Kuŵalitsa Kuunika Kwathu Mopitiriza
1 Kodi kuunika nchiyani? Dikishonale ina imakufotokoza kukhala “kanthu kena kamene kamachititsa chinthu kuoneka.” Koma kunena zoona, ngakhale kuti anthu apita patsogolo m’luso la zopangapanga, iwo samadziŵa mokwanira yankho la funso limene Yehova anapereka lolembedwa pa Yobu 38:24. Kodi tingachite zinthu popanda kuunika? Popanda kuunika sitingakhale ndi moyo. Kuunika nkofunika kaamba ka maso athu enieni, ndipo Baibulo limatiuza kuti m’lingaliro lauzimu, “Mulungu ndiye kuunika.” (1 Yoh. 1:5) Ife timadalira kotheratu pa Uyo amene ‘amatiunikira.’—Sal. 118:27.
2 Zimenezi nzoona m’lingaliro laumunthu komanso nzoona kwambiri m’njira yauzimu. Chipembedzo chonyenga chasocheretsa namtindi wa anthu, chikumawaika mumdima wauzimu, ‘akumayambasira khoma ngati akhungu.’ (Yes. 59:9, 10) Posonkhezeredwa ndi chikondi chake chachikulu ndi chifundo, Yehova ‘amatumiza kuunika kwake ndi choonadi.’ (Sal. 43:3) Mamiliyoni enieni a anthu oyamikira alabadira, akumatuluka ‘mumdima, kuloŵa kuunika kwake kodabwitsa.’—1 Pet. 2:9.
3 Yesu Kristu amachita mbali yofunika pa kuloŵetsa kuunika m’dziko. Iye anati: “Ndadza ine kuunika ku dziko lapansi, kuti yense wokhulupirira ine asakhale mumdima.” (Yoh. 12:46) Nthaŵi yake yonse, nyonga, ndi maluso zinaikidwa pa kupangitsa kuunika kwa choonadi kudziŵika. Anayendayenda m’dziko lonse lakwawo, akumalalikira ndi kuphunzitsa pafupifupi mumzinda uliwonse ndi mudzi. Anapirira chizunzo chosalekeza chochokera kumbali zonse, koma iyeyo anachirimikabe pantchito yake ya kuwanditsa kuunika kwa choonadi.
4 Yesu anasumika maganizo pa kusankha, kuphunzitsa, ndi kulinganiza ophunzira, ndi cholinga china chapadera. Pa Mateyu 5:14-16 timaŵerenga za malangizo ake kwa iwo kuti: “Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. . . . Chomwecho muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wakumwamba.” Monga momwe Yesu anachitira, iwo anafunikira kukhala “mauniko m’dziko lapansi,” akumaŵalitsa kuunika kwa choonadi konsekonse. (Afil. 2:15) Analandira mokondwera thayo limenelo, akumaliona kukhala chifuno chawo chachikulu m’moyo. Patapita nthaŵi yaifupi, Paulo anatha kunena kuti uthenga wabwino ‘unalalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’ (Akol. 1:23) Mpingo wonse Wachikristu unali wogwirizana m’kuchita ntchito yaikulu imeneyo.
5 Ife lerolino tiyenera kukhala othokoza kuti tafikira kukhala pakati pa awo amene ‘avula ntchito za mdima.’ (Aroma 13:12, 13) Tingasonyeze chiyamikiro chathu mwa kutsanzira chitsanzo choperekedwa ndi Yesu ndi Akristu okhulupirika akale. Kufunika kwakuti ena amve choonadi nkofulumira kwambiri ndiponso kuli nkhani yaikulu tsopano kuposa nthaŵi ina iliyonse m’mbiri ya anthu. Palibe ntchito ina imene tingaiyerekezere ndi ntchito imeneyi pa kufulumira kwake ndi mapindu ake aakulu.
