Nyimbo 218
Ndi Kristu m’Paradaiso
1. Kristu ananena naye
‘Udzakhala m’paradaiso.’
Lonjezoli kwa wochimwa
Latisonkhezera
Chikhulupiliro.
Lipatsa chiyembekezo,
Mulungu achotsa imfa.
Chowonadicho tidziŵa.
Chiyanjo tipeza
Mu Baibulolo.
2. Khamu lalikulukulu
Lasunga chiyembekezo.
Silikhalanso mumantha.
Mawu a Mulu
ngu Amvekera bwino.
Tipempha modzichepetsa,
Timchitire utumiki
Ndi kumtamanda kosatha,
Mokhulupirika
Ndi chikondwerero.
3. “Nkhosa zina” zopambana
Zidzakhala m’paradaiso.
Izinso zizindikira
Ntchito za Mulungu!
Zochoka kwa iye.
Zilalikira Mbiriyo
Ndikusangalatsa anthu.
Njirayidi ndi ya nzeru;
Akhale ndi moyo
Mu paradaiso.