Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/01 tsamba 6
  • Dongosolo ‘Loyenera ndi Lolongosoka’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dongosolo ‘Loyenera ndi Lolongosoka’
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu” wa 1996
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Msonkhano Wachigawo wa 1997 wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu” wa Mboni za Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2006 Wakuti “Chipulumutso Chayandikira”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2008
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 7/01 tsamba 6

Dongosolo ‘Loyenera ndi Lolongosoka’

1 Kuti msonkhano wachigawo uyende bwino, pamafunika ogwira ntchito ambiri. Oyang’anira msonkhano wachigawo amafuna malo amsonkhano ndiponso aubatizo abwino. Anthu ena komanso mabanja ena amakonza okha kayendedwe ndi malo ogona. Ndipo mipingo imasonkhanitsa antchito odzifunira kuti akagwire ntchito m’madipatimenti ambiri ofunika pamsonkhano wachigawo. Cholinga n’chakuti ‘zonse zichitike moyenera ndi molongosoka.’—1  Akor.  14:40.

2 Pothandizana ntchito ndi oyendetsa msonkhano, kumbukirani kuti kukonzekera kumatenga miyezi, nthaŵi zina zaka zimene. Abale ambirimbiri amathera nthaŵi yochuluka kukonza zinthu monga kufuna malo, kusonkhanitsa zipangizo ndiponso kupeza anthu antchito. Kukonzekera kumeneku kumapindulitsa anthu onse mwauzimu. Kodi tingathandize motani?

3 Mungaganizire njira zambiri zimene mungathandizire oyendetsa msonkhano, koma pano tingotchula zina mwa izo:

(1) Fikani nthaŵi yabwino. Ngati akulu akuyang’ana galimoto yoti mpingo udzayendere, aonetsetse kuti galimotoyo idzabwere kudzatenga anthu mofulumira kuti dalaivala asadzathamangitse kwambiri galimoto n’cholinga chokafika kumalo amsonkhanowo kusanade.

(2) Khalani pansi nthaŵi yabwino kuti muimbe nawo nyimbo yotsegulira chigawo chilichonse. Mukaona tcheyamani atakhala pampando nyimbo zoyambirira zili m’kati, khalani pansi.

(3) Mverani akalinde. Abale olimbikira ntchito ameneŵa amasungitsa bata kuti tonse tisangalale nawo kwambiri msonkhano.

(4) Lingalirani Ena. Musadodometse ena mwa kulankhulana mokweza ndi am’banja lanu kapena anzanu amene mwayandikana nawo mapulogalamu ali m’kati. Musatchingire ena amene akuonera seŵero.

(5) Samalani kwambiri anthu okalamba ndi olumala. Musalekerere ana kuthamanga mozungulira kapena moyandikira anthu ameneŵa kuopera kuti angawagunde n’kuwagwetsa.

(6) Ngati mukukhala m’nyumba ya munthu wina, lemekezani katundu wake. Musalole ana kulemba makoma kapena kuwononga mipando, matebulo ndi katundu wina.

(7) Aperekezeni ana aang’ono ku chimbudzi. Izi zidzapangitsa kuti zimbudzi zikhale zaudongo zoti ena n’kugwiritsa ntchito.

(8) Ngati mungathe, thandizani kulipirira zowonongedwa pamsonkhano. Pamsonkhano padzakhala mabokosi a zopereka zantchito imeneyi.

4 Monga atumiki a Yehova Mulungu, tili ndi mpata wosonyeza khalidwe lake m’zochita zathu zonse. Zimenezi zikuphatikizapo pokonzekera msonkhano ndiponso popita kumsonkhano umene umakhudza dzina la Mulungu. Kumbukirani kuti “sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere.” (1 Akor. 14:33) Chotero titsimikize mtima kuti anthu onse otiona azindikire khalidwe la Yehova limeneli mwa kuona khalidwe lathu pokonzekera ndiponso popita ku Msonkhano Wachigawo wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu.” Anthu oona mtima omwe adzationa azindikire kuti anthu a Yehova m’misonkhano amakhala adongosolo ‘loyenera ndi lolongosoka.’—Sal. 68:26.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena