Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2008
1. (a) Kodi n’chifukwa chiyani malangizo a Paulo kwa Akhristu achiheberi ali ofunika kwambiri masiku ano? (Werengani Aheberi 10:24, 25.) (b) Kodi tidzakhala ndi mwayi wotani wosonyezera kuti tikumvera malangizo a Paulo?
1 Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu achiheberi kusonkhana pamodzi ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake, “makamaka” poona kuti tsikulo likuyandikira. (Aheb. 10:24, 25) Masiku ano pali umboni wambiri wotsimikizira kuti “tsiku” lomwe ananena Paulo layandikira kwambiri. Choncho, timasangalala ndi mwayi wosonkhana pamodzi ndi abale ndi alongo athu n’cholinga cholandira malangizo auzimu amene angatitsogolere “m’masiku otsiriza” ndi oopsa ano. (2 Tim. 3:1) Mwayi woterewu udzapezeka pa msonkhano wachigawo wa 2008.
2. (a) N’chifukwa chiyani kuli kofunika kupezeka masiku onse atatu a msonkhanowu? (b) Kodi tingayambe bwanji kukonzekera kuti tikapezeke ku msonkhano wachigawo?
2 Mudzakhalepo Masiku Onse Atatu: Tikulimbikitsidwa kuti tidzakhalepo masiku onse atatu. Mwa ‘kusaleka kusonkhana kwathu pamodzi’ sitidzaphonya chakudya chilichonse chauzimu. (Aheb. 10:25) Ndi bwino kuyambiratu kukonzekera. Tingayambiretu kupempha mabwana athu kuti aone mmene angakonzere zinthu. Ngati msonkhano udzachitike nthawi ya sukulu, tiuze aphunzitsi a ana athu za nkhaniyi. Tiwauze kuti misonkhano yachigawo ndi mbali ya kulambira kwathu kwa nthawi zonse. Ngati tichita khama kuika zinthu za Ufumu patsogolo, Yehova adzatithandiza.—Mat. 6:33.
3. Kodi ndi njira ziti zimene tingasonyezere kuganizira ena?
3 Tithandize Anthu Ena Kuti Adzapezekepo: Paulo anachonderera abale kuti ‘aganizirane wina ndi mnzake.’ (Aheb. 10:24) Kodi ku Phunziro lathu la Buku la Mpingo kuli abale ndi alongo amene angafunikire thandizo kuti adzapite ku msonkhano wachigawo? Kodi tingathandize ophunzira Baibulo athu kuti adzapite ku msonkhanowu ngakhale tsiku limodzi lokha? Tikamadziwitsa achibale athu omwe si Mboni za msonkhanowu, tiwapemphe kuti adzapite nafe. Kuchita kwanu zinthu mwachikondi kungabweretse madalitso osayembekezereka.
4. (a) Kodi tingadziwe bwanji za masiku ndi malo a kumene kukachitikire msonkhano? (b) Kodi tingatani ngati tikufuna malo ogona kumsonkhano wina osakhala umene mpingo wathu udzapiteko?
4 Ngati Pali Zimene Tikufuna Kufunsa: Ofesi ya nthambi imalandira mafoni ambiri chaka chilichonse ofunsa nthawi ndi malo a kumene msonkhano ukachitikire. Pafupifupi mafoni onse amachokera kwa abale ndi alongo amene anauzidwa kale zimenezi. Tisanaimbire ofesi ya nthambi, tikupemphedwa kuti tione kaye Nsanja ya Olonda ya March 1, 2008 kapena Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2008. Komanso ngati mudzapite ku msonkhano wina osakhala umene mpingo wanu udzapiteko, tikukulimbikitsani kuti mukonze nokha za malo ogona.
5. (a) Kodi tingamulemekeze motani Yehova tikapita ku msonkhano? (b) Kodi mabwana a pahotela ananena zotani ataona khalidwe labwino la abale athu?
5 Ntchito Zabwino: Tikamvera lamulo la Yehova losonkhana ndi kulambira pamodzi ‘timapindula.’ Chofunika kwambiri, timakhala ndi mpata wolemekeza dzina la Yehova. (Yes. 48:17) ‘Ntchito zathu zokoma zimaonekera’ kwa anthu ambiri tikakhala pa msonkhano, ndipo ena alankhulapo mmene amationera. (1 Tim. 5:25) Mumzinda wina momwe mwakhala mukuchitikira misonkhano yachigawo kwa nthawi yaitali, bwana wa pahotela ina anati: “Anthu ambiri mumzinda uno akunena zabwino za inu Mboni za Yehova ndipo akuyamikira misonkhano yanu. Tikudziwa mmene anthu inu mumayeretsera bwalo lomwe mumapempha kuchitiramo msonkhano, ndipo timakuonani mukuyeretsa malo oimikako galimoto. Timasangalala kulandira anthu inu panyengo ino yachilimwe. Tikukhulupirira kuti mgwirizano wathu upitirira mpaka m’tsogolo.” Bwana wa pahotela ina atafotokoza za mavuto amene amakumana nawo ndi magulu ena komanso anthu azisudzo akabwera pa hotela yawo, anayamikira abale athu kuti amakhala ogwirizana ndi anthu a pahotelapo komanso okoma mtima. Iye anati, “Timalakalaka alendo athu onse akanakhala ngati Mboni za Yehova!” Khalidwe la abale athu lomwe limachititsa kuti tiyamikiridwe motere limakondweretsa mtima wa Mulungu wathu, Yehova.
6. Kodi lemba la Mateyo 4:4 likusonyeza bwanji kufunika komvetsera mwatcheru nkhani iliyonse ya pamsonkhano?
6 Yesu anati munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha koma ndi “mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mat. 4:4) Pamisonkhano yathu yachigawo, Yehova amapereka chakudya chauzimu “panthawi yoyenera,” chokonzedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Pachitika ntchito yaikulu kuti phwando lauzimu limeneli likonzedwe. Tiyeni tisonyeze kuti timayamikira mmene Yehova amatisamalirira mwachikondi mwa kudzapezekapo ndi kumvetsera mwatcheru nkhani iliyonse ya pamsonkhanowo.
Nthawi za Msonkhano:
Tsiku Loyamba ndi Lachiwiri
8:20 a.m. - 3:55 p.m.
Tsiku Lomaliza
8:20 a.m. - 3:00 p.m.