Maganizo Oyenera Pankhani ya Umbeta
1 M’mbuyomu takhala tikulandira malangizo ambiri onena za umbeta ndi ukwati. Kuti tonsefe tipindule, kuphatikizaponso anthu ambiri amene aphunzira choonadi zaka zingapo zapitazi, m’pofunika kubwereza mfundo zina ndi zina.—2 Pet. 1:12.
2 Kodi ukwati timauona motani?: Ukwati ndi makonzedwe apadera, omwe Yehova anakhazikitsira ana ake apadziko lapansife monga chinthu choyenera ndiponso chosangalatsa. Komabe, Baibulo silisonyeza kuti ukwati ndi kubereka ana ndizo zinthu zofunika kwambiri. (Mlal. 12:13; Marko 13:20) Yesu anali wosakwatira ndipo zimenezi zinam’pangitsa kuthera nthaŵi ndi maluso ake muutumiki. Yohane Mbatizi analinso wosakwatira. Pamenepa, kodi ndi bwino kunyoza abale ndi alongo achikristu amene akutumikira Yehova ali mbeta?
3 Malingaliro osagwirizana ndi malemba akuti zivute zitani munthu ayenera kupeza banja kapena kubereka ana, anachokera pa miyambo inayake. Anthu ambiri amaona ukwati ndi kubereka ana kukhala zinthu zomwe munthu safunika kuziphonya m’moyo. Choncho, amene amakhala mbeta kapena opanda ana amawaona ngati ali ndi vuto. Ndithudi, kulingalira bwino zimene timakhulupirira kudzapangitsa abale ndi alongo kuleka kukakamiza ndiponso kutonza ana awo kapena achinyamata ena mumpingo chifukwa chakuti ndi mbeta.
4 Pa Mateyu 19:11, 12, Yesu analimbikitsa umbeta ngati munthu angathe kukhala moyo woterowo. Iye anasonyeza kuti cholinga cha zimenezi chingakhale chakuti Mkristuyo athe kutumikira Mulungu popanda chododometsa. Yesu anatipempha kuti tiziona Ufumu kukhala chinthu chapamwamba kwambiri. Pempholi linali losiyana ndi zimene anthu ambiri a m’nthaŵi ya Yesu komanso a m’nthaŵi ino amaganiza, iwo amaika ukwati patsogolo pa kutumikira Mulungu ndi zinthu za Ufumu wake. Kuti tipambane polimbana ndi miyambo ya m’dera lathu tifunika kukonda Yehova kwambiri ndiponso kulimba mtima. Kukhala ndi maganizo a Kristu pankhani imeneyi kudzathandizanso Mkristu amene ali mbeta kukhala wopambana.
5 Mulungu saletsa ukwati; kukwatira n’kwabwino kwa anthu amene sangapeze chimwemwe ali mbeta kapena amene sangathe kudziletsa. (1 Akor. 7:8, 9, 28, 32-34, 38) Komabe, Baibulo sililimbikitsa kukwatira msanga koma limalimbikitsa munthu kukwatira atapyola pa unyamata, nthaŵi imene chikhumbo cha kugonana sichingasonkhezere zosankha zathu. Limanenanso bwino lomwe kuti banja lililonse lidzakhala ndi mavuto ndiponso lidzalepheretsa Mkristu kuchita zochuluka potumikira Yehova. Mtumwi Paulo anati ukwati umakhala ndi masautso.—1 Akor. 7:28.
6 Ena angathe kukhala mbeta kwanthaŵi yakutiyakuti, ena angathe kukhala kwamoyo wawo wonse. Mwa anthu ameneŵa tili ndi abale ndi alongo abwinoabwino amene akutumikira mwakhama monga apainiya kapena amene akutumikira m’nyumba za Beteli. Bwanji ana athu? Kodi tidzasangalala ngati atasankha kukhala kaye asanakwatire n’cholinga chakuti achite mokwanira utumiki wa Yehova, monga Samueli, mwana wamkazi wa Yefita, Timoteo ndiponso abale ndi alongo okhulupirika a otsalira odzozedwa? Tidzakhala osangalala kwabasi, ngati maganizo athu afanana kwambiri ndi a Mulungu pankhaniyi.