Nyimbo 63
Lolani Kuunika Kuŵale
1. M’lungu walamula
Kuti kuŵale
Akuchotsa mdima
wakale lomwe.
Kukachisi wake
Mphezi ziŵala,
Tikatsogozedwe
Ndi kuŵalako.
2. Mbiri ya Ufumu
Tilalikira
Kutonthoza onse
Akulirawo.
Mphamvu yofalitsa
Nja kwa Mulungu.
Ativumbulira
Za ntchito yathu.
3. Tithandizireni
Muutumiki,
Kutitu tisunge
Umphumphu wathu.
Ife anthu anu,
Mosangalala
Tidzalemekeza
Dzina loyera.