Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira June 11
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 15: “Maganizo Oyenera Pankhani ya Umbeta.” Nkhani yokambidwa ndi mkulu amene ali mpainiya kapena amene ali ndi mzimu waupainiya.
Mph. 20: “M’fikeni Pamtima Wophunzira Wanu.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo malingaliro abwino a mmene tingathandizire atsopano kukulitsa chikhulupiriro ndiponso chikondi mwa Yehova ndi Yesu m’mitima yawo. Gwiritsani ntchito mfundo zazikulu za mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 1999, tsamba 14, ndime 18-20.
Nyimbo Na. 184 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 18
Mph. 5: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 10: Kuyankha Oimitsa Kukambirana. Kukambirana ndi omvetsera. Pendani “Ndemanga” patsamba 15-16 m’buku la Kukambitsirana. Sankhani patsamba 16-20 ena a mawu otsutsa opezeka m’gawo lanu. Pemphani omvetsera kufotokoza mayankho amene amakhala ndi zotsatirapo zabwino ndiponso chifukwa chake.
Mph. 10: “Pitirizani ‘Kuchita Zabwino.’” Nkhani yolimbikitsa ya m’Malemba yokambidwa ndi mkulu.
Mph. 20: “Malingaliro Oyenera Pankhani ya Ukwati.” Akulu aŵiri akambirane nkhaniyi.
Nyimbo Na. 197 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 25
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Pendani mabuku ogaŵira mu July ndi August. Tchulani mitundu iŵiri ya mabulosha amene muli nawo pampingopo. Sonyezani chitsanzo cha ulaliki chokonzedwa bwino cha mmene tingagaŵirire mabuloshawo mu utumiki. Kuti muone zitsanzo zaulaliki, onani tsamba lomaliza la Utumiki Wathu wa Ufumu wa July ndi August kuyambira 1995 mpaka 1998.
Mph. 17: “Malingaliro Oyenera Pankhani ya Phwando la Ukwati.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
Mph. 18: “Kodi Mumasangalala Kuyenda ndi Ena mu Ulaliki?” Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Funsani mpainiya amene akuthandiza wofalitsa wina mu utumiki ndiponso wofalitsa amene akuthandizidwayo, akambirane ndandanda imene apanga yoyendera limodzi mu utumiki ndipo anene mapindu amene onseŵa akupeza.
Nyimbo Na. 29 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 2
Mph. 13: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wakumunda a June. Pendani bokosi lakuti “Zotsatira Zolimbikitsa za m’Munda.”
Mph. 20: Achinyamata—Sankhani Ntchito Mwanzeru. Iyi ndi mbali yoyamba ya nkhani zitatu za mu Msonkhano wa Utumiki imene idzafotokoza mfundo za chikhalidwe za m’Malemba zokhudza maphunziro owonjezera akusukulu. Achinyamata ena achikristu akuphunzira maphunziro apamwamba kuti adzapeze ntchito zakudziko, zimene zikusokoneza moyo wawo wauzimu. Mbali imeneyi ndiyoti bambo ndi mayi akambirane ndi mwana wawo wamwamuna kapena wamkazi wa zaka zapakati pa 13 ndi 19. Mwanayo wafika posankha chinthu chachikulu pankhani ya zolinga zam’tsogolo. Ngakhale kuti ena angasankhe kupeza ndalama zambiri, kutchuka, kapena moyo wa mwana alirenji, banjalo liŵerenge Baibulo kuti lione zimene Baibulolo limalimbikitsa. (Onani Achichepere Akufunsa, masamba 174-5; Nsanja ya Olonda ya August 15, 1997, tsamba 21, ndiponso ya September 1, 1999, masamba 19-21, ndime 1-3 ndi 5-6.) Mwanayo avomereze kuti ndi bwino kusankha ntchito imene idzam’thandize kukwanitsa zolinga zateokalase kuti apititse patsogolo ntchito ya Ufumu.
Mph. 12: “Kodi Mumasonyeza Mzimu Wachikristu?” Nkhani yolimbikitsa yokambidwa ndi woyang’anira wotsogolera.
Nyimbo Na. 32 ndi pemphero lomaliza.