“Onetsani Kuwala Kwanu”
1. Kodi tili ndi mwayi wochita chiyani?
1 Kuwala kumene timaona kuyambira m’bandakucha mpaka madzulo, kumachititsa kutamanda Yehova Mulungu. Yesu anauza ophunzira ake kuti aonetse kuwala kwa mtundu wina, “kuwala kwa moyo.” (Yoh. 8:12) Kuonetsa kuwala kwauzimu kumeneku ndi mwayi wapadera kwambiri ndipo sitiyenera kukuona mopepuka. Yesu anati: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu.” Kuchita zimenezi kumathandiza anthu ena. (Mat. 5:16) Masiku ano, anthu ambiri ali mumdima wauzimu wandiweyani ndipo akufunikira kwambiri kuwala. Kodi tingatani kuti tionetse kuwala kwathu ngati mmene Khristu anachitira?
2. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ntchito yoonetsa anthu kuwala kwauzimu ndi yofunika kwambiri?
2 Polalikira: Yesu anagwiritsa ntchito nthawi yake, mphamvu zake ndi zinthu zake zina, pothandiza anthu kuti aone kuwala kwa choonadi. Iye ankalalikira anthu kulikonse monga kunyumba zawo, m’misika ndi m’mapiri. Ankadziwa kuti kuwala kwauzimu n’kothandiza kwambiri. (Yoh. 12:46) Pofuna kuthandiza anthu ambiri, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti akhale “kuwala kwa dziko.” (Mat. 5:14) Ophunzirawo anaonetsa kuwala kwawo pochitira zabwino anthu ena ndiponso polalikira choonadi.
3. Kodi tingasonyeze bwanji kuti kuwala kwa choonadi n’kofunika kwambiri?
3 Anthu a Mulungu sapeputsa udindo wawo ‘woyendabe ngati ana a kuwala.’ (Aef. 5:8) Iwo amalalikira kulikonse kumene kungapezeke anthu. Kungowerenga Baibulo kapena mabuku ena ofotokoza Baibulo pamalo oonekera, kungachititse kuti tiyambe kukambirana mfundo za m’Malemba ndi anthu. Tingachite zimenezi pa nthawi yopuma kuntchito kapena kusukulu. Mtsikana wina wamng’ono anachita zimenezi kusukulu, moti anayambitsa phunziro la Baibulo ndiponso anagawira mabuku kwa anzake 12 a m’kalasi mwake.
4. N’chifukwa chiyani khalidwe labwino lili lofunika kuti ‘tionetse kuwala kwathu’?
4 Pochita Zabwino: Kuti kuwala kwathu kuonekere, zimadaliranso khalidwe lathu. (Aef. 5:9) Tikakhala kuntchito, kusukulu ndi kumalo ena, makhalidwe athu achikhristu amatisiyanitsa ndi anthu ena ndipo zimenezi zimatipatsa mwayi wouza ena choonadi cha m’Baibulo. (1 Pet. 2:12) Mwachitsanzo, kamnyamata kena kazaka zisanu kanali ndi khalidwe labwino kwambiri. Choncho, aphunzitsi ake ataona khalidweli anaitanitsa makolo a mwanayo. Aphunzitsiwo anati: “Sindinaonepo mwana wamakhalidwe abwino ngati ameneyu.” Izi zikusonyeza kuti utumiki umene timachita komanso khalidwe lathu labwino, zimakopa anthu kuti aone “kuwala kwa moyo” n’kuyamba kutamanda Mulungu wathu.