Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2009
1. (a) Kodi tidzapeza madalitso otani tikadzapezeka pamsonkhano wachigawo masiku onse atatu? (b) Kodi tiyenera kukonzekera bwanji panopa?
1 Tonsefe tikuyembekeza mwachidwi msonkhano wachigawo wa 2009 pamene tidzakhale ndi mwayi wosonkhana ndi anzathu amene timatamanda nawo Yehova, omwenso “amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mat. 5:3) Popeza tsiku la Yehova layandikira kwambiri, tikulimbikitsa aliyense kudzapezeka masiku onse atatu, kuti tidzapindule mokwanira pocheza ndi Akhristu anzathu komanso kuti tidzalimbikitsidwe mwauzimu n’cholinga choti tidzalimbitse chikhulupiriro chathu. (Zef. 1:14) Dziwitsani aphunzitsi anu kapena okulembani ntchito kuti msonkhano wachigawo ndi wofunika kwambiri pakulambira kwanu. Kuti zitheke, mufunika kulimba mtima n’kuwadziwitsa mofulumira. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni ndipo iye adzakudalitsani.—Yes. 50:10.
2. N’chifukwa chiyani misonkhano ina yachigawo idzakhale ngati misonkhano ya mayiko?
2 Misonkhano ya Mayiko: Popeza misonkhanoyi idzachitikira m’mayiko komanso m’mizinda yowerengeka, amene ayenera kukapezekako ndi okhawo amene aitanidwa. Tikatsatira malangizo amenewa zidzathandiza kuti anthu asadzapanikizane. (1 Akor. 14:40; Aheb. 13:17) Ngakhale zili choncho, misonkhano yachigawo yambiri idzakhalanso ngati misonkhano ya mayiko chifukwa chakuti amishonale, abale amene akutumikira pa Beteli m’mayiko ena, ndiponso abale a zomangamanga a m’mayiko ena, adzapita kwawo kukachita msonkhano.
3. Kodi tingasonyeze bwanji chikondi chachikhristu kwa ena mumpingo wathu?
3 Tithandize Anthu Ena Kuti Adzapezekepo: Kodi pali anthu ena mumpingo wanu amene adzafuna thandizo kuti apezeke pa msonkhanowu? Ngati mudzathandiza ena kupezeka pa msonkhanowu ndiye kuti ‘simukusamala zofuna zanu zokha, koma mukusamalanso zofuna za ena.’—Afil. 2:4.
4. Ngati mudzapite ku msonkhano wosiyana ndi umene mpingo wanu udzapite, kodi muyenera kutani?
4 Ngati Pali Zimene Tikufuna Kufunsa: Tisanaimbe foni ku ofesi ya nthambi kufunsa za masiku komanso malo a misonkhano yachigawo, tiyenera kuona kaye Nsanja ya Olonda ya March 1, 2009, kapena kufunsa mlembi wa mpingo wathu kuti tidziwe zimene tikufunazo. Zimenezi zidzathandiza kuti ofesi ya nthambi isalandire mafoni ambirimbiri. Ngati mudzapite kumsonkhano wosiyana ndi umene mpingo wanu udzapite, konzani nokha mmene mudzayendere.
5. Kodi tiyenera kukhala ndi cholinga chotani pokonzekera msonkhano wachigawo wa 2009?
5 Ntchito Zimene Zimalemekeza Mulungu: Tikamasonyeza chipatso cha mzimu pa zochita zathu zonse, kulankhula bwino komanso kusonyeza khalidwe labwino pochita zinthu ndi ena pamalo a msonkhano, tidzathandiza anthu kuona kuti anthu a Yehova ndi akhalidwe labwino ndipo sitidzakhumudwitsa ena. (1 Akor. 10:31; 2 Akor. 6:3, 4) Yesetsani kulemekeza Mulungu mwa kupezeka pamsonkhano wachigawo wa 2009, komanso posonyeza khalidwe labwino.—1 Pet. 2:12.
[Bokosi patsamba 5]
Nthawi za Msonkhano:
Tsiku Loyamba ndi Lachiwiri
8:20 m’mawa - 3:55 masana
Tsiku Lachitatu
8:20 m’mawa - 3:00 masana