Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/00 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira November 13
  • Mlungu Woyambira November 20
  • Mlungu Woyambira November 27
  • Mlungu Woyambira December 4
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 11/00 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira November 13

Nyimbo Na. 4

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.

Mph. 13: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokamba mkulu.

Mph. 22: “Limbikitsani Chidwi Chokopedwa ndi Uthenga wa Ufumu Na. 36.” Kukambirana ndime 1-5 mwa mafunso ndi mayankho. Longosolani makonzedwe apampingo okafola gawo lililonse limene silinafoledwe. Kambiranani maulaliki operekedwa m’ndime 7 ndi 8 za maulendo obwereza, ndipo chitani chitsanzo cha ulaliki uliwonse. Gogomezani kufunika kobwereranso kwa onse amene anasonyeza chidwi ndi kuyesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Malizani mwa kukambirana ndime 9 ndi malemba operekedwawo.

Nyimbo Na. 63 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 20

Nyimbo Na. 111

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 15: Zokumana Nazo Pogaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36. Fotokozani mmene kufola gawo kunaliri kopambana. Kodi alipo amene analoŵa mu utumiki kwa nthaŵi yoyamba? Simbani mawu olimbikitsa onenedwa ndi eninyumba. Kodi ofalitsa ena anatha kuyambitsa maphunziro a Baibulo? Ngati anatero, apempheni kuti afotokoze kapena achitire chitsanzo mmene anachitira. Kumbutsani onse kuti akalimbikitse chidwi chimene anachipeza.

Mph. 20: “Lalikiranibe!” Nkhani ndi kufunsa wofalitsa. Ena akhala m’gulu la Yehova moyo wawo wonse ndipo alimbikirabe m’ntchito yolalikira. Poona zinthu ndi maganizo abwino, apeza chisangalalo mwa kutero. (Onani buku la Chidziŵitso, tsamba 179, ndime 20, ndi Nsanja ya Olonda ya May 1, 1992, masamba 21-2, ndime 14-15.) Pemphani wofalitsa amene wakhala wokangalika kwa zaka zambiri kuti afotokoze zifukwa zimene wakhalira wolimbikira m’ntchito yolalikira.

Nyimbo Na. 141 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 27

Nyimbo Na. 153

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti a utumiki wa November. Buku logaŵira mu December ndi la Chidziŵitso. Fotokozani mbali yaikulu imene Mboni za Yehova zachita potulutsa Baibulo m’zinenero zambiri.—Onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1997, masamba 11-12.

Mph. 20: Gwiritsani Ntchito Kwambiri Buku la Kukambitsirana. Kukambirana masamba 7-8 mwa mafunso ndi mayankho. Sonyezani mmene bukuli linakonzedwera kutithandiza kukonzekera ulaliki wogwira mtima kwambiri. Onetsani mmene tingapezere mfundo zothandiza kuyankha funso. Limbikitsani onse kulidziŵa bwino kwambiri buku limeneli, azilisungira m’chola chawo cha mu umboni, ndipo aziligwiritsa ntchito nthaŵi zonse.

Mph. 15: “Kuthandiza Ana Athu Kukhalabe m’Choonadi—Mbali Yachitatu: Mwa Phunziro la Baibulo la Banja Lokhazikika.” Kambiranani nkhaniyi mwa mafunso ndi mayankho. Nkhani ya mkulu.

Nyimbo Na. 175 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira December 4

Nyimbo Na. 189

Mph. 10: Zilengezo za pampingo.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: “Mawu Oyenera a pa Nthaŵi Yake.” Kukambirana koloŵetsamo omvetsera ndi zitsanzo. Ambiri amadziona kukhala osadziŵa kuyambitsa bwino makambirano, akumalingalira molakwa kuti ayenera kukhala ndi luso lapadera kuti aphulepo kanthu. Fotokozani mmene tonsefe, kuphatikizapo ofalitsa atsopano ndi aang’ono, tingayambitsire makambirano mwa kungoikirapo khama basi. Longosolani maulaliki osonyezedwawo, mukumagogomeza kusavuta kwake, ndipo funsani ofalitsa aŵiri kapena atatu kuti aonetse zitsanzo zake. Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 1998, tsamba 8, kuti muone maulaliki ena amene angagwiritsidwe ntchito. Limbikitsani onse kukhala ndi maganizo olimbikitsa kuti akhale ndi chisangalalo chokulirapo mu utumiki wawo.

Nyimbo Na. 218 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena