Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase
Kubwereramo kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa May 7 kufikira August 20, 2001. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso n’ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Zonama m’ndemanga zotsatirazi:
1. Pemphero lotchulidwa pa Nehemiya 2:4 linaperekedwa mothedwa nzeru, ladzidzidzi. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 2/15 tsa. 30 ndime 8.]
2. Mawu akuti “mpingo” amamasulidwa kuchokera ku mawu achigiriki akuti ek·kle·siʹa, amene amapereka lingaliro la umodzi ndi kuchirikizana. [w99-CN 5/15 tsa. 25 ndime 4]
3. Ngakhale kuti atumiki a Yehova amapeŵa miyambo yokhudza akufa yomwe imatsutsana ndi Mawu a Mulungu, iwo satsutsa miyambo yonse yokhudza akufa. (Yoh. 19:40) [rs-CN tsa. 155 ndime 4]
4. M’nyengo imene Yobu anakhala ndi moyo, iye anali munthu yekhayo wokhulupirika kwa Yehova. (Yobu 1:8) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 8/1 tsa. 31 ndime 3-4.]
5. Mfundo yakuti Saulo, kapena kuti Paulo, ankadzipezera yekha chithandizo mwa kusoka mahema imasonyeza kuti iye ankachokera ku banja lotsika. (Mac. 18:2, 3) [w99-CN 5/15 tsa. 30 ndime 2–tsa. 31 ndime 1]
6. Ngakhale kuti Davide anachita machimo akuluakulu, Yehova ananena kuti ‘ananditsata ndi mtima wake wonse’ chifukwa cha mtima wolapa ndiponso makhalidwe abwino. (1 Maf. 14:8) [w99-CN 6/15 tsa. 11 ndime 4]
7. Kusiyapo ngati chinthu chomwe talonjeza sichokhudzana ndi malemba, tiyenera kuyesetsa kukwaniritsa malonjezo athu ngakhale pamene taona kuti kuchita zimene tinalonjezazo n’kovuta kwambiri. (Sal. 15:4) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89- CN 9/15 tsa. 28 ndime 6.]
8. Salmo 22:1 limasonyeza kuti Davide atapanikizika maganizo anataya chikhulupiriro kwakanthaŵi. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 7/1 tsa. 8 ndime 19.]
9. Mkristu ‘angagwe’ chifukwa chokhumudwa, kugwiritsidwa mwala, kapenanso zothetsa nzeru zokhudza malamulo kapena ndalama, koma mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu ndiponso olambira anzake achikondi, iye ‘sadzatayikiratu’ mwauzimu. (Sal. 37:23, 24) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 11/1 tsa. 29 ndime 14.]
10. Genesis chaputala 1 chimaphunzitsa kuti Mulungu analenga zonse za padziko lapansi pano m’masiku asanu ndi limodzi a maora 24 lililonse. [rs-CN tsa. 104 ndime 1]
Yankhani mafunso otsatiraŵa:
11. Kodi ndi motani mmene Ezara ndi om’thandiza ake ‘anatanthauzirira’ Chilamulo? (Neh. 8:8) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 2/15 tsa. 31 ndime 5.]
12. Kodi “chimwemwe cha Yehova” chimapezeka bwanji? (Neh. 8:10) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 2/15 tsa. 31 ndime 10.]
13. N’chifukwa chiyani anthu ‘odzinenera mwaufulu kuti adzakhala m’Yerusalemu’ anadalitsidwa? (Neh. 11:2) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 2/15 tsa. 31 ndime 13.]
14. Kodi n’chifukwa chiyani Estere anachedwa kuuza mfumu cholinga chake chenicheni? (Estere 5:6-8) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 3/1 tsa. 27 ndime 18.]
15. Kodi ndi chitsimikizo chabwino chotani chomwe Salmo 27:10 limatipatsa? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 3/15 tsa. 22 ndime. 17.]
16. N’chifukwa chiyani uphungu wa Elifazi unafoola Yobu ndi kulephera kum’limbikitsa? (Yobu 21:34; 22:2, 3) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 2/15 tsa. 27 ndime 5-6.]
17. Kodi Salmo 10:13 amavumbula lingaliro lolakwika liti lomwe ochimwa osalapa amakhala nalo? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 11/1 tsa. 6.]
18. Kodi ndi zinthu “zopanda pake” ziti zimene amitundu ‘akupokosera’ malinga ndi kufotokoza kwa Salmo 2:1? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 7/1 tsa 8 ndime 5.]
19. Kodi ndi phunziro lotani laphindu lonena za kupanda tsankho lomwe tingapeze pa utumiki wa Filipo wokhudza Asamariya ndi mdindo wa ku Aitiopiya? (Mac. 8:6-13, 26-39) [w99-CN 7/15 tsa. 25 ndime 2]
20. Kodi Yobu anasonyeza motani chidaliro chake choti Mulungu angamuukitse kuchokera kumanda, komwe anakuona ngati kobisalirako mavuto? (Yobu 14:7, 13-15) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w00-CN 5/15 tsa. 27 ndime 7 tsa. 28 ndime 1.]