6 Kodi Tingaŵale Motani Monga Mauniko? Njira yaikulu yoŵalitsira kuunika kwathu ndiyo ya kukhala ndi phande mu ntchito yolalikira Ufumu. Mpingo uliwonse uli ndi makonzedwe olinganizidwa okhazikika kaamba ka kulalikira mu gawo lake. Mitokoma yaikulu ya mabuku osiyanasiyana imatumizidwa m’zinenero zambiri. Maphunziro ambiri amaperekedwa m’misonkhano, ndipo thandizo la kuphunzitsa ena mwaumwini limaperekedwa ndi awo amene ali okhoza. Mipata ya kukhalamo ndi phande njotseguka kwa amuna, akazi, achikulire, ndipo ngakhale ana. Munthu aliyense mumpingo amapemphedwa kukhala ndi phande malinga ndi kukhoza kwake ndi mmene mikhalidwe yake ingamlolere. Zochitika zonse za mpingo zimasumikidwa pa kulalikira, pamodzi ndi makonzedwe a kuthandiza chiŵalo chilichonse kuti chikhale ndi phande mwanjira ina yake. Kuyanjana kwathithithi ndi mpingo nthaŵi zonse ndiko njira yabwino koposa yoŵalitsirabe kuunika kwathu.
7 Tingathe kuŵala m’njira zimene sizingaphatikizepo umboni wapakamwa. Tingathe kukopa ena mwa khalidwe lathu chabe. Zimenezo nzimene Petro analingalira pamene analimbikitsa kuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, . . . akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino.” (1 Pet. 2:12) Ambiri amaona ntchito kapena gulu malinga ndi khalidwe la anthu ake. Pamene anthu ena aona anthu amakhalidwe abwino, oona mtima, amtendere, ndi omvera lamulo, amaona anthu otero kukhala osiyana ndi ena ndipo amanena kuti amakhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo imene ili yapamwamba kwambiri kuposa ija imene ambiri amatsatira. Chotero mwamuna wokwatira amaŵalitsa kuunika kwake pamene alemekeza ndi kusunga mkazi wake m’njira yachikondi; mkazi amachitanso chimodzimodzi mwa kulemekeza umutu wa mwamuna wake. Ana amakhala osiyana ndi ena pamene amvera makolo awo ndi kupeŵa dama ndi anamgoneka. Wolembedwa ntchito amene amasamalira ntchito yake, woona mtima, ndi amene ali wolingalira ena amaŵerengeredwa kwambiri. Mwa kusonyeza mikhalidwe imeneyi Yachikristu, timaŵalitsa kuunika kwathu, tikumasonyeza ena ubwino wa njira yathu ya moyo.
8 Kulalikira ndiko kulankhula kwa ena za zimene taphunzira m’Mawu a Mulungu. Zimenezo zimachitidwa poyera papulatifomu kapena pamakomo, koma sizimangolekezera pomwepo. Zochita zathu za tsiku ndi tsiku zimatichititsa kuonana ndi anthu ambiri. Kodi mumalankhula kangati patsiku ndi anansi anu oyandikana nawo nyumba? Kodi anthu amagogoda kangati pakhomo panu? Kodi ndi anthu angati osiyanasiyana amene mumakumana nawo pamene mukugula zinthu, muli m’basi, kapena amene amagwira ntchito kuntchito kwanu? Ngati muli mwana wa sukulu, kodi mungadziŵe chiŵerengero cha anthu amene mumalankhula nawo tsiku lililonse? Mipata yolankhula ndi ena njosaŵerengekadi. Zimene mungangofunikira kuchita ndizo kukumbukira mfundo zingapo za Malemba, kukhala ndi Baibulo ndi matrakiti pang’ono, ndi kuyamba kulankhula pamene mupeza mpata.
9 Ena amazengereza kuyesa ulaliki wamwamwaŵi, ngakhale kuti uli wosavuta. Angakhale okayikira, akumaumirira kuti ali amanyazi kwambiri kapena amantha kwambiri kulankhula ndi anthu osawadziŵa. Angakhale amantha ponena za kudzidziŵikitsa kapena ponena za kuyankhidwa mwaukali. Awo amene amadziŵa za kulalikira mwamwaŵi angakuuzeni kuti kaŵirikaŵiri palibe chifukwa chodera nkhaŵa. Ena kwakukulukulu ali ofanana nafe; amafuna zimene tifuna, ali ndi nkhaŵa zofanana ndi zathu, ndipo amafuna zinthu zofanana ndi zathu kaamba ka iwo ndi mabanja awo. Ambiri amakhala okoma mtima pamene munthu amwetulira kwa iwo kapena awapatsa moni mwaubwenzi. Kuti muyambe kukambitsirana nawo, mufunikira ‘kulimbika.’ (1 Ates. 2:2) Komabe, pamene muyamba, mudzadabwa ndipo mudzakondwera ndi zotulukapo zake.
10 Timadala Pamene Tiŵalitsa Kuunika Kwathu: Nazi zitsanzo zina za zokumana nazo zotsitsimula zochitika chifukwa cha kuchitira umboni kwamwamwaŵi: Mkazi wina wazaka 55 anali kuyesa kudutsa msewu. Pamene galimoto lina linatsala pang’ono kumgunda, mlongo wina anagwira mkono wake ndi kumkokera kumbuyo, akumati: “Samalani chonde. Tikukhala m’nthaŵi zangozi!” Ndiyeno mlongoyo anafotokoza chifukwa chake nthaŵizi zili zangozi motere. Mkaziyo anafunsa kuti, “Kodi ndinu wa Mboni za Yehova?” Atapeza buku lathu lina kwa mbale wake, mkaziyo anafuna kuonana ndi wa Mboni za Yehova wina, ndipo chochitikachi chinatheketsa zimenezo.
11 Mlongo wina anayamba kukambitsirana ndi mkazi wina m’chipinda choyembekezera ku ofesi ya dokotala. Mkaziyo anamvetsera mwatcheru ndiyeno anati: “Ndakhala ndikukumana ndi Mboni za Yehova nthaŵi zingapo; koma ngati nthaŵi ina mtsogolomu ndidzakhala mmodzi wa Mboni za Yehova, ndidzatero chifukwa cha zimene mwangondiuza kumenezi. Kukumvetserani kwachita ngati ndayamba kuona kuunika m’malo amdima.”
12 Kukoma mtima kungakhale mlatho wothandizira ena kuphunzira choonadi. Pamene alongo ena aŵiri anali kupita kwawo kuchokera ku utumiki wakumunda, anaona mkazi wina wokalamba amene anaonekera kukhala wodwala pamene anali kutsika basi. Iwowo anaima ndi kufunsa gogoyo ngati anali kufuna thandizo. Iyeyo anadabwa kwambiri kuti anthu aŵiri amene sanawaonepo anasonyeza chifundo kwa iye kwakuti anaumirira kuti adziŵe chimene chinawasonkhezera kuchita mchitidwe wokoma mtima kwa iye. Zimenezi zinatsegula khomo la kupereka umboni. Gogoyo anapereka adiresi yake mosavuta ndipo anawapempha mokondwera kuti adzafike kwawo. Phunziro linayambidwa. Posapita nthaŵi gogoyo anayamba kufika pamisonkhano ndipo tsopano akuuza ena choonadi.
13 Mlongo wina wokalamba amagwiritsira ntchito nthaŵi ya mmamaŵa kuchitira umboni kugombe lakwawo. Amakumana ndi olembedwa ntchito za m’nyumba achikazi, olera ana, antchito a m’banki, ndi ena amene amakonda kuyenda kwawo kolimbitsa thupi m’misewu mmaŵa. Amachititsa maphunziro a Baibulo, atakhala pamabenchi. Anthu angapo aphunzira choonadi kwa iye ndipo tsopano ndi Mboni za Yehova.
14 Mlongo wina anamva wantchito mnzake kuntchito kwake akumalankhula za chipani china chandale chimene mkaziyo anakhulupirira kuti chingathetse mavuto a dziko. Mlongoyo anayamba kulankhula, akumasimba za malonjezo onena za zimene Ufumu wa Mulungu udzachita. Makambitsirano akuntchito ameneŵa anayambitsa phunziro la Baibulo lokhazikika panyumba, ndipo potsirizira pake mkaziyo ndi mwamuna wake anakhala Mboni.
15 Musaiŵale Konse Kuti Ndinu Mboni! Pamene Yesu anatchula kuti ophunzira ake anali “kuunika kwa dziko lapansi,” anafotokoza kuti anayenera kuthandiza ena kupindula ndi kuunikira kwauzimu kwa Mawu a Mulungu. Ngati tigwiritsira ntchito uphungu wa Yesu, kodi utumiki wathu tidzaulingalira motani?
16 Pofunafuna ntchito, anthu ena amasankha ntchito ya maola ochepa. Amaika malire a kuchuluka kwa nthaŵi ndi zoyesayesa zimene adzachita chifukwa chakuti akufuna kugwiritsira ntchito nthaŵi yawo yochuluka akumachita zinthu zimene amaona kukhala zofupa kwambiri. Kodi tili ndi lingaliro lofananalo pa utumiki wathu? Ngakhale kuti tingakhale okakamizika ndipo mwinamwake ofunitsitsa kupatula nthaŵi ina kaamba ka utumiki, kodi mtima wathu uyenera kukhala kwina?
17 Pozindikira kuti palibe chinthu chotchedwa kuti Mkristu wa maola ochepa, tinadzipatulira, ‘tikumadzikana’ ndi kuvomereza kutsata Yesu “mopitiriza.” (Mat. 16:24, NW) Chikhumbo chathu ndicho kupitiriza kuchita “mochokera mumtima,” tikumagwiritsira ntchito mwaŵi uliwonse kuŵalitsa kuunika kwathu kuti tifikire anthu kulikonse kumene ali. (Akol. 3:23, 24) Tiyenera kukaniza makhalidwe adziko, tikumasunga changu chathu monga momwe chinalili poyamba, ndi kutsimikizira kuti kuunika kwathu kukuŵalabe kwambiri. Ena angakhale atalola changu chawo kuzirala ndiponso kuunika kwawo kukhala kongoziya, kosaoneka ngakhale pafupi. Oterowo afunikira thandizo kuti apezenso changu cha utumiki.
18 Ena angafune kuleka chifukwa chakuti uthenga wathu uli wosayanjidwa ndi ambiri. Paulo anati uthenga wonena za Kristu unali “chinthu chopusa kwa iwo akutayika.” (1 Akor. 1:18) Komabe, mosasamala kanthu za zimene ena ananena, iye analengeza mwamphamvu kuti: “Uthenga wabwino sundichititsa manyazi.” (Aroma 1:16) Munthu amene amachita manyazi amaganiza kuti ali wapansi kapena wopanda pake. Kodi ife tingachite bwanji manyazi pamene tikulankhula za Mfumu Yam’mwambamwamba ya chilengedwe ndi makonzedwe ake odabwitsa amene yachita kaamba ka chimwemwe chathu chosatha? Nchinthu chosayenera kuganiza kuti tili apansi kapena opanda pake pamene tilankhula za choonadi chimenechi kwa ena. M’malo mwake, tiyenera kusonkhezeredwa kuchita zomwe tingathe, tikumasonyeza chikhulupiriro chathu chakuti tili “opanda chifukwa cha kuchita manyazi.”—2 Tim. 2:15.
19 Kuunika kwa choonadi kumene tsopano kukuŵala m’maiko ambiri padziko lonse lapansi kukupereka chiyembekezo chabwino cha moyo wosatha m’dziko latsopano laparadaiso. Tiyeni tisonyeze kuti tikulabadira chilangizo cha kuŵalitsa kuunika kwathu mopitiriza! Ngati titero, tidzakhala ndi chifukwa chosangalalira mofanana ndi ophunzira amene tsiku lililonse “sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.”—Mac. 5:42.