9) Chitsanzo chimodzi chodziwika bwino chosonyeza kuti iye ndi woleza mtima, chimaonekera pa ntchito yolalikira za Ufumu imene ikuchitika padziko lonse. Yehova wakhala akuchita zinthu ndi anthu kwa zaka pafupifupi 2,000, komabe akupitiriza kukoka anthu amene akufuna kukhala naye pa ubwenzi. (Yoh. 6:44) Kodi ifeyo tingatsanzire bwanji kuleza mtima kwa Yehova pochita utumiki wathu?
2. Kodi tingasonyeze bwanji kuleza mtima polalikira m’gawo lathu?
2 Utumiki wa Kunyumba ndi Nyumba: Timatsanzira kuleza mtima kwa Yehova ‘popitiriza’ kulalikira m’gawo limene anthu sanayambe kuchita chidwi ndi uthenga wathu. (Mac. 5:42) Timasonyeza kuleza mtima tikamapirira anthu akamatisala, kutinyoza ndi kuletsa ntchito yathu. (Maliko 13:12, 13) Timasonyezanso kuleza mtima poyesetsa kuthirira mbewu za choonadi m’mitima ya anthu ngakhale amene sapezekapezeka pakhomo.
3. N’chifukwa chiyani kuleza mtima kuli kofunika pochita maulendo obwereza ndi pochititsa maphunziro a Baibulo?
3 Maphunziro a Baibulo: Tikadzala mbewu, timayembekezera modekha kuti zikule. Tikhoza kuzisamalira kuti zikule bwino koma sitingazifulumizitse kuti zikule msanga. (Yak. 5:7) Mofanana ndi mbewu, kukula mwauzimu kumachitika pang’onopang’ono komanso pa nthawi yake. (Maliko 4:28) Anthu amene tikuphunzira nawo Baibulo angamavutike kuti asiye zikhulupiriro za chipembedzo chonyenga kapena miyambo yosagwirizana ndi Malemba. Choncho tisakakamize anthu kuti asinthe msangamsanga moyo wawo. M’pofunika kuleza mtima kuti mzimu wa Mulungu ugwire ntchito mokwanira mumtima mwa wophunzirayo.—1 Akor. 3:6, 7.
4. Kodi kuleza mtima kungatithandize bwanji kuti tizilalikira mogwira mtima kwa achibale athu omwe si Mboni?
4 Achibale Amene si Mboni: Timafunitsitsa kuti achibale athu omwe si Mboni aphunzire choonadi. Komabe, tifunika kuyembekezera mpaka nthawi yoyenera yoti tiwafotokozere za chikhulupiriro chathu itakwana. Komanso tifunikira kupewa kuwauza zinthu zambirimbiri nthawi imodzi. (Mlal. 3:1, 7) Pa nthawi yonseyi, khalidwe lathu labwino limaonetsa mmene choonadi chatithandizira. Tifunikanso kukhala okonzeka kufotokoza chikhulupiriro chathu mofatsa ndi mwaulemu kwambiri. (1 Pet. 3:1, 15) Tikamachita utumiki wathu moleza mtima, utumikiwo udzakhala waphindu kwambiri, ndiponso Atate wathu wakumwamba adzasangalala nawo.