Pezani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
21. Estere 8:17 amati anthu “anasanduka Ayuda”; chimodzimodzinso lerolino, “ ․․․․․․․” la “nkhosa zina” likuyendera limodzi ndi ․․․․․․․ . (Chiv. 7:9; Yoh. 10:16; Zek. 8:23) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 3/1 tsa. 28 ndime 14.]
22. Monga momwe Machitidwe 1:7 amasonyezera, ngakhale kuti Yehova amasunga ․․․․․․․ kwambiri, tsiku lake loŵerengera mlandu lidzadza ngati ․․․․․․․ , pamene anthu sakuliyembekezera. (2 Pet. 3:10) [w99-CN 6/1 tsa. 5 ndime 2-3]
23. Pa 2 Petro 3:7, 10, mawu oti “miyamba” ndi “dziko” agwiritsidwa ntchito ․․․․․․․; malinga ndi mmene nkhaniyi imasonyezera, “dziko” limatanthauza ․․․․․․․ . [rs-CN tsa. 133 ndime 2-4]
24. Kulankhulana kwabwino kumatheka ngati pali kudalirana, kukhulupirirana ndiponso kumvetsetsana, ndipo mikhalidwe imeneyi imakhalapo ngati ukwati uonedwa kukhala mgwirizano wa ․․․․․․․ komanso ․․․․․․․ ndi mtima wonse kuti zimenezi zitheke. [w99-CN 7/15 tsa. 21 ndime 3]
25. Chisonkhezero chabwino cha mabwenzi chingatithandize ․․․․․․․ miyezo ya makhalidwe abwino ndi yauzimu ndipo mwakutero kudzatithandiza kutumikira Yehova ndi ․․․․․․․ . [w99-CN 8/1 tsa. 24 ndime 3]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. ‘Kukhala m’bwalo la mfumu’ kwa Moredekai kumasonyeza kuti iye anali (msilikali wa mfumu; mmodzi wa nduna za Mfumu Ahaswero; anali kuyembekezera kulankhulana ndi mfumu). (Estere 2:19, 20) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 3/1 tsa. 27 ndime 9.]
27. Malinga ndi zomwe Yobu 19:25-27 amanena, Yobu anasonyeza chikhulupiriro chake kuti ‘akapenya Mulungu’ mlingaliro lakuti (adzadalitsidwa ndi masomphenya; adzaukitsidwira ku moyo wakumwamba; maso ake akuzindikira adzatsegulidwa pa choonadi chonena za Yehova). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w94-CN 11/15 tsa. 19 ndime 17.]
28. Mboni za Yehova zilibe chifukwa chokhudza chipembedzo chokanira kugwiritsa ntchito (mwazi; zochulukitsira mwazi zopanda magazi; madzi a m’magazi) [rs-CN tsa. 316 ndime 1]
29. Maziko omwe agwetsedwa, monga momwe kwalembedwera pa Masalmo 11:3, akunena za (maziko a kachisi ku Yerusalemu; Yesu Kristu monga Mwala Wapangodya; maziko amene mgwirizano wa anthu umadalira, monga chilungamo, malamulo, ndiponso malangizo). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 7/1 tsa. 8.]
30. Yobu anaona Mulungu, monga kwalembedwera pa Yobu 42:5 mwanjira yakuti iye (anaona masomphenya a Mulungu ali m’chimphepo; anaona mngelo amene anamuonekera; anafika podziŵa Yehova mokwanira) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 8/15 tsa.12 ndime 11.]
Gwirizanitsani malemba otsatiraŵa ndi ndemanga zomwe zili m’munsizi:
Neh. 3:5; Sal. 12:2; 19:7; 2 Tim. 3:16, 17; Yak. 5:14-16
31. Tiyenera kukhala ofunitsitsa kudzipereka osati kupeŵa monyada, n’kumaona ntchito ya kalavulagaga kukhala yosatiyenera. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86 -CN 2/15 tsa. 30 ndime 12, 19.]
32. Mkristu amene wachita cholakwa chachikulu ayenera kuulula tchimo lake kwa akulu. [rs-CN tsa. 221 ndime 7]
33. Ngakhale kuti Mulungu ankagwiritsa ntchito maloto kuchenjezera anthu, kuperekera malangizo, ndi ulosi kwa anthu ake m’nthaŵi zakale, iye tsopano akutipulumutsa kudzera m’Mawu ake ouziridwa omwe analembedwa. [rs-CN tsa. 247 ndime 6]
34. Ngati tifuna kukhala paubwenzi ndi Mulungu, tiyenera kukhala oona mtima kotheratu, opanda chinyengo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 9/15 tsa. 27 ndime 1.]
35. Kumvera malamulo a Mulungu kumatsitsimula moyo ndipo kumalimbikitsa kuti munthu akhale wabwino. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani see w00-CN 10/1 tsa. 13 ndime. 4.]