Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/01 tsamba 5-6
  • Maganizo Oyenera Pankhani ya Phwando la Ukwati

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maganizo Oyenera Pankhani ya Phwando la Ukwati
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 6/01 tsamba 5-6

Maganizo Oyenera Pankhani ya Phwando la Ukwati

1 Nyimbo Zakudziko ndi Kuvina pa Ukwati Wachikristu: Bwanji ngati mkwati ndi mkwatibwi akufuna kukhala ndi nyimbo zakudziko ndi kuvina paukwati wawo? Bwanji ngati asankha kudzakhala ndi vinyo kapena moŵa winawake? Mafunso ameneŵa n’ngofunikira kuwapenda mosamala kwambiri, popeza Baibulo limalamula kuti: “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”—1 Akor. 10:31.

2 Akwati ena amasankha nyimbo zoyenerera, amakonza nthaŵi yovina, ndiponso amagaŵa moŵa pamlingo wabwino. Malemba saletsa kuvina konse ndiponso saletsa kumwa moŵa pamlingo wabwino. Choncho, ngati mkwati ndi mkwatibwi asankha kuti padzakhala kuvina koyang’aniridwa bwino ndiponso moŵa pamlingo wabwino, amene sangakonde zimenezi asawanyoze chifukwa chakuti aika zimenezi pa ukwati wawo. Ndi nkhani imene akwati ayenera kusankha. Komanso, chifukwa cha kuipa kwa mavinidwe ena amasiku ano, nyimbo zosokosa, ndi kumwa moŵa mosadziletsa, akwati angapo achikristu asankha kusakhala ndi zochitika zimenezi paukwati wawo. Pasapezeke owanyoza chifukwa cha zimenezi, koma m’malo mwake athokozedwe chifukwa chofunitsitsa kupewa chilichonse chimene chingadzetse chitonzo padzina loyera la Mulungu. Mulimonsemo, kaya afuna kuti padzakhale kuvina ndiponso moŵa kapena ayi, mkwati ndiye ali ndi udindo wa zimene walola kuchitika paukwati wake.

3 N’zoonekeratu kuti paukwati womwe Yesu anapezekapo panali chakudya chambiri chabwino, popeza Baibulo limati linali phwando laukwati. Monga tikudziŵira, panalinso vinyo wochuluka. Mosakayikira, panali nyimbo zabwino ndi kuvina modzilemekeza chifukwa chakuti n’zimene Ayuda ankakonda kuchita pamacheza awo. Yesu anasonyeza zimenezi m’fanizo lake lotchukalo la mwana woloŵerera. Atate wolemera wa m’fanizo limenelo anasangalala kwambiri kuti mwana wawo walapa ndipo wabwerera moti anati: “[Tiyeni] tidye, tisekere.” Malinga n’kunena kwa Yesu, madyererowo anaphatikizapo “kuimba ndi kuvina.”—Luka 15:23, 25.

4 Choncho ngati mkwati ndi mkwatibwi asankha kukhala ndi vinyo kapena moŵa winawake paukwati wawo, ayenera kulinganiza kuti zimenezi ziyang’aniridwe bwino ndi anthu osamala kwambiri. Ndipo ngati asankha kuti padzakhale nyimbo zakudziko, ayenera kusankha nyimbo zoyenerera ndiponso asankhe munthu wosamala woyang’anira kukwera kapena kutsika kwa voliyumu. Anthu oitanidwawo asaloledwe kuloŵerera ndi kuika nyimbo zokayikitsa kapena kukweza kwambiri voliyumu ya choimbira. Ngati padzakhala kuvina, zimenezo zingachitidwe m’njira yaulemu ndi modziletsa. Ngati achibale osakhulupirira kapena Akristu osakhwima m’nzeru avina monyanyula kapena modzutsa chilakolako chonyansa, mkwati angafunikire kusintha nyimbo zoimbidwazo kapena kupempha mwanzeru kuti pasakhalenso kuvina. Apo ayi, phwando laukwati lingasanduke chipwirikiti ndi kukhumudwitsa ena.—Aroma 14:21.

5 Baibulo limachenjeza kuti “chakumwa chaukali chisokosa.” (Miy. 20:1) Mawu achihebri otembenuzidwa kuti “kusokosa” amatanthauza “kupanga phokoso lalikulu.” Ngati moŵa ungapangitse munthu mmodzi kusokosera, tangolingalirani zimene ungachite kwa chinamtindi cha anthu amene asonkhana pamodzi n’kumwa mopitirira muyeso! Mosakayikira, sikungakhale kovuta kuti zochitika zimenezo zifike pokhala “kuledzera, mchezo, ndi zina zotere,” zomwe Baibulo limazitcha kuti ndi “ntchito za thupi.” Zochitika zimenezi ndizo zimapangitsa aliyense wosalapa kukhala wosayenerera kulandira moyo wosatha mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu.—Agal. 5:19-21.

6 Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “mchezo” ankatchulidwa ponena za achinyamata oledzerako pang’ono omwe ankasokosera, kuvina ndi kuimba nyimbo mumsewu. Ngati anthu akumwa moŵa mopitirira paukwati, ndiponso ngati pali nyimbo zosokosa ndi kuvina kotayirira, pali ngozi yaikulu yakuti phwandolo lingakhale ngati mchezo. Zikatero, ofooka angagwere mwamsanga m’chiyeso ndi kuchita ntchito zina zathupi monga “dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, [kapena kuyamba] ndewu.” M’pofunika kwambiri kupewa ntchito zathupi zimenezi kuti zisawononge chisangalalo cha phwando lachikristu la ukwati. Njira imodzi yochitira zimenezi ndiyo kuyang’anira bwino anthu obwera pa phwando laukwati.

7 Kodi N’ndani Ayenera Kubwera pa Phwando la Ukwati?: Yesu ndi ophunzira ake anaitanidwa ku ukwati wina ku Kana wa ku Galileya. Iwo anapita ku mwambowo, ndipo Yesu anachitaponso kanthu kena kuti anthu asangalale paukwatiwo. Vinyo atatha, iye mozizwitsa anapanga wina wabwino koposa. Ukwatiwo utatha, n’zosakayikitsa kuti vinyo amene anatsala anatenga ndi mkwati woyamikirayo ndi banja lake amene anam’gwiritsa ntchito kwa kanthaŵi ndithu.—Yoh. 2:3-11.

8 Pali maphunziro angapo amene tingaphunzirepo pa ukwati umene Yesu anapezekapo. Choyamba, Yesu ndi ophunzira ake sanapite kuphwando laukwatilo osaitanidwa. Baibulo limanena molunjika kuti anachita kuitanidwa. (Yoh. 2:1, 2) Momwemonso, m’mafanizo ake aŵiri a mapwando aukwati, Yesu mobwerezabwereza ananenapo kuti anthuwo analipo chifukwa anachita kuitanidwa.—Mat. 22:2-4, 8, 9; Luka 14:8-10.

9 M’mayiko ena, n’zofala kuti aliyense amakhala womasuka kupita kuphwando laukwati kaya wachita kuitanidwa kapena ayi. Komabe, zimenezi zingapangitse mavuto a zandalama. Mkwati ndi mkwatibwi omwe alibe ndalama zambiri angaloŵe m’ngongole pofuna kuonetsetsa kuti padzakhale chakudya ndi zakumwa zokwanira khamu lalikulu, losadziŵika bwino chiŵerengero chake. Chotero, ngati mkwati ndi mkwatibwi asankha kukhala ndi phwando laling’ono la anthu oŵerengeka okha, Akristu anzawo omwe sanaitanidwe ayenera kumvetsa ndi kulemekeza zimenezi.

10 Ngati sananene kuti aliyense abwere kuphwando laukwatilo, wotsatira woona wa Yesu adzapeŵa kupita mosaitanidwa ku phwando laukwati ndi kudya nawo chakudya chomwe akonzera anthu oitanidwa. Awo amene mtima wawo ukuwasonkhezera kupita ngakhale kuti sanaitanidwe adzifunse kuti, ‘Kodi ndikapita kuphwando laukwati limeneli sindidzasonyeza kuti eni ukwatiwo sindiwakonda? Kodi sindikasokoneza zimene akonza pa chisangalalo chaukwati wawo?’ Mkristu wachifundo atha kutumizira banjalo uthenga wowathokoza ndi kuwafunira madalitso a Yehova mwachikondi, m’malo mokhumudwa chifukwa choti sanamuitane. Angaganizenso zothandiza banjalo mwa kulitumizira mphatso kuti awonjezere chisangalalo cha tsiku la ukwati wawo.—Mlal. 7:9; Aef. 4:28.

11 Inde, Baibulo limapereka malangizo anzeru pankhani za umbeta, ukwati ndi mmene mapwando achikristu a ukwati ayenera kukhalira. Tonse tisamaliretu malangizo ameneŵa ndi kuwagwiritsa ntchito kuti miyoyo yathu ilemekeze Atate wathu wakumwamba Yehova, amene anayambitsa banja.—Aef. 3:14, 15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena