Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2007 Wakuti “Tsatirani Khristu!”
1, 2. (a) Kodi Mose analimbikitsa bwanji Aisiraeli kupindula ndi misonkhano? (b) Kodi panopa tiyenera kuyamba kukonzekera zinthu ziti?
1 Mose anapereka malangizo kwa Aisiraeli ndi alendo onse kuti azisonkhana pamodzi zaka 7 zilizonse kuti akamvetsere Chilamulo chikuwerengedwa. Cholinga chake chinali chotani? “Kuti amve, ndi kuti aphunzire.” (Deut. 31:10-12) Yehova anaona kufunika kosonkhanitsa anthu ake m’magulu akuluakulu. Posachedwapa, anthu a Yehova adzasonkhananso pa misonkhano yachigawo ya masiku atatu yakuti “Tsatirani Khristu!”
2 Kodi mwayamba kukonzekera? Kodi mukufunika kupempha abwana anu kuti adzakuloleni kupita ku msonkhanoko? Kodi mungathandize ophunzira Baibulo anu kapena achibale anu osakhulupirira kuti mudzapite nawo limodzi kumsonkhano? Kodi mumpingo wanu muli ena amene akufunika thandizo kuti akapezekepo? Kodi mukukonza zodzapita ku msonkhano wosiyana ndi umene mpingo wanu udzapite? Kodi mudzafunikira malo ogona? Mfundo zotsatirazi zikuthandizani kukonzekera.
3. (a) Kodi lemba la Yesaya 25:6 likukwaniritsidwa motani masiku ano? (b) Kodi chimachitika n’chiyani tsiku loyamba la msonkhano, ndipo aliyense wa ife ayenera kuchita chiyani?
3 Mudzakhaleko Masiku Onse Atatu: Yehova amapatsa anthu ake chakudya chauzimu cha mwanaalirenji. (Yes. 25:6) China mwa chakudya chimenechi ndi phwando lauzimu limene timakhala nalo pamisonkhano yathu yapachaka. Zaoneka kuti anthu obwera tsiku loyamba amakhala ochepa kwambiri poyerekezera ndi masiku ena. Yesetsani kudzapezekapo masiku onse atatu otsitsimula a msonkhano umene gulu la Yehova latikonzera. Ngati mukufunikira kupempha abwana anu kuti musadzagwire ntchito, pemphererani nkhani imeneyi. Kenaka ‘limbani mtima’ n’kulankhula ndi abwana anuwo tsiku la msonkhano wanu likadzangolengezedwa. (1 Ates. 2:2; Neh. 2:4, 5) Zingakhale zothandiza kuwafotokozera kuti pachipembedzo chanu, mumakhala ndi msonkhano wapachaka. Kuchita zimenezi nthawi ikadalipo kungathandize abwana anu kuti athe kukonzekera ndipo zitha kukhala zosavuta kuti akuloleni kudzapita ku msonkhanowo.
4. Kodi tingachite chiyani kuti ophunzira Baibulo athu ndi anthu osakhulupirira a pabanja pathu adziwe za msonkhano?
4 Konzekeretsani Ophunzira Baibulo Ndiponso Banja Lanu: Zingakhale zosangalatsa kwambiri ngati mungadzabwere ku msonkhano ndi amene mumaphunzira nawo Baibulo kuti adzadzionere okha ubale wathu wachikhristu “mu msonkhano waukulu”! (Sal. 22:25) Auzeni nthawi ikadalipo kuti adzabwere. Auzeni zifukwa zimene inuyo mumasangalalira ndi kupita ku misonkhano. Ophunzira Baibulowo titha kuwaonetsa mavidiyo athu amene amasonyeza anthu ali pa misonkhano, makamaka vidiyo ya United by Divine Teaching, kuti asakachite chilendo. Dziwitsani anthu osakhulupirira a pabanja panu za msonkhanowu. Mwina angakonze zoti adzaonerere sewero kapena adzabwere nanu tsiku limodzi la msonkhano kapena masiku angapo.
5. Kodi tingasonyeze bwanji mtima wowolowa manja wotchulidwa pa 1 Timoteyo 6:18?
5 Kuthandiza Abale ndi Alongo Anu: Mtumwi Paulo analangiza Akhristu amene anali achuma kuti “azichita zabwino, akhale olemera pa ntchito zabwino, owolowa manja, okonzeka kugawana ndi ena.” (1 Tim. 6:17, 18) Tingasonyeze mtima wowolowa manja umene Paulo analimbikitsa mwa kuganizira za anthu okalamba ndi odwala, amene ali mu utumiki wa nthawi zonse, mabanja a kholo limodzi, ndiponso mwina ena mumpingo mwathu amene angafunike kuwathandiza kuti adzapezeke pa msonkhano. Kusamalira anthu oterowo makamaka ndi ntchito ya achibale awo amene ali m’choonadi, koma akulu ndi ena mokoma mtima angawathandize pamene pangafunikire kutero.—Agal. 6:10; 1 Tim. 5:4.
6. Kodi malangizo akuti chiyani ngati tikufuna kudzapita ku msonkhano wosiyana ndi wathu?
6 Kupita ku Msonkhano Wina: Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2007 uli ndi misonkhano yonse imene idzachitike m’Malawi muno. Ngati mukufuna kudzapita ku msonkhano wina wosiyana ndi umene mpingo wanu udzapita, konzani nokha za kayendedwe ndi malo ogona.
7, 8. (a) Kodi ndi zinthu zotani zimene amatikonzera tisanafike pa malo a msonkhano? (b) Kodi tingayamikire bwanji ntchito yonse yomwe yagwirika chifukwa cha ife? (Werengani Aheberi 13:17.)
7 Tsatirani Zomwe Zakonzedwa: Tikafika pa malo a msonkhano, zimachita kuonekeratu kuti anthu agwira ntchito yaikulu pokonzekera kufika kwathu. Abale achikondi ogwira ntchito ya ukalinde amatipatsa moni, mapulogalamu, ndi kutithandiza kupeza pokhala. Abale ndi alongo amakhala atayeretsa malowo n’kukonza pulatifomu yokongola. Pamakhala patachitikanso ntchito yofunika kwambiri yosaonekera poyera pokonzekera nkhani, ndi kusamalira zinthu zina zambiri.
8 Pamsonkhano uliwonse, anthu ambiri amakhala atagwira ntchito kwa miyezi yambiri kukonza zinthu zosiyanasiyana, ndipo mabanja awo amakhalanso atathandizapo powalola kusamalira zinthu zofunika zimenezo. Kodi sitiyamikira kudzipereka kwa anthu amenewa kuti ife tipindule? Tiyenera kuyamikira mwa kumvera malangizo amene ali mu nkhani ino ndi malangizo ena alionse amene tingalandire msonkhano wathu usanafike. (Aheb. 13:17) Aliyense akamvera malangizo, ‘zinthu zonse zimachitika moyenera ndi mwadongosolo.’—1 Akor. 14:40.
9. (a) N’chifukwa chiyani misonkhano ya anthu a Yehova ili yofunika kwambiri masiku ano? (b) Kodi aliyense wa ife angachite chiyani panopa?
9 Misonkhano ya anthu a Mulungu ndi yofunika kwambiri chifukwa “tsikulo likuyandikira.” (Aheb. 10:25) Pamisonkhano yathu yachikhristu, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatiuza zinthu zotithandiza “kusamalira kuchita mawu onse” amene Yehova akufuna kuti tizitsatira. (Deut. 31:12) Yambani panopa kukonzekera kudzakhala nawo masiku onse atatu pa msonkhano wachigawo wakuti “Tsatirani Khristu!” n’kudzapindula ndi malangizo onse auzimu ndi mayanjano osangalatsa!
[Bokosi patsamba 4]
Nthawi ya Mapulogalamu
Tsiku Loyamba ndi Lachiwiri
8:20 a.m. - 3:55 p.m.
Tsiku Lachitatu
8:20 a.m. - 3:00 p.m.