Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira March 12
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph.15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: “April—Nthaŵi ‘Yogwiritsitsa Ntchito ndi Kuyesetsa.’” (Ndime 1-13) Woyang’anira wotsogolera achititse. Kukambirana mwamphamvu zimene tikufuna kuchita mu April. Limbikitsani onse mu mpingo kulalikira mokwanira kuti tikwanitse cholinga chakuti tonse tichite utumiki mwezi umenewu.
Nyimbo Na. 147 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 19
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph.17: Konzekerani Kudzapezeka pa Msonkhano Wachigawo wa 2001. Mlembi akambirane nkhani ya msonkhano wachigawo ya m’mphatika mwa mafunso ndi mayankho. Monga afotokozera mu nkhaniyi, agogomezere mfundo zachikhalidwe za m’Malemba chifukwa chake tiyenera kumvera malangizo a Sosaite pankhani ya msonkhano. Yamikirani abale chifukwa chotsatira malangizo a Sosaite.
Mph. 20: “April—Nthaŵi ‘Yogwiritsitsa Ntchito ndi Kuyesetsa.’” (Ndime 14-30) Woyang’anira utumiki achititse. Nkhani komanso sankhani mbali zina zokambirana mwa mafunso ndi mayankho. Aliyense ayenera kulemba ndandanda yabwino kuti mu April athe kuchita utumiki mokwanira. Fotokozani ndandanda ya misonkhano yonse yokonzekera utumiki wakumunda imene yakonzedwa m’mwezi umenewu. Limbikitsani onse amene angathe kuchita upainiya wothandiza kutenga mafomu pambuyo pamsonkhano uno.
Nyimbo Na. 188 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 26
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Akumbutseni abale kuti sikuchedwa kupereka pakalipano fomu yofunsira upainiya wothandiza m’April. Limbikitsani onse kutsatira ndandanda ya kuŵerenga Baibulo ya Chikumbutso ya April 3-8, monga alembera m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku —2001. Lengezani tsiku limene mudzachite phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu wa Chikumbutso. Musaiŵale nkhani yapoyera yapadera Lamlungu likudzali pa April 1, yamutu wakuti “Kodi Ndani Angapulumutsidwe?” Limbikitsani onse kuchita utumiki tsiku limeneli, kuti mwezi wa April tiuyambe bwino.
Mph. 20: “Tonse Tilemekeze Yehova ndi Mwana Wake.” Nkhani ya m’malemba yosonkhezera maganizo yokambidwa ndi mkulu. Limbikitsani onse kuchita mokwanira ntchito yapadera imene yakonzedwa m’April ndiponso kuyesetsa kuitanira anthu ku Chikumbutso.
Mph.15: Kukonzekera Ulaliki Wathu wa Magazini. Mu April tidzagaŵira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pendani tsamba 8 la Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 1996 pandime 3 ndi 10. Gogomezerani (1) nkhani, (2) fundo yosangalatsa kukambirana, (3) funso lochititsa chidwi, ndi (4) lemba lapanthaŵi yake logwira mtima pogaŵira kope lililonse la magazini atsopano. Yesetsani kugwiritsa ntchito bulosha la Mulungu Amafunanji kapena buku la Chidziŵitso kuti muyambe kuphunzira Baibulo ndi anthu achidwi. Malizani ndi chitsanzo chokonzedwa bwino cha mmene tingachitire zimenezi paulendo woyamba.
Nyimbo Na. 207 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 2
Mph. 9: Zilengezo za pampingo. Limbikitsani ofalitsa kupereka malipoti awo a mu utumiki wakumunda a March. Pendani “Zofunika Kukumbukira Panthaŵi ya Chikumbutso.”
Mph.18: “Chikondi Chimatisonkhezera Kulalikira.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gogomezerani malemba a mu nkhaniyi. Pemphani wofalitsa amene wakhala wachangu kwa zaka zambiri kusimba mmene kukonda Mulungu kumam’sonkhezerera kupitirizabe kugwira ntchito yolalikira. Limbikitsani ofalitsa onse kugwira ntchito yolalikira mu April ndi kumka m’tsogolo.
Mph.18: “Thandizani Ena Kupezeka Pamisonkhano.” Mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa June 1996, ndime 14-16, ili ndi malingaliro ena a mmene tingatsogolere ophunzira Baibulo ku gulu. Sonyezani mmene bulosha la Mulungu Amafunanji (phunziro 5, ndime 7) ndi buku la Chidziŵitso (mutu 5, ndime 22) zingagwirire ntchito pachiyambi pomwe, kulimbikitsa ophunzira kupezeka pamisonkhano. Chitsanzo cha zimenezi, onetsani ulaliki wokonzedwa bwino, wofalitsa wozoloŵera akulimbikitsa mwachikondi wophunzira kulingalira mozama nkhani yopezeka pamisonkhano.
Nyimbo Na. 47 ndi pemphero lomaliza.