Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/01 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 6/01 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu June: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. July ndi August: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabulosha amasamba 32 aŵa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo N’chiyani? Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, What Happens to Us When We Die?, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndiponso “Taonani!” Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” Mabulosha a Buku la Anthu Onse ndiponso Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi iyo Ilikodi? mungagaŵire pamene kuli koyenera kutero. September: Buku lililonse la masamba 192 limene mpingo uli nalo.

◼ Ofesi ya Sosaite ikulandira maoda a mabuku ndi magazini otumizidwa ndi ofalitsa. Tikupempha ofalitsa kuitanitsa mabuku ndi magazini ameneŵa kudzera ku mpingo wawo ndipo mabungwe a akulu akukumbutsidwa kuti oda ya mabuku a mpingo (S-14) aziitumiza ku Sosaite mwezi uliwonse.

◼ Anthu amene ali ndi vidiyo, wailesi ya kaseti kapena wailesi ya CD ndi okhawo amene angaitanitse makaseti avidiyo, awailesi ndiponso madisiki. Komanso kumbukirani kuti zinthu zimenezi n’zokwera mtengo, “Zinthu Zaoda Yapadera” ndipo oitanitsa zinthu zimenezi akhale oti angathe kupereka chopereka chogwirizana ndi zinthuzi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena