Ndandanda ya Mlungu wa June 13
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 13
Nyimbo Na. 40 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 8 ndime 10-17 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 38-44 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 41:1– 42:5 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Zimene Tingaphunzire kwa Anthu Ogwirizana Kwambiri Otchulidwa M’Baibulo Ndiponso pa Makhalidwe Awo (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Maulosi Onena za Kubwezeretsedwa kwa Aisiraeli Akukwaniritsidwa kwa Ndani Masiku Ano?—rs tsa. 46 ndime 3 mpaka tsa. 47 ndime 2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino: Kuchititsa Maphunziro a Baibulo a Panyumba. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Gulu, tsamba 98 ndime 1 mpaka tsamba 99 ndime 1. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene amasangalalira chifukwa chophunzitsa munthu choonadi ndiponso kumuona akupita patsogolo mwauzimu. Mungapempheretu munthu mmodzi kapena awiri kuti adzayankhepo.
Mph. 10: Kodi Malamulo Achikhristu pa Nkhani ya Kukwatira, Kuthetsa Banja ndi Kupatukana ndi Otani? Nkhani yokambidwa ndi mkulu yochokera m’buku la Gulu, tsamba 194 mpaka 195, funso 1 mpaka 3.
Mph. 10: “Kuleza Mtima N’kofunika Kwambiri pa Utumiki Wathu.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero