Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/01 tsamba 4
  • Maganizo Oyenera Pankhani ya Ukwati

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maganizo Oyenera Pankhani ya Ukwati
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 6/01 tsamba 4

Maganizo Oyenera Pankhani ya Ukwati

1 Kodi N’ndani Ayenera Kuyendetsa Ukwati wa Wofalitsa? Mbale angafune kukwatira. Angafune kupita kumudzi kwawo kukapeza mlongo woyenerera woti amange naye banja. Mabungwe ena a akulu amalemba kalata yodziŵikitsa mbaleyo ku bungwe la akulu la mpingo wina, akumati munthuyo akufuna wokwatirana naye, ndipo amam’kometsera mwakunena kuti ndi munthu wabwino, wa mbiri yabwinonso mu mpingo. Mabungwe ena a akulu akalandira kalata yotere, nthaŵi zina amaloŵa chintchito chofunira mbaleyo mlongo woyenerera wa mu mpingo wawowo. Izi sizoyenera, chifukwa si ntchito yawo. Akulu sasankhira mbale mtundu wa zovala zimene amavala, ntchito kapena malo okhala. Chotero, zisamawakhudzenso pamene mbaleyo akusankha mlongo wachikristu womanga naye banja.

2 Komanso, tikudziŵa kuti m’mipingo ina, akulu amaganiza kuti mbale ndi mlongo aziyamba avomerezedwa ndi akulu asanakwatirane, ngakhale kuti apitirira zaka zovomerezeka ndi malamulo a boma zoti munthu akwatire. Palibe zifukwa zilizonse za m’Malemba zochitira zimenezi. Ngati mbale ndi mlongo omwe ali ndi mbiri yabwino akufuna kukwatirana, izo n’zawo, malinga ngati ali omasuka mwa Malemba kuti akwatirane.

3 Ngati ali omasuka mwa Malemba kuti akwatirane, chinthu chokha chimene akufunika kuchita kuti akwatirane moyenera ndicho kuchita zimene boma limafuna pankhani ya ukwati, mwa kulembetsa moyenerera ukwati wawowo. Si kofunika kuti mwambo wa ukwati uchitikire m’Nyumba ya Ufumu kuti ukwati wawowo ukhale wovomerezeka kwa Mulungu kapena anthu.

4 Komabe, ngati amene akukwatiranawo akufuna kuti nkhani ya m’Malemba idzakambidwire m’Nyumba ya Ufumu, ayenera kulemba kalata ku komiti ya utumiki ya mpingowo kupempha kudzagwiritsira ntchito nyumbayo. Komiti ya utumiki idzaona ngati pali zifukwa zomveka zokanizira nyumbayo.

5 Ndithudi, ndi nkhani ya aliyense payekha kusankha kukwatira, nthaŵi yokwatira, kokakwatira ndiponso munthu wokwatirana naye. Ngati munthu wasankha bwino ukwati umakhala wosangalatsa kwambiri. Komabe, ngati wina wasankha udyo, awo adzakhala mavuto ake. —Agal. 6:5, 7.

6 Mwamuna wachikristu ndiye mutu wa banja lake ndipo ali ndi udindo wa m’Malemba wothandiza ana ake kusankha mwanzeru. Izi zingaphatikizepo kusankha wokwatirana naye. Nthaŵi zambiri, adzafuna mwana wawo kukwatirana ndi munthu amene adzathandiza mwana wawoyo mwauzimu. Komabe, ngati bambo waloŵetsedwa m’zimenezi, zimene achite poyendetsa ukwati wa mmodzi wa ana ake aamuna kapena aakazi kuti akwatirane ndi munthu woyenerera, ndi udindo wake. Ngati akonza zoti mwana wake akwatirane ndi m’kunja, kapena ngati n’zimene mwana wake wasankha kale ndipo iye akuthandizira zimenezo, ziyeneretso za maudindo ake ena mu mpingo adzazipenda.

7 Komabe mabungwe a akulu azipeŵa kudziloŵetsa mu nkhani zopezera abale alongo amene akuwayenerera mu mpingo. Asamalembenso ndiponso kutumiza makalata ankhani zimenezi. Kulemba makalata ndi mbali yofunika kwambiri mu mpingo wachikristu, komabe, tiyenera kuzindikira bwinobwino zimene zili zoyenera ndiponso zosayenera kulemba m’makalata afotokoza maganizo a mpingo. Tiyeneranso kumvetsa ntchito ya a akulu achikristu. Ndi zoona kuti pali zinthu zambiri zimene akulu angachite kuti athandize amene akufuna malangizo pankhani za ukwati ndi zina zotero. (1 Akor. 7:39) Chotero, tiyeni tonse modzichepetsa ndiponso mwanzeru tigwire ntchito zathu zofotokozedwa m’Malemba, zomwe ndi kuphunzitsa, kuweta ndi kulalikira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena