Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/01 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 8/01 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu August: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabulosha amasamba 32 aŵa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo N’chiyani? Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndiponso “Taonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” Mabulosha a Buku la Anthu Onse, ndiponso Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi iyo Ilikodi? mungawagaŵire pamene kuli koyenera kutero. September: Buku lililonse la masamba 192 limene mpingo uli nalo. October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Paulendo wobwereza mukapeza anthu achidwi, aikeni pandandanda ya anthu amene mumakawapatsa magazini. November: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.

◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wamusankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa September 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detili. Mukatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo pambuyo pa lipoti lotsatira la maakaunti.

◼ Mipingo iyambe kufunsira Makalendala a Mboni za Yehova a 2002 pofunsira mabuku a September. Makalendala adzapezeka m’Chicheŵa, m’Chingelezi ndi m’Chitumbuka.

◼ Mafomu okwanira kugwiritsa ntchito m’chaka cha utumiki cha 2002 awatumiza ku mipingo yonse. Chonde gwiritsani ntchito mafomuŵa moyenera. Agwiritsireni ntchito pachifukwa chimene anapangidwira basi.

◼ Kuŵerengera mabuku ndi magazini onse amene ali m’sitoko kumene kumachitika pachaka kuchitike pa August 31, 2001 kapena pafupi ndi detilo ngati n’kotheka. Kuŵerengera kumeneku n’kofanana ndi kuŵerengera mabuku kumene mtumiki wa mabuku amachita mwezi uliwonse, ndipo ziŵerengero zonse zilembedwe pafomu Yoŵerengera Mabuku (S-18). Chiŵerengero chonse cha magazini amene alipo mungachipeze kwa mtumiki wa magazini. Mpingo uliwonse udzalandira mafomu atatu a Kuŵerengera Mabuku (S-18). Chonde tumizani pepala loyamba ku Sosaite pasanafike pa September 6.  Sungani pepala lachiŵiri m’faelo yanu. Pepala lachitatulo mungaligwiritse ntchito ngati poŵonkhetsera. Mlembi ndiye amene adzayang’anire kuŵerengeraku. Mlembi ndi woyang’anira wotsogolera asaine fomuyi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena