Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu July ndi August: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabulosha amasamba 32 aŵa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndiponso “Taonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” Mabulosha a Buku la Anthu Onse, ndiponso Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi iyo Ilikodi?, mungawagaŵire pamene kuli koyenera kutero. September: Buku lililonse la masamba 192 limene mpingo uli nalo. October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Paulendo wobwereza mukapeza achidwi, aikeni pandandanda ya anthu amene mumawapatsa magazini.
◼ Kuyambira mwezi wa September, oyang’anira dera azikamba nkhani yapoyera ya mutu wakuti “Mmene Akristu Oona Amakometsera Chiphunzitso cha Mulungu.”
◼ Pakufunika kuwongolera zimene tinasindikiza mu Bokosi la Mafunso pa tsamba 7 mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2001. Pamenepo tinanena kuti, “Kaya mwanayo ndi wofalitsa wobatizidwa kapena wosabatizidwa, choyamba komiti ya chiweruzo yosankhidwa ndi bungwe la akulu idzasamalira nkhani yake malinga ndi zimene zili mu buku la Olinganizidwa, patsamba 148.” Pomveketsa zimenezi, tiyenera kunena kuti, ngati wolakwayo ndi wobatizidwa komanso wamng’ono, bungwe la akulu lidzasankha komiti ya chiweruzo kuti isamalire nkhaniyo, monga momwe angachitire ngati munthu wamkulu walakwa. Ngati munthu wobatizidwa wamng’onoyo ali ndi makolo okhulupirira, zingakhale bwino kwambiri kuonana naye limodzi ndi makolo ake. Koma ngati amene wachita tchimo lalikululo ndi munthu wamng’ono wosabatizidwa, tsamba 148 m’buku la Olinganizidwa limanena kuti bungwe la akulu lidzasankha akulu aŵiri kuti asamalire nkhaniyo. Ngakhale kuti akulu aŵiriŵa ali ndi udindo waukulu woweruza munthuyo, iwo si komiti ya chiweruzo. Pa zimene takambazi, tingaone kuti pali kusiyana posamalira nkhani ya kulakwa kwa wofalitsa wosabatizidwa ndi mwana wobatizidwa. (Onani w88-CN 11/15 masamba 18-20)
◼ Madeti a misonkhano yachigawo ya m’Chingelezi asintha. Mukudziŵa kuti msonkhano wachingelezi wa ku Blantyre unafunika kudzachitika pa September 7-9, 2001. Tsopano udzachitika pa August 10-12, 2001. Msonkhano wachingelezi wa ku Lilongwe unafunika kudzachitika pa August 10-12, 2001, koma tsopano udzachitika pa September 7-9, 2001.
◼ Chonde dziŵani kuti msonkhano wachigawo umene umafunika kuchitikira ku Ntaja ukachitikira ku Nselema.