Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/00 tsamba 2
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 11/00 tsamba 2

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu November: Tidzapitiriza kugaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36. Mipingo imene yamaliza gawo lawo mwa kufikira anthu okhala m’nyumba iliyonse ndi kope la Uthenga wa Ufumu Na. 36 ingagaŵire bulosha la Mulungu Amafunanji kapena buku la Chidziŵitso. December: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. January: Buku lililonse lakale la masamba 192 lofalitsidwa mu 1986 kapena m’mbuyomo limene mpingo ungakhale nalo m’sitoko. Mipingo imene ili ndi buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja ingaligaŵirenso. February: Bulosha la Mulungu Amafunanji, kapena buku lililonse la masamba 192 limene mpingo ungakhale nalo m’sitoko.

◼ Ndawala ya Uthenga wa Ufumu ikadzatha, mipingo imene idzakhalebe ndi mtokoma wa Uthenga wa Ufumu Na. 36 idzalimbikitse ofalitsa kugaŵira wotsalawo monga momwe timagaŵira mathirakiti—kaya kukhomo ndi khomo kapena kwina kulikonse. Ngati kuli kololeka, ofalitsa angamasiye kope limodzi pakhomo limene sanapezepo anthu, akumaonetsetsa kuti anthu odutsa m’njira sangalione. Ayenera kuyesetsa kugaŵira makope onse otsala a uthenga wofunika umenewu.

◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye angam’pemphe aŵerengere maakaunti a mpingo pa December 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Zikachitika zimenezi, lengezani ku mpingo pambuyo polengeza lipoti la maakaunti lotsatirapo.

◼ Mipingo iyenera kuyamba kufunsira Yearbook of Jehovah’s Witnesses ya 2001 pofunsira mabuku a November. Yearbook imeneyi idzakhala m’Chingelezi. Kufikira Yearbook itabwera ndi kutumizidwa, idzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mndandanda wolongedzera katundu. Ma Yearbook ndi zinthu zofunsira mwapadera.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena