Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/01 tsamba 1
  • Kodi Mumasonyeza Mzimu Wachikristu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumasonyeza Mzimu Wachikristu?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 6/01 tsamba 1

Kodi Mumasonyeza Mzimu Wachikristu?

1 Paulo anamaliza kalata yake yopita ku mpingo wa ku Filipi ndi mawu olimbikitsa akuti: “Chisomo cha Ambuye Yesu Kristu chikhale ndi mzimu wanu.” (Afil. 4:23) Anawayamikira chifukwa chakuti anali achidwi chenicheni cholalikira uthenga wabwino komanso ochezeka ndi ofunirana zabwino.—Afil. 1:3-5, 4:15, 16.

2 Tiziyesetsa kusonyeza mzimu womwewu mu mpingo wathu. Anthu onse akasonyeza changu, kukoma mtima, ndi kuchereza alendo, zimabweretsa mzimu umene anthu ena amatha kuuzindikira. Mzimu wabwino ndiponso wokondana umabweretsa mgwirizano ndiponso mpingo umapita patsogolo mwauzimu. (1 Akor. 1:10) Mzimu woipa umafooketsa ndiponso umachititsa munthu kuchita zinthu monyinyirika.—Chiv. 3:15, 16.

3 Yambani Ndinu Akulu: Akulu ali ndi udindo wosungitsa mzimu wabwino pakati pa akulu anzawo ndiponso mu mpingo mwawo. N’chifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa chakuti mpingo ungasonkhezeredwe ndi maganizo awo ndiponso zochita zawo. Timayamikira kukhala ndi akulu achangu mu utumiki wakumunda, otipatsa moni mwachimwemwe ndiponso mawu abwino, amenenso amalangiza bwino ndiponso molimbikitsa, kaya mukhale mwamseri kapena pa pulatifomu.—Aheb. 13:7.

4 N’zoona kuti tonsefe tizichita mbali yathu kupangitsa mpingo kukhala waubwenzi, wochereza alendo, wachangu ndiponso wokonda zinthu zauzimu. Aliyense angasonyeze kuchezeka ndiponso chikondi pamene tikucheza ndi ena. (1 Akor. 16:14) Tisasankhe ena chifukwa cha zaka zawo, mtundu wawo, maphunziro kapena kupeza kwawo. (Yerekezerani ndi Aefeso 2:21.) Chiyembekezo chathu chingatipangitse kusonyeza mzimu wachimwemwe, wochereza kwambiri alendo, ndiponso wachangu mu utumiki.—Aroma 12:13; Akol. 3:22, 23.

5 Onse amene amayanjana nafe, kuphatikizapo atsopano, azidzimva kuti alandiridwa ndiponso azitha kuona kuti timawakonda kwambiri abale athu. Mwa utumiki wathu ndiponso mwa kusonyeza mikhalidwe yabwino yachikristu, timapereka umboni wakuti mpingo ndi “mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Tim. 3:15) Timakhalanso otetezeka mwauzimu chifukwa cha “mtendere wa Mulungu” umene umasunga mitima yathu ndi maganizo athu. (Afil. 4:6, 7) Tonse tiyesetsetu kusonyeza mzimu umene udzatipatsadi chisomo cha Yehova mwa Ambuye Yesu Kristu.—2 Tim. 4:22.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena