Kubwereramo Kolemba M’sukulu Ya Utumiki Wateokalase
Kubwereramo kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa January 1 kufikira April 23, 2001. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso n’ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Zonama m’ndemanga zotsatirazi:
1. Ngakhale kuti kutengeka maganizo sikuyenera kutipangitsa kusaona kulakwa kwakukulu, tingatsanzire chitsanzo cha Yosefe mwa kukhululukira mwachifundo munthu wolapa yemwe anatichimwira. (Gen. 42:21; 45:4, 5) [w99-CN 1/1 tsa. 31 ndime 2-3]
2. “Munthu wamkazi wa ana aakazi a Dani” anakwatiwanso ndi munthu wa fuko la Dani. (2 Mbiri 2:14) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w79 4/15 tsa. 31.]
3. Baibulo limatchula za ‘wokana Kristu’ mmodzi yekha, amene adzaonekere nthaŵi ina m’tsogolo. [rs-CN tsa. 414]
4. Yesu anasonyeza kudzichepetsa kwake mwa kulandira ntchito yapadera yobwera padziko lapansi kuchokera kumwamba ndi kukhala munthu wamba, wotsika poyerekeza ndi angelo. (Afil. 2:5-8; Aheb. 2:7) [w99-CN 2/1 tsa. 6 ndime 3]
5. Kulandidwa kwa Yuda kochitidwa ndi Sisaki ndiponso kufunkhidwa kwa “chuma cha m’nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu” zimatsimikiziridwa ndi zofukulidwa m’mabwinja. (2 Mbiri 12:9) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 2/1 tsa. 26 ndime 4.]
6. Akristu a m’zaka za zana loyamba sankachita ubatizo wamakanda. [rs-CN tsa. 364]
7. Munthu ayenera kutumikira Mulungu popanda malingaliro odzalandira mphoto patsogolo pake. [w99-CN 4/15 tsa. 16 ndime 1]
8. Potchula za ‘zochita’ za Yehova, monga zalembedwera pa Salmo 103:2, Davide ankalingalira za chilengedwe chooneka cha Yehova. [w99-CN 5/15 tsa. 21 ndime 5-6]
9. Umboni wa zofukulidwa m’mabwinja umachirikiza kwambiri nkhani ya m’Baibulo ya pa 2 Mafumu 17:6-18 yonena za kuwonongedwa kwa ufumu wakumpoto wa Israyeli kochitidwa ndi Asuri. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani gm-CN mas. 47-8.]
10. Mawu a Davide a pa 1 Mbiri 16:31 amasonyeza kuti ngakhale kuti ulamuliro wa Yehova ndi wochokera pachiyambi cha kulenga, Iye nthaŵi zina analankhulapo mwapadera ponena za ulamuliro wake zomwe zachititsa kuti anenedwe kuti ‘amachita ufumu’ nthaŵi zina. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 5/1 tsa. 11.]
Yankhani mafunso otsatiraŵa:
11. Mogwirizana ndi 2 Mafumu 19:32, 33, kodi mfumu ya Asuri inaletsedwa motani kuloŵa mu Yerusalemu? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 2/15 tsa. 28.]
12. Malinga ndi momwe Mateyu 24:45-51 akusonyezera, kodi chizindikiro cha anthu ampatuko n’chiyani? [rs-CN tsa. 301]
13. Kodi ndi phunziro lofunika kwambiri lokhudza nyonga liti lomwe tingaphunzire pa zimene zinachitikira Uziya Mfumu ya Yuda? (2 Mbiri 26:15-21) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w99-CN 12/1 tsa. 26 ndime 1-2.]
14. M’malo moyambitsa mwambo, kodi ndi phunziro lofunika lotani limene Yesu anatipatsa mwa kusambitsa mapazi a atumwi ake? (Yoh. 13:4, 5) [w99-CN 3/1 tsa. 31 ndime 1]
15. N’chifukwa chiyani nkhani yopezeka pa 1 Mbiri 14:8-17 inali yofunika m’tsiku la Yesaya, ndipo n’chifukwa chiyani iyenera kukhala yofunika kwa Matchalitchi Achikristu lerolino? (Yes. 28:21) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 6/1 tsa. 21 ndime 2-3.]
16. Kodi ndi mbali ziti za kulambira Baala zomwe zinakopa Aisrayeli ambiri? [w99-CN 4/1 tsa. 29 ndime 2-6]
17. Kodi ndi phunziro liti lothandiza lomwe tingatenge pa ntchito ya Hezekiya yoteteza ndi kuchulukitsa madzi a Yerusalemu? (2 Mbiri 32:3, 4) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 8/15 tsa. 6 ndime 1-2.]
18. Kodi ndi motani mmene chitsanzo cha Yosiya chingalimbikitsire achinyamata lerolino kutumikira Mulungu ndi kuima nji polimbana ndi kulambira konyenga? (2 Mbiri 34:3, 8, 33) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 8/1 tsa. 5 ndime 2.]
19. Kodi Ayuda onse amene anatsala m’Babulo anali osakhulupirika, ndipo kodi ndi phunziro lofunika liti lomwe tingaphunzire pa zimenezi? (Ezara 1:3-6) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 2/15 tsa. 28 ndime 4, 7.]
20. M’nkhani ya pa 2 Mbiri 5:13, 14, kodi muli umboni wotani wakuti Yehova anali kumvetsera chitamando cha mang’ombe cha anthu ake ndi kuti anakondwera nacho? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w94-CN 5/1 tsa. 10 ndime 7.]
Pezani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
21. Munthu amene akupereka uphungu kwa Mkristu mnzake ayenera kutsimikizira kuti zonse zimene akulankhula ndi zozikidwa pa ․․․․․․․ ya Mulungu, osati pa ․․․․․․․ za anthu ndi ․․․․․․․ zawo. (Akol. 2:8) [w99-CN 1/15 tsa. 22 ndime 1]
22. Sikudzatheka kukhala mu mkhalidwe ․․․․․․․ pa nkhondo ya ․․․․․․․ (Mat. 12:30; 2 Ates. 1:8) [rs-CN tsa. 41]
23. Monga momwe minga zingalepheretsere m’mera kukula, ․․․․․․․ zosalamulirika ndiponso mphamvu zonyenga za ․․․․․․․ zingalepheretse munthu kukula mwauzimu. (Mat. 13:19, 22) [w99-CN 3/15 tsa. 22 ndime 5]
24. ‘Kubatizidwa chifukwa cha akufa,’ monga momwe Paulo analembera pa 1 Akorinto 15:29, kumatanthauza kumizidwa kuloŵa m’njira ya moyo imene idzatsogolera ku ․․․․․․․ mofanana ndi ija ya Kristu ndiyeno ․․․․․․․ kumoyo wauzimu monga momwe iye anachitira. [rs-CN tsa. 367]
25. Kuti Mkristu woona apambane pa zinthu zomwe Solomo analephera, iye ayenera kukhala ataika kumbali ․․․․․․․ kapena ․․․․․․․ m’kulambira kwake ndi kuchita mogwirizana ndi mawu a ․․․․․․․ a ‘kukonda Yehova Mulungu wake ndi mtima wake wonse.’ (Mat. 22:37; 1 Mbiri 28:9) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 11/15 tsa. 19 ndime 17-18.]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. Nkhani ya pa 2 Mafumu 17:5, 6 imafotokoza za mmene (Tiligati-pilesere; Salimanezere V; Esarihadoni) anagonjetsera ufumu wakumpoto wa mafuko khumi a Israyeli ndi kumangira misasa Samariya kwa zaka zitatu, amene pomalizira pake anagonja kwa Asuri mu ( 740; 607; 537) B.C.E. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 2/15 tsa. 27 ndime 1.]
27. “Chaka cha makumi aŵiri cha Yotamu” chimatanthauza chaka cha 20 cha (moyo wake; ulamuliro wake weniweni; nthaŵi yomwe inadutsa kuchokera pamene anakhala mfumu). (2 Maf. 15:30) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w80 9/15 tsa. 8.]
28. Monga momwe Eksodo 4:11 amasonyezera, Yehova Mulungu ‘amalenga wosalankhula, wogontha, wamaso, ndi wakhungu’ chifukwa chake iye (ayenera kuimbidwa mlandu chifukwa cha zilema za anthu; amapanga anthu osiyanasiyana kaamba ka maudindo autumiki; walola kuti zilema zionekere pakati pa anthu). [w99-CN 5/1 tsa. 28 ndime 2]
29. Anthu amene anadza “kwa Davide kum’thandiza” (anasonkhezeredwa ndi dyera; anafuna ndi mtima wonse kuchirikiza ufumu wa Davide; ankangochita mwachiphamaso). (1 Mbiri 12:22) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w83 3/1 tsa. 18.]
30. Maumboni aŵiri okha a mapwando a tsiku la kubadwa a m’Baibulo (amachititsa mapwandowo kukhala ovomerezeka; amachititsa mapwandowo kukhala osavomerezeka; sasonyeza chilichonse pa za mapwando a tsiku la kubadwa). (Gen. 40:20-22; Mat. 14:6-10) [rs-CN tsa. 362]
Gwirizanitsani malemba otsatiraŵa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:
Eks. 21:22, 23; Miy. 25:11; Aroma 12:2; 2 Pet. 3:15, 16; Chiv. 16:13, 14
31. N’kofunika kuyesetsa kuti tisinthe kalingaliridwe kathu ndi kudzaza maganizo athu ndi choonadi cha Mulungu. [w99-CN 4/1 tsa. 22 ndime 2]
32. Popereka uphungu, n’kofunika kusankha mawu oyenera. [w99-CN 1/15 tsa. 23 ndime 1]
33. Yehova wasonyeza kuti munthu aziimbidwa mlandu chifukwa chovulaza mwana wosabadwa. [rs-CN tsa. 211]
34. Chisonkhezero cha Satana Mdyerekezi chikukankhira amitundu ku mkhalidwe wa padziko lonse umene udzachititsa kumenyana ndi Mulungu. [rs-CN tsa. 41]
35. Kupotoza Malemba kuti ayenerane ndi maganizo athu kungachititse chivulazo chosatha. [rs-CN tsa. 59